Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tsogolo Lodalirika

Tsogolo Lodalirika

Tsogolo Lodalirika

Tiyerekezere kuti mwafika pa mphambano ya msewu. Msewu uliwonse uli ndi chikwangwani. Cha msewu wina chikuti, “Ikani tsogolo lanu m’manja mwa anthu ndipo khulupirirani malonjezo awo,” koma cha winawo chikuti, “Khulupirirani Mulungu ndi Ufumu wake.” Kodi mungalowere msewu uti?

CHINTHU chanzeru ndicho kukhulupirira Mulungu. Iye amati: “Wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.” (Miyambo 1:33) Timamvera Mlengi wathu potsatira zimene amatiphunzitsa m’Baibulo chifukwa timadziwa kuti mfundo zake n’zodalirika. (2 Timoteyo 3:16) Kodi pali zifukwa zomveka zodalirira mfundo zimenezi? Ndithudi zilipo. Mwachitsanzo, mu nkhani yachiwiri ija, taona kuti Baibulo lokha ndi limene limafotokoza bwino chifukwa chake anthu amalephera kudzilamulira bwinobwino. Kodi simukuvomereza kuti zimene Baibulo limanenazi n’zogwirizana ndi zimene timaonadi?

Kulondola kwa Baibulo kumaonekanso pankhani ya maulosi. Mwachitsanzo, Baibulo linalosera zoopsa zimene zidzachitike “m’masiku otsiriza.” Panopo tikutha kuona zimenezi zikuchitika. (Mateyo 24:3-7; 2 Timoteyo 3:1-5) Baibulo linaloseranso kuti anthu adzawononga dziko lapansi. Lemba la Chivumbulutso 11:18 limanena kuti Mulungu ‘adzawononga iwo owononga dziko lapansi.’

Mawu amenewa analembedwa zaka 2,000 zapitazo. Panthawiyo, panalibe munthu amene ankaganiza zoti anthu angawononge kwambiri zinthu monga mpweya, nyanja, nthaka, kuchititsa kuti dziko lizitentha kwambiri, ndiponso kuwonongeratu mitundu yosiyanasiyana ya zachilengedwe. Koma izitu n’zimene zikuchitika. Inde Mulungu sanama. Nthawi zonse Mawu ake amakwaniritsidwa ndendende. * (Tito 1:2; Aheberi 6:18) Ndipotu, Mulungu amalumbira pa dzina lake potsimikizira kuti malonjezo ake adzakwaniritsidwa.

Dzina Lodalirika

Dzina la Mulungu lakuti Yehova limatsimikizira kuti malonjezo ake onse a m’Baibulo adzakwaniritsidwa. Lili ngati siginecha yomwe imachititsa kuti cheke chikhale chovomerezeka. * Munthu wina amene analemba nawo Baibulo, yemwe nthawi zambiri ankaona kuti Mulungu akumusamalira, anati: “Takhulupirira dzina lake loyera.”—Salmo 33:21; 34:4, 6.

Lemba la Miyambo 18:10 limagwirizanitsa dzina la Mulungu ndi chisamaliro chake. Lembali limati: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; Wolungama athamangiramo napulumuka.” Komanso lemba la Aroma 10:13 limati: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” Komabe, dzina la Mulungu silili ngati chithumwa chotiteteza ku zinthu zoipa ayi. Mulungu weniweniyo ndi amene amatipulumutsa. Ndipo monga lembali likunenera, anthu amene amaitanira pa dzina lake, amatero chifukwa chomukhulupirira ndi mtima wonse. Iwo amadziwa kuti sanganame ngakhale pang’ono. Lemba la Salmo 91:14 limati: “Popeza andikondadi ndidzam’pulumutsa; ndidzam’kweza m’mwamba, popeza adziwa dzina langa.”

Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimakhulupirira ndani, Mulungu kapena anthu?’ Mboni za Yehova zimakhulupirira Mulungu ndi Ufumu wake, osati chifukwa chongotengeka maganizo, koma chifukwa chokhulupirira zinthu zenizeni zolembedwa m’Baibulo. (Aheberi 11:1; 1 Yohane 4:1) Chifukwa cha zimenezi, saopa za m’tsogolo koma ‘amakondwera ndi chiyembekezo’ chimene ali nacho. Ndipo akufuna kuti nanunso mukhale ndi chiyembekezo chabwino chimenechi.—Aroma 12:12.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani magazini yapadera ya Galamukani!, ya November 2007, yomwe inafotokoza nkhani yakuti “Kodi Mungakhulupirire Baibulo?”

^ ndime 7 Onani bokosi lakuti “Dzina Lake Ndi Umboni Wakuti N’zosakayikitsa.”

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Dzina la Mulungu limatsimikizira kuti malonjezo ake onse a m’Baibulo adzakwaniritsidwa, mofanana ndi siginecha yomwe imachititsa kuti cheke chikhale chovomerezeka

[Bokosi patsamba 9]

DZINA LAKE NDI UMBONI WAKUTI N’ZOSAKAYIKITSA

Dzina lakuti Yehova si dzina wamba ayi. * N’chifukwa chiyani tikutero? Dzinali limatanthauza kuti “Amachititsa Kukhala.” Mwachidule, tinganene kuti Mulungu ali ndi chikondi, mphamvu ndiponso nzeru zoti akhoza kukhala chilichonse chimene wafuna kuti akwaniritse cholinga chake ndiponso mawu ake. Mwachitsanzo, angakhale Mpulumutsi wa olungama, Wowononga oipa, Wakumva pemphero kapena Atate wachikondi. Zimene zikutanthauza kuti angakhale chilichonse chimene akufuna.

Yehova anati: “Ine ndine Mulungu, . . . ndilalikira za chimariziro kuyambira pachiyambi . . . ndi kunena, uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse.” (Yesaya 46:9, 10) Timatsimikizira kuti Mawu a Mulungu adzakwaniritsidwa chifukwa nthawi zonse Mulungu amachita zimene wanena ndipo izi zimakhudza dzina lake, kapena kuti mbiri yake. “Mulungu sindiye munthu, kuti aname.”—Numeri 23:19.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Dzina lakuti Yehova n’losiyana ndi maina omulemekezera akuti Wamphamvuyonse, Mlengi, Mulungu ndiponso Ambuye. M’malemba oyambirira a Baibulo Lopatulika, dzinali limapezekamo pafupifupi maulendo 7,000. Mulungu anadzipatsa yekha dzina limeneli. Lemba la Eksodo 3:15 limati: “Yehova . . . ndi dzina langa nthawi yosatha.”