Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndi Bwino Kumenyana ndi Wachiwembu?

Kodi Ndi Bwino Kumenyana ndi Wachiwembu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Ndi Bwino Kumenyana ndi Wachiwembu?

PAKATI pausiku mukumva phokoso limene likudzidzimutsani. Kenaka mukumva mgugu wosonyeza kuti m’nyumba mwanu mwalowa chigawenga. Mtima wanu ukuyamba kugunda kwambiri ndipo simukudziwa chochita.

Zimenezi zingathe kuchitikira wina aliyense. Masiku ano zoopsa ngati zimenezi zikuchitika m’mayiko ndiponso m’mizinda yosiyanasiyana. N’chifukwa chake anthu ambiri ayamba kugula zida kapena kuphunzira masewera omenyana pofuna kuti azitha kudziteteza. Maboma ena amakhazikitsa malamulo oti nzika zawo zizitha kudziteteza ngakhale popha wachiwembuyo. Koma kodi Baibulo limati chiyani pankhaniyi? Kodi nthawi zina ndi bwino kuti munthu adziteteze kapena kuteteza banja lake pomenyana ndi wachiwembu?

Mulungu Amadana ndi Chiwawa

Baibulo limaletsa zachiwawa ndipo limadzudzula anthu amene amachita zimenezi. Wamasalmo Davide ananena za Yehova kuti: “Moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” (Salmo 11:5) Mulungu anadzudzula mitundu ingapo ya anthu kuphatikizapo mtundu wake, chifukwa choti ankachita zachiwawa ndi kupha anthu. (Yoweli 3:19; Mika 6:12; Nahumu 3:1) M’Chilamulo chimene Mulungu anapatsa Aisiraeli, ngakhale kupha munthu mwa ngozi yoti akanatha kuipewa unali mlandu waukulu kwambiri.—Deuteronomo 22:8.

Baibulo limalimbikitsa anthu kuti azipewa mikangano poyesetsa kuchita zinthu zolimbikitsa mtendere tsiku lililonse. Nthawi zambiri chiwawa chimayamba chifukwa cholankhulana mawu okhadzula. Baibulo limati: “Posowa nkhuni moto ungozima; ndi popanda kazitape makangano angoleka.” (Miyambo 26:20) Nthawi zambiri kuchita zinthu modekha kumathandiza kuti munthu azizire mtima n’kupewa kuchita zinthu zachiwawa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”—Aroma 12:18.

Mukakumana ndi Achiwembu

Sikuti tingapeweretu kukumana ndi anthu achiwawa ngakhale kuti nthawi zonse timayesetsa kukhala mwa mtendere. Kuyambira kalekale, anthu olambira Mulungu mokhulupirika akhala akuvutitsidwa kapena kuphedwa ndi achiwembu. (Genesis 4:8; Yobu 1:14, 15, 17) Kodi tiyenera kutani tikakumana ndi wachiwembu wokhala ndi chida? Yesu anati: “Usalimbane ndi munthu woipa.” (Mateyo 5:39) Iye anatinso: “Iye amene wakulanda malaya ako akunja, usamuletse kutenga malaya ako a mkati.” (Luka 6:29) Yesu sanali kulimbikitsa anthu kuti aziteteza katundu wawo kwa achiwembu. Munthu wanzeru sangalimbelimbe pofuna kuti asalandidwe katundu wake ndi chigawenga chomwe chili ndi chida. Kunena zoona, moyo ndi wofunika kwambiri kuposa katundu wina aliyense.

Komano munthu angatani ngati wachiwembuyo akufuna kumupha? Lamulo limene Mulungu anapereka kwa Aisiraeli limatithandiza kudziwa zimene tingachite. Wakuba akagwidwa masana n’kuphedwa, munthu amene wamuphayo ankaimbidwa mlandu wakupha munthu. Zikuoneka kuti ankatero chifukwa choti chilango cha mlandu wakuba sichinali kuphedwa ayi. Komanso poti anali masana, wakubayo akanatha kumuona bwinobwino n’kumuweruza. Koma wakuba akaphedwa usiku, mwininyumbayo sankaimbidwa mlandu chifukwa choti zinali zovuta kuona zimene wakubayo amachita n’kudziwa zolinga zake. Motero mwininyumbayo amaonedwa kuti sanalakwe podziteteza kuti banja lake lisavulazidwe.—Eksodo 22:2, 3.

Choncho Baibulo limasonyeza kuti munthu angathe kudziteteza kapena kuteteza banja lake kuti lisavulazidwe ndi achiwembu. Angathe kupherera, kum’gwira wachiwembuyo, ngakhalenso kum’menya mwamphamvu kuti afooke n’kugonja. Cholinga chake n’chongoletsa munthuyo kuchita zachiwawazo basi. Motero, ngati wachiwembuyo atavulazidwa kwambiri mpaka kufa zingaoneke kuti waphedwa mwangozi.

Njira Yabwino Yodzitetezera

N’zoonekeratu kuti nthawi zina pamakhala zifukwa zabwino zodzitetezera. Munthu aliyense ali ndi ufulu wodziteteza ndiponso woteteza banja lake kwa anthu ofuna kuwavulaza kapena kuwapha. Ngati n’zosatheka kuthawa munthu amene akufuna kutivulaza Baibulo sililetsa kudziteteza. Komabe njira yabwino kwambiri yodzitetezera ndiyo kuyesetsa kupewa zinthu zimene zingachititse kuti tikumane ndi zinthu zoterezi.—Miyambo 16:32.

Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘tiyesetse kupeza mtendere ndi kuusunga’ pa zinthu zosiyanasiyana zimene timachita m’moyo wathu. (1 Petulo 3:11) Njira imeneyi imathandiza kwambiri kuti tizikhala mwamtendere.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa zachiwawa?—Salmo 11:5.

▪ Kodi tingachite bwanji zinthu mwanzeru poteteza katundu wathu?—Miyambo 16:32; Luka 12:15.

▪ Kodi tingatani kuti tipewe zachiwawa?—Aroma 12:18.

[Mawu Otsindika patsamba 11]

Baibulo limasonyeza kuti munthu angathe kudziteteza kapena kuteteza banja lake ngati wachiwembu atafuna kuwavulaza