Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kodi Chikhristu Chili ndi Tsogolo Lotani? (February 2007) Zambiri zimene munanena m’nkhaniyi n’zogwirizana ndi Mawu a Mulungu, ndipo ndikugwirizana nazo. Komano pali mfundo ziwiri zimene sindinasangalale nazo. Yoyamba ndi yakuti munakhala ngati mwanyoza matchalitchi ena, ndipo ina ndi yakuti munaonetsa kuti inuyo mumachita bwino kuposa matchalitchi ena onse. Inde zikanakhala bwino tonse tikanakhala ndi chikhulupiriro chimodzi koma si mmene zinthu zilili. Ineyo sindiona kuti chipembedzo chinachake ndiye chabwino kuposa zina.

S. S., United States

Yankho la “Galamukani!”: Mboni za Yehova sizitsutsana ndi anthu a zipembedzo zina, ndipo siziona kuti zimachita bwino kuposa ena. Timadziwa kuti anthu “onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Choncho, timachita khama kugwiritsa ntchito chuma chathu komanso nthawi yathu kuti tifikire anthu m’nyumba zawo pofuna kukambirana nawo choonadi cha m’Baibulo ndiponso chiyembekezo chabwino chimene chili m’Baibulo. Komabe, Mboni za Yehova zimatsanzira Yesu ndi ophunzira ake amene ankatsutsa chinyengo komanso zinthu zolakwika zimene zinkachitika m’zipembedzo.

Kodi Mungayankhe Bwanji? Ndili ndi ana awiri. M’mbuyomu sitinkakonda kuwerenga chigawo chimenechi. Koma panopa ndikuona kuti ndi chigawo chabwino kwambiri chophunzitsira ana anga kuti azikonda choonadi cha Baibulo. Ndiponso mfundo zake zimandithandiza kulimbitsa chikhulupiriro changa.

I. H., Czech Republic

Ndikuthokoza kwambiri chifukwa cha chigawo chosangalatsa kwambiri chimenechi. Chimakhala ndi mitu yabwino imene ndimawerenga pa phunziro la umwini. Zikuoneka kuti pamakhala chintchito chachikulu kuti mulembe mfundo zomveka bwino chonchi. Mfundo zimenezi zimandithandiza kuyandikira kwambiri kwa Yehova, yemwe ndi atate wathu wanzeru.

A. S., Russia

“Yehova, Ndiloleni Kuti Ndikutumikireni” (July 2007) Chikhulupiriro changa mwa Yehova chinalimba kwambiri nditawerenga nkhani ya Danielle Hall. Ngakhale kuti anali wamng’ono, sankaopa kuuza aliyense kusukulu kwawo kuti ndi wa Mboni za Yehova. Ndikukhulupirira kuti ana ambiri a Mboni za Yehova adzatengera chitsanzo chake.

A. R., Madagascar

Ndili ndi zaka 9. Ine ndi mayi anga tangomaliza kumene kuwerenga nkhani ya Danielle. Nkhaniyi yandipangitsa kudziwa kuti ndili ndi mwayi chifukwa makolo anga ndi a Mboni ndipo sizovuta kuti nditumikire Yehova. Mfundo yomwe inandisangalatsa kwambiri ndi yakuti “zilibe kanthu kuti tili kuti, Yehova amakhala nafe pafupi nthawi zonse.” Komanso ndinachita chidwi kumva kuti Danielle akaweruka kusukulu ankakhala pa bedi lake n’kumapemphera kwa Yehova. Iye ankamuuza zochitika zonse za tsiku limenelo ngati mmene munthu angachitire ndi bambo ake. Ndikufuna kutengera chitsanzo chimenechi.

A. D., Italy

“Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . N’chifukwa Chiyani Ndimasowa Anthu Ocheza Nawo? (July 2007) Nkhani imeneyi ndinaikonda kwambiri chifukwa inangokhala ngati kuti alembera ineyo. Ndinasangalalanso ndi mafunso amene anafunsidwa ndiponso mipata imene inasiyidwa kuti ndilembemo mayankho. Zikomo kwambiri. Nkhaniyi yandithandiza kwambiri.

C. A., Canada