Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mitengo Yam’madzi

Mitengo Yam’madzi

Mitengo Yam’madzi

YOLEMBEDWA KU AUSTRALIA

M’mitengo imeneyi mumakhala nyama ndiponso mbalame zambiri zimene zayamba kuchepa padziko pano. Mitengoyi imathandiza kukonza madzi kuti azikhala abwino. Kum’mwera kwa boma la Florida, ku United States, nsomba zamitundu yosiyanasiyana zimadalira mitengoyi. Mitengo ya m’madziyi imathandizanso kuti madzi asasefukire n’kuwononga madera a m’mphepete mwa nyanja.

MITENGOYI imapezeka m’madera ambiri a m’mphepete mwa nyanja ndipo imamera yambiri malo amodzi n’kupanga malunje. Nthawi zambiri imamera m’mphepete mwa nyanja zikuluzikulu chifukwa choti madzi ake amakhala amchere pang’ono chabe. Ngakhale kuti zomera zambiri sizikula bwino pamalo a mchere wotere, mitengoyi imakula bwinobwino. Kodi zimenezi zimatheka bwanji? Mitengoyi ili ndi njira zake.

Imamera Malo Amchere

Mitengo ina yotereyi imatsekereza mchere kuti usalowe m’mizu yake. Imatsekerezeratu mchere wonse moti anthu a paulendo akamva ludzu amazula mitsitsi ya mitengo yotereyi n’kuifinya kuti apeze madzi akumwa. Mitundu ina ya mitengoyi sitsekereza mcherewo koma imalola kuti ulowe. Zikatero mcherewo umakasonkhana m’masamba ake okalamba kapena m’nthambi zina zotha ntchito, ndipo kenaka imayoyola masambawo kapena nthambizo.

Palinso mitundu ina imene imalola kuti mcherewo ulowe koma imautulutsa mwamsanga kudzera m’masamba ake. Masamba a mitengo yotereyi amawawa mchere kwambiri mukawanyambita. Koma m’pofunika kusamala. Utomoni wa m’masamba a mitengo ina ya mtunduwu ukalowa m’maso umatha kum’chititsa munthu khungu. Utomoniwu ulinso ndi ubwino wake chifukwa ndi mankhwala a zilonda zapakhungu ndiponso othandiza munthu akalumidwa ndi tizilombo.

Kodi Zimatheka Bwanji Kuti Izikula Bwinobwino?

Zomera zambiri zimafuna dothi lokhala ndi mpweya wokwanira. Koma nthawi zambiri dothi limene mitengoyi imamerapo limakhala lodzadza madzi. Chinsinsi cha mitengoyi n’chakuti mizu yake ina siilowa m’dothi, motero imatha kupuma mpweya wa mumlengalenga. Mizu imeneyi imamera mosiyanasiyana. Ina imamera mopindika ngati bondo.

Ina mwa mizu ya mitengoyi imatuluka m’dothi ili yoongoka ngati pensulo. Ina imamera mooneka ngati miyendo ya mtengowo. Ina imamera ngati miyendo ya nkhanu. Mizu imeneyi imathandiza kuti mtengowo uzitha kupuma bwinobwino komanso kuti usagwe.

Kodi Nkhalango za Mitengoyi Zimakula Bwanji?

Mtundu wina wa mitengoyi umakhala ndi zipatso zikuluzikulu zobulungira ndipo zipatsozo zimakhala ndi nthangala zoumbika mosiyanasiyana. Zipatsozo zikakhwima zimasweka ndipo nthangala zake zimagwera m’madzi. Zina zimatengedwa ndi madziwo mpaka kukafika malo ena amene zingathe kumerapo.

Nthangala za mitundu ina ya mitengoyi zimamera zidakali pa mtengo pomwepo ndipo ndi mitengo yochepa kwambiri imene imachita zinthu ngati zimenezi. Kenako kamtengoko kamagwa n’kumayandama kwa miyezi ingapo kapenanso chaka chimene, kakufunafuna malo oti kakhazikike.

Kayandamidwe ka timitengoti kamathandiza kuti timere tikafika pa malo opanda mchere wambiri. Timayandama chogona tikamadutsa malo amchere wambiri koma tikafika malo amene alibe mchere wambiri timayandama tili njoo. Zimenezi zimathandiza kuti tikhazikike m’matope n’kumera pomwepo.

Mumakhala Zamoyo Zosiyanasiyana

M’mitengo imeneyi mumakhala zamoyo zambiri zimene zimadalirana. Tizilombo ting’onoting’ono timadya masamba ndi nthambi zimene zayoyoka n’kuyamba kuwola. Ndiyeno tinyama tina timadya tizilomboti. Zamoyo zambiri zimagona, kudya, kuswana ndiponso kukulira m’mitengo imeneyi.

