Polera Ana—Luntha N’lofunika
Polera Ana—Luntha N’lofunika
Tayerekezani kuti mwapita ku dziko la chilendo ndipo simudziwa chinenero cha kumeneko. N’zosachita kufunsa kuti mungavutike kulankhula ndi anthu koma sikuti zingakhale zosatheka. Mwina mungagwiritsire ntchito buku lomasulira mawu kuti muphunzire mawu ena a chinenerocho. Apo ayi, mwina munthu wina angamatanthauzire kuti muzitha kumvana ndi anthu.
MAKOLO amene akulera achinyamata angakumane ndi zinthu zofanana ndi zimenezi. Zochita za achinyamata zili ngati chinenero chachilendo. Mungavutike kuzimvetsa, komabe sikuti ndi zosatheka kuzimvetsa. Chofunika ndi chakuti makolo aziyesetsa kumvetsa zimene zikuchitika panthawi imeneyi, yomwe imakhala yosangalatsa komanso yovuta.
Zimene Zimawachititsa Kusintha Khalidwe
Ngati wachinyamata akufuna kuti azisankha yekha zochita sikuti nthawi zonse umakhala umboni wakuti akupanduka. Kumbukirani kuti Baibulo limanena kuti panthawi Genesis 2:24) Choncho, pokonzekera udindo umene adzakhala nawo m’tsogolo, ndi bwino kuti nthawi zina achinyamata azisankha okha zochita.
ina “mwamuna adzasiya atate wake ndi amake.” (Tiyeni tione zimene zimachititsa kusintha kumene makolo amene tawatchula m’nkhani yoyamba ija anaona mwa ana awo.
Lia, wa ku Britain, anadandaula kuti: “Mwana wanga atayamba kusinkhuka ankangomva zake zokha ndipo anayamba kutiderera.”
Mofanana ndi mwana wamng’ono, wachinyamata amafuna kudziwa zifukwa zimene mukunenera mawu enaake. Komabe yankho lachidule silingakhale lokwanira kwa wachinyamata. N’chifukwa chiyani zili choncho? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pamene ndinali kamwana, ndinali . . . kuganiza ngati kamwana.” (1 Akorinto 13:11) Achinyamata akamakula, maganizo awo amasintha ndipo amafuna kuwafotokozera zinthu momveka ndithu kuti “luntha lawo la kuzindikira” likule.—Aheberi 5:14.
John, wa ku Ghana, anati: “Ana athu aakazi anayamba kuganizira kwambiri za maonekedwe awo.”
Mwana akamasinkhuka, thupi lake limasintha kwambiri. Ndipo akangoyamba kusinthaku, amayamba kuganizira kwambiri za maonekedwe ake. Atsikana amasangalala matupi awo akayamba kusintha koma nthawi zina amada nkhawa. Achinyamata ambiri amachita manyazi akayamba kutuluka ziphuphu ndipo n’chifukwa chake amatha nthawi yaitali podzikongoletsa m’malo momawerenga mabuku awo a kusukulu.
Daniel wa ku Philippines, anati: “Ana athu ankatibisira zimene akuchita kapena zimene akuganiza. Ndipo nthawi zambiri ankakonda kukhala ndi anzawo m’malo mocheza nafe.”
Kuchita zinthu mwamseri n’koopsa. (Aefeso 5:12) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti munthu asamakhale ndi nthawi yochita zinthu zina payekha. Ngakhale Yesu anaona kufunika kopeza nthawi yopita “kumalo kopanda anthu kuti akakhale payekha.” (Mateyo 14:13) Achinyamata akamakula amafunanso nthawi yochita zinthu zina paokha ndipo amafuna kuti akuluakulu aziwapatsa mpata wochita zimenezi. Mpata wabwino ungathandize achinyamata kusinkhasinkha pa nkhani zina ndipo zimenezi zingadzawathandize atakula.
Achinyamata akamakula amafunikanso kuphunzira kucheza ndi anzawo. N’zoona kuti “mayanjano oipa amawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:33) Komabe, Baibulo limanena kuti: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miyambo 17:17) Kudziwa kucheza ndi anthu oyenera n’kofunika kwambiri ndipo kumathandiza wachinyamatayo patsogolo akadzakula.
M’pofunika luntha kuti makolo athandize ana awo ngati akusintha khalidwe. Ndipo lunthalo lidzawathandiza kuti aziona moyenera kusintha kwa anawo. Kuwonjezera pa luntha, makolo afunikanso kukhala ndi nzeru zimene zimathandiza kuti azichita zinthu m’njira yoyenera. Kodi makolo angachite bwanji zimenezi?
[Mawu Otsindika patsamba 5]
Achinyamata akamakula, maganizo awo amasintha ndipo amafuna kuwafotokozera momveka bwino malamulo a m’banja mwanu