Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kodi Mwana Wangayu Watani?”

“Kodi Mwana Wangayu Watani?”

“Kodi Mwana Wangayu Watani?”

Mwana wawo wamkazi wa zaka 15 atalowa m’nyumba, Scott ndi Sandra * anadabwa kwambiri kuona tsitsi lake lili psuu kufiira. Atamufunsa za tsitsilo anakhumudwa kwambiri ndi mayankho ake.

“Kodi ife tinakuuza kuti ukasinthe mtundu wa tsitsi lako?”

“Ayi, koma nanga munandiuza kuti ndisalisinthe?”

“Nanga bwanji sunatifunse?”

“Chifukwa ndimadziwa kuti simungalole.”

ZIMENE Scott ndi Sandra anakumana nazo, zikusonyeza kuti nthawi imene wachinyamata akukula imakhala yovuta kwa wachinyamatayo komanso makolo ake. Makolo ambiri sakonzekera kusintha kumene kumachitika mwana wawo akamasinkhuka. Mayi wina wa ku Canada dzina lake Barbara anati: “Mwana wathu anangosintha mwadzidzidzi. Ndinadabwa kuti, ‘kodi mwana wangayu watani?’ Zinangokhala ngati kuti anthu ena anam’tenga tili mtulo n’kutiikirapo mwana wina.”

Zimene zinachitikira Barbara si zachilendo. Taonani zimene makolo ambiri a m’mayiko osiyanasiyana anauza olemba Galamukani!

“Mwana wanga atayamba kusinkhuka ankangomva zake zokha ndipo anayamba kutiderera.”—Anatero Lia, wa ku Britain.

“Ana athu aakazi anayamba kuganizira kwambiri za maonekedwe awo.”—Anatero John, wa ku Ghana.

“Mwana wanga wamwamuna ankafuna kuchita zinthu payekha ndipo sankafuna kumuuza zochita.”—Anatero Celine, wa ku Brazil.

“Mwana wathu wamkazi sankafunanso kuti tizimukumbatira kapena kumupsompsona.”—Anatero Andrew, wa ku Canada

“Ana athu aamuna anayamba kulusa kwambiri. M’malo momvera zimene tikuwauza, iwo ankatsutsa motiderera.”—Anatero Steve, wa ku Australia.

“Mwana wanga wamkazi ankangokhala phee. Ndipo ndikafuna kucheza naye ankangoona ngati ndikumusokoneza.”—Anatero Joanne, wa ku Mexico.

“Ana athu ankatibisira zimene akuchita kapena zimene akuganiza. Ndipo nthawi zambiri ankakonda kukhala ndi anzawo m’malo mocheza nafe.”—Anatero Daniel, wa ku Philippines.

Ngati mwana wanu akusinkhuka mwina mwakumanapo ndi zimene tafotokoza pamwambazi. Ngati ndi choncho dziwani kuti Baibulo lingakuthandizeni kumumvetsa mwana wanuyo. Kodi lingakuthandizeni bwanji?

M’pofunika Nzeru Ndiponso Luntha

Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Tenga nzeru, tenga luntha.” (Miyambo 4:5) Makhalidwe amenewa ndi ofunika kwambiri mwana wanu akamasinkhuka. Luntha limakuthandizani kuti muzitha kuona moyenera khalidwe la wachinyamatayo komanso zimene zikuchititsa khalidwelo. Ndipo nzeru zimakuthandizani kuchita zinthu zimene zingathandize wachinyamatayo kuti akule bwino n’kudzakhala munthu wodalirika.

Musakhumudwe mukamaona ngati kuti simukugwirizana ndi mwana wanu monga munkachitira kale. Dziwani kuti makolo amafunika kuthandiza ana awo panthawi yovutayi ndipo zimenezi n’zimene achinyamatawo amafuna. Kodi nzeru ndi luntha zingakuthandizeni bwanji kuchita zimenezi?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Mayina m’nkhani ino tawasintha.