Mwachitsanzo, mbalame zamitundumitundu zimamanga zisa m’mitengoyi n’kumaswana. Nthawi zina zimapuma m’mitengo imeneyi zikakhala pa ulendo wautali. M’dziko la Belize lokha, muli nkhalango ya mitengo imeneyi mmene muli mitundu ya mbalame pafupifupi 500. Nsomba zamitundumitundu zimaswana m’malo amene muli mitengoyi ndipo zina zimangobwerako kudzafuna chakudya. Pakati pa mayiko a India ndi Bangladesh pali malo otchedwa Sundarbans omwe ali ndi malunje a mitengo imeneyi ndipo pa malowa pali mitundu pafupifupi 120 ya nsomba.

M’malunje a mitengo yotereyi mulinso zomera zina zambiri. M’madera a m’mphepete mwa nyanja, kum’mawa kwa dziko la Australia, muli ndere za mitundu 105 zomwe zimamera m’malunje amenewa. Mumapezekanso maluwa osiyanasiyana ndiponso zomera zina. Kunena zoona, padziko lonse malunje amenewa amathandiza zamoyo ndiponso zomera zosiyanasiyana. Mwachitsanzo amathandiza kuti ndere zizimera bwino komanso ndi ofunika pa moyo wa akambuku akuluakulu komanso wa anthu.

Anthu Amapindula Nayo Kwambiri

Mitengo yam’madziyi imathandizanso m’njira zina kuwonjezera pa kuteteza chilengedwe. Pali zinthu zambiri zimene timapeza kuchokera ku mitengoyi, monga nkhuni, makala, utoto, zakudya za ziweto ndiponso mankhwala. M’malunje ake mumapezekanso zakudya zosiyanasiyana monga nsomba, nkhanu komanso uchi. Chifukwa choti nkhanu zinazake zimakonda kupezeka m’malunje a mitengoyi, asodzi ena ankaganiza kuti mizu ya mitengoyo ndi imene imabala nkhanuzo.

Mitengo imeneyi imagwiritsidwa ntchito ndi makampani opanga mapepala, zovala, ofufuta zikopa ndiponso a zomangamanga. Mitengoyi imathandizanso makampani opha nsomba komanso a zokopa alendo.

Ngakhale kuti mitengoyi ndi yothandiza, chaka chilichonse anthu amagwetsa nkhalango za mitengoyi zokwana mahekitala 100,000. Anthu amagwetsa mitengoyi kuti apeze malo olima komanso omangapo nyumba ndipo amaona kuti izi n’zothandiza kwambiri. Anthu ambiri amaona kuti nkhalango zoterezi n’zachabechabe chifukwa mumakhala matope, fungo loipa komanso udzudzu.

Koma zoona zake n’zakuti nkhalango zoterezi zimathandiza kwambiri pa moyo wa anthu. Mizu yake komanso zimene imachita posefa mchere zimathandiza kwambiri zamoyo zosiyanasiyana. Mitengoyi ndi yofunika kwambiri ku makampani osiyanasiyana. Imathandizanso kuti nthaka isamakokoloke m’mphepete mwa nyanja komanso kuti madzi asamasefukire n’kumapha anthu. Motero mitengoyi tiziiona kuti ndi yofunika kwambiri.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 24]

Kufula Uchi M’mitengoyi

Nkhalango yaikulu ya mitengo imeneyi ili ku Sundarbans pa malo amene mtsinje wa Ganges umakathira m’nyanja. Derali lili pakati pa mayiko a India ndi Bangladesh. Ena mwa anthu amene amakhala m’dera limeneli ndi a Mowalis ndipo amadalira nkhalango zimenezi pamoyo wawo. Ntchito imene amagwira ndi yoika moyo pachiswe.

Iwo amafula uchi. M’miyezi ya April ndi May anthu amenewa amayendayenda m’nkhalangozi kufunafuna uchi. Njuchi zake ndi zikuluzikulu ngati abemberezi. Njuchizi ndi zolusa kwambiri ndipo akuti zimatha kupha njovu.

Chifukwa cha kuopsa kwa njuchizi, ofula uchiwo amapanga muuni pogwiritsa ntchito tinthambi touma ta mitengoyi ndipo utsi wake umabalalitsa njuchizo. Pofuna kuti njuchizo zisasamuke, anthu anzeru amasiyako zisa za njuchizo. Izi zimathandiza kuti chaka chilichonse azipeza uchi.

Kwa anthuwa, zinthu zoopsa m’nkhalango zimenezi si njuchi zokha. Mulinso ng’ona ndi njoka zaululu kwambiri. Palinso anthu achiwembu amene amawadikirira kuti awalande uchi ndi phula akamatuluka m’nkhalangozi. Izi zili apo, mulinso akambuku akuluakulu oopsa kwambiri. Chaka chilichonse akambukuwa amapha anthu 15 kapena 20 amene amapita kukafula uchi.

[Mawu a Chithunzi]

Zafer Kizilkaya/Images & Stories

[Chithunzi patsamba 23]

Mitengo yam’madziyi imakula bwino m’malo oti mitengo ina singamere

[Mawu a Chithunzi]

Top right: Zach Holmes Photography/Photographers Direct; lower right: Martin Spragg Photography (www.spraggshots.com)/Photographers Direct