Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Magazi Akayezedwa Ndiye Kuti Alibedi Kachilombo ka HIV?

Kodi Magazi Akayezedwa Ndiye Kuti Alibedi Kachilombo ka HIV?

Kodi Magazi Akayezedwa Ndiye Kuti Alibedi Kachilombo ka HIV?

YOLEMBEDWA KU NIGERIA

▪ ANTHU anafunsa funso limeneli chifukwa mwana wina amene analandira magazi oyezedwa bwinobwino pachipatala chodziwika ku Nigeria anapezeka ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi.

Malinga ndi zimene ananena mkulu wa pachipatalacho, mwana wina dzina lake Eniola anabadwa ndi matenda achikasu. Dokotala anaona kuti ndi bwino kum’chotsa magazi ake n’kumupatsa ena ndipo bambo ake ndiwo anapereka magazi enawo. Koma kunapezeka kuti magazi a bamboyo sanali ogwirizana ndi a mwanayo. Choncho, anaganiza zomupatsa magazi a kuchipatala konko. Posapita nthawi mwanayo anapezeka kuti ali ndi kachilombo ka HIV ngakhale kuti makolo ake analibe kachilomboko. Achipatalawo ananena kuti, “panthawi imene ankapereka magaziwo anawaunika n’kupeza kuti analibe kachilombo.”

Ndiyeno, zinatheka bwanji kuti mwanayo apezeke ndi kachilomboko? Boma la Nigeria litafufuza nkhaniyi linapeza kuti magazi anapatsidwawo anali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi. Nyuzi ina ya ku Nigeria inagwira mawu a dokotala wina, yemwe anati: “Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti panthawi imene ankayeza magaziwo, tizilomboto tinali tisanayambe kuonekera.”—Nigerian Tribune.

Zimene zinachitikazi ndi umboni wakuti kuika anthu magazi n’koopsa. Pofotokoza mmene zimakhalira kuti tizilombo tisaonekere m’magazi, bungwe lina loona za matenda linati: “Zimatenga nthawi kuti mphamvu yoteteza thupi ku matenda iyambe kuonetsa zizindikiro zomwe zimathandiza madokotala kuona kuti magazi ali ndi tizilomboti. Kutalika kwa nthawi imeneyi n’kosiyanasiyana malinga ndi thupi la munthu. Anthu ena zimangowatengera milungu iwiri kapena 8 basi (koma ambiri zimawatengera pafupifupi masiku 25). Ngakhale zili choncho, anthu ena zimawatengera nthawi ndithu. . . . Moti alipo ena amene amafika mpaka miyezi 6.”—U.S. Centers for Disease Control and Prevention.

Choncho sikuti akayeza magazi n’kupeza kuti alibe kachilombo ka HIV ndiye kuti basi alibedi. Bungwe lina loona za matenda a Edzi linachenjeza kuti: “Ngakhale panthawi imene sikakuonekera m’magazi, kachilombo ka HIV kangathebe kufalikira kwa munthu wina. Ndipotu panthawiyi m’pamene zimakhala zosavuta kuti munthu wa kachilomboka akafalitse.”—The San Francisco AIDS Foundation.

Kwa nthawi yaitali, a Mboni za Yehova akhala akutsatira malangizo a m’Baibulo onena za “kupewa . . . magazi.” (Machitidwe 15:29) Malangizo amenewa awateteza kwambiri, kusonyeza kuti kutsatira malangizo a Mulungu n’chinthu chanzeru. Kuti mudziwe njira zina zothandiza munthu popanda kumuika magazi, onani kabuku kakuti Kodi Mwazi Ungapulumutse Motani Moyo Wanu? *

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Kamafalitsidwa ndi Mboni za Yehova.