Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Polera Ana—Nzeru N’zofunika

Polera Ana—Nzeru N’zofunika

Polera Ana​—Nzeru N’zofunika

“Timayesetsa kulera bwino ana athu, koma timakonda kuwakalipira akalakwitsa zinazake. Moti nthawi zina timadzifunsa kuti, kodi tikuwathandizadi kuti akhale odzidalira, kapena tikuwachititsa kuti azidzikayikira? Zimativuta kudziwa njira yabwino yochitira zinthu mosapitirira malire.”—Anatero George ndi Lauren, a ku Australia.

ANA akamasinkhuka amavuta kulera. Kuwonjezera pa mavuto amene wachinyamata amayambitsa, makolo amakhalanso ndi nkhawa podziwa kuti mwana wawo akukula. Bambo wina wa ku Australia dzina lake Frank anati: “Ndimada nkhawa ndikangokumbukira kuti tsiku lina mwana wathu adzachoka pakhomo. Zimakhala zovuta kuvomereza kuti akuchoka m’manja mwathu.”

Lia, amene tam’tchula m’nkhani ina ija, akuvomerezanso zimenezi. Iye anati: “Zimandivuta kuona mwana wanga wamwamuna ngati munthu wamkulu. Ndimangomuonabe ngati kamwana basi. Ndikakumbukira tsiku limene anayamba sukulu ndimangoona ngati ndi dzulodzuloli.”

Ngakhale kuti ndi zovuta kuvomereza, achinyamata si ana aang’ono. Iwo amakhala akuphunzira kuchita zinthu ngati achikulire ndipo makolo ayenera kuwaphunzitsa ndiponso kuwathandiza. Ndipotu zimene ananena George ndi Lauren amene tawatchula pamwambawo, ndi zoona. Makolo angathe kuthandiza ana kukhala odzidalira kapena kuwachititsa kuti azidzikayikira. Kodi makolo angatani kuti asamachite zinthu mopitirira malire? Baibulo lili ndi malangizo othandiza. (Yesaya 48:17, 18) Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

Kukambirana Momasuka N’kofunika

Baibulo limanena kuti Akhristu afunika kukhala ‘ofulumira kumva’ koma ‘odekha polankhula.’ (Yakobe 1:19) Ngakhale kuti malangizo amenewa ndi ofunika polera mwana wa msinkhu uliwonse, kumvetsera n’kofunika kwambiri polera wachinyamata. Ndipo izi zimafuna khama.

Bambo wina wa ku Britain dzina lake Peter anati: “Ndinafunika kukulitsa luso lokambirana ndi ana anga aamuna pamene anayamba kusinkhuka. Ali aang’ono, ankangomvetsera zimene ine ndi mkazi wanga tinali kuwauza kuchita. Koma pamene akula timafunika kukambirana nawo bwino ndi kuwathandiza kugwiritsa ntchito luntha lawo posankