Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ “Pali umboni wankhaninkhani wa sayansi wotsimikizira kuti zamoyo zinachita kusanduka. Tonse timachita kuona tokha mfundo imeneyi ndipo imatithandiza kudziwa zambiri zokhudza moyo.”—PAPA BENEDIKITO WA CHI 16.
▪ “Akuluakulu aboma anavutika . . . kupeza ndalama zounikira ndi kukonzera milatho 74,000 ‘yowonongeka’ ku United States. Anachita zimenezi mlatho wina wa ku Minneapolis [Minnesota], womwe wakhala zaka 40, utaphwasuka mwadzidzidzi n’kugwera mumtsinje wa Mississippi. Mlathowo unapitira limodzi ndi magalimoto ambirimbiri amene anali kudutsa panthawiyo, moti mpaka [anthu 13] anafa.”—THE WEEK, U.S.A.
Anthu Ambiri Akuphwanya Malamulo
Nyuzipepala ina ya ku London inati: “Zakuti anthu amamvera malamulo ndi nkhambakamwa chabe. Anthu ambiri a ku Britain amanena kuti amangotsatira malamulo amene akufuna komanso panthawi imene akufuna basi.” Kafukufuku amene anachitika pa King’s College wokhudza maphunziro a za chilungamo komanso milandu, wasonyeza kuti anthu olemekezeka ndi amenenso amaphwanya malamulo. Munthu mmodzi pa anthu atatu alionse amene anafunsidwa anati amapereka ziphuphu kuti azembe msonkho. Komanso munthu mmodzi pa anthu atatu alionse akapatsidwa chenje chambiri sabweza, ndipo munthu mmodzi pa anthu asanu alionse amaba zinthu kuntchito. Ochita kafukufukuwo ananena kuti, “makhalidwe a anthu alowa pansi kwambiri. Ndipo zimenezi ndi zofala kuposa ziwawa zosiyanasiyana, monga ziwawa za mumsewu.”—The Times.
Kodi N’zoona Kuti Zida za Nyukiliya Zili “M’manja mwa Mulungu”?
Tchalitchi cha Orthodox ku Russia chinadalitsa ntchito imene anthu osunga ndi kukonza zida za nyukiliya ku Russia anagwira. Nyuzipepala ina inafalitsa uthenga umene unawerengedwa m’tchalitchi chachikulu cha Katolika chotchedwa Christ the Savior ku Moscow. Mu uthengawo, mkulu wa tchalitchicho, Alexis Wachiwiri anati: “Ndimapemphera kwa Mulungu kawirikawiri . . . kuti zida zanu zankhondo zimene munakonza zikhalebe m’manja mwa Mulungu ndipo zikuthandizeni poopseza ndi kubwezera adani anu.”—Krasnaya Zvezda.
Ku Isiraeli Kunalidi Uchi
Lipoti lochokera ku yunivesite ina linati: “Akatswiri a mbiri yakale apeza umboni wotsimikizira zimene Baibulo limanena zakuti dziko la Isiraeli linali . . . ‘dziko la mkaka ndi uchi’ (makamaka kuti linali dziko la uchi).” Ku Tel Rehov m’chigwa cha Beth Shean ku Israel anapezako ming’oma itatu yosanja. Lipotilo linati zikuoneka kuti njuchi zinkakhala m’ming’omayi “cha m’ma 900 kapena 800 B.C.E., ndipo n’kutheka kuti ming’omayi inalipo 100.” Odziwa za ulimi wa njuchi amanena kuti n’kutheka kuti chaka chilichonse “ankapeza uchi wokwana pafupifupi makilogalamu 500.”—Hebrew University of Jerusalem Institute of Archaeology.
Amakonda Ziweto Kuposa Anthu
Anthu ena atafufuza pa Intaneti anapeza kuti “munthu mmodzi pa anthu anayi alionse a ku Australia amakonda kwambiri galu, mphaka, kapena chiweto chawo china. Ndipo nthawi zambiri amakonda ziwetozi kuposa mkazi kapena mwamuna wawo ngakhalenso makolo awo amene. Munthu mmodzi pa anthu atatu alionse amene anafunsidwa ndi ofufuza a pakampani ina ya zachuma ku Australia, anati amawononga “nthawi ndiponso ndalama zambiri posamalira chiweto chawo kuposa zimene amawononga kuchipatala pa matenda awo.” Masiku ano ziweto zimalandira chithandizo chosiyanasiyana chapamwamba kwambiri. Amatha kuzichita opaleshoni yapamwamba, kuzipatsa chithandizo chapamwamba cha matenda a khansa, kuziika ziwalo zosiyanasiyana, ngakhalenso kuzichita opaleshoni ya ubongo.—The Sydney Morning Herald.