Msonkhano wa Chigawo wa Mboni za Yehova
Msonkhano wa Chigawo wa Mboni za Yehova
Wakuti “Mzimu wa Mulungu Umatitsogolera”
▪ MISONKHANO yambirimbiri ya masiku atatu, yomwe inayamba ku United States Lachisanu, Loweruka ndi Lamlungu pa May 23 mpaka 25, ipitirira kuchitika m’mizinda yambirimbiri padziko lonse m’miyezi ikubwerayi. M’chaka cha 2007, anthu oposa 12 miliyoni anapita ku misonkhano 3,200 yotereyi.
Chaka chino m’madera ambiri, chigawo cha m’mawa chizidzayamba 9:20 ndi nyimbo za malimba. Mutu wa tsiku Lachisanu wachokera pa Yohane 16:13 ndipo ndi wakuti “Mzimu . . . Udzakutsogolerani M’choonadi Chonse.” Zina mwa nkhani zoyambirira zili ndi mitu yotsatirayi: “N’chifukwa Chiyani Mzimu wa Mulungu Uyenera Kutitsogolera?” ndiponso “Mzimu Woyera Unagwira Ntchito Polenga Zinthu.” Nkhani yosiyirana ya mutu wakuti “Mzimu wa Mulungu Unkatsogolera Anthu Akale Okhulupirika” idzakhala ndi mbali zakuti “M’nthawi ya Mose,” “M’masiku a Oweruza,” ndi “M’nthawi ya Atumwi.” Nkhani yaikulu ya mutu wakuti, “Ntchito ya Mzimu Woyera Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova,” ndi imene idzakhale nkhani yomaliza pa chigawo cha m’mawa.
Nkhani yoyamba pa Lachisanu masana ndi yakuti “Kuyankha Mafunso Okhudza Mzimu Woyera,” ndipo pambuyo pake padzakambidwa nkhani yakuti “Mzimu Umafufuza . . . Zinthu Zakuya za Mulungu.” Kenako padzakambidwa nkhani yakuti “Muzichita Zimene Mawu a Mulungu Amanena Osati Kungomva Chabe.” Nkhani yosiyirana yakuti “Achinyamata, Yendani mwa Mzimu wa Mulungu” idzafotokoza mmene achinyamata angachitire zimenezi “Kusukulu,” “Kuntchito,” “Kunyumba,” “Mumpingo,” “Pocheza ndi Anzawo,” komanso “Akakhala Okha.” Tsiku loyamba lidzatha ndi nkhani yochititsa chidwi yakuti “Achinyamata Tetezani Ubale Wanu ndi Yehova,” ndipo nkhani imeneyi idzathandiza achinyamata kuteteza ubale wawo ndi Yehova.
Mutu wa tsiku Loweruka udzakhala wakuti “Kufesera Mzimu” ndipo udzachokera pa Agalatiya 6:8. Nkhani ina imene idzakambidwe chigawo cha m’mawa idzakhala yosiyirana ndipo mutu wake ndi wakuti “Mzimu wa Mulungu Umatitsogolera mu Utumiki Wathu.” Nkhaniyi idzakhala ndi mbali zitatu. Chigawo cha m’mawachi chidzatha ndi nkhani ya ubatizo ndipo pambuyo pake anthu oyenerera adzabatizidwa.
Chigawo cha masana tsiku Loweruka chidzayamba ndi nkhani yakuti: “Mzimu wa Mulungu Unatsogolera Olemba Baibulo.” Kenako padzakhala nkhani yosiyirana yomwe idzakhala ndi mbali zisanu. Mutu wake ndi wakuti “Mzimu wa Mulungu Umatipatsa Mphamvu Zoti,” Tilimbane ndi Mayesero. “Tipirire Ngati Tatopa Kapena Kukhumudwa.” “Tisafooke Pozunzidwa.” “Tipewe Kutengera Zoipa Zimene Anzathu Amachita,” komanso “Tipirire Mavuto.” Nkhani yomaliza tsiku limeneli idzakhalanso yochititsa chidwi ndipo idzakhala ndi mutu wakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu.”
Pulogalamu yam’mawa ya tsiku Lamlungu idzafotokoza bwino mutu wakuti “Pitirizani Kuyenda mwa Mzimu,” womwe wachokera pa Agalatiya 5:16. Padzakhala nkhani yosiyirana yomwe idzakhale ndi mbali 9, ndipo ili ndi mutu wakuti “Yesetsani Kukhala ndi ‘Zipatso Za Mzimu’” yomwe idzafotokoze zipatso za mzimu zotchulidwa pa Agalatiya 5:22, 23. Nkhani ya anthu onse ya mutu wakuti “Dalitsidwani ndi Mfumu Yotsogoleredwa ndi Yehova” ndi imene idzakhale nkhani yomalizira chigawo cha kum’mawa. Chigawo cha madzulo chidzakhala ndi sewero lokhala ndi zovala zake zapadera la mutu wakuti “Musasiye Chikondi ‘Chimene Munali Nacho Poyamba.’” Nkhani ya m’seweroli ndi yosonyeza maganizo amene mwina analipo pakati pa Akhristu kumapeto kwa nthawi ya atumwi. Nkhani yotsiriza pa msonkhanowu idzakhala ndi mutu wakuti “Kutumikira Yehova Mogwirizana ndi Gulu Lake Lotsogoleredwa ndi Mzimu.”
Konzani zodzapezekapo. Kuti mudziwe malo oyandikana ndi kwanu, funsani ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kapena tilembereni kalata. Magazini ya Nsanja ya Olonda, ya March 1 ili ndi malo amene kudzachitikire misonkhano imeneyi ku Malawi ndi Mozambique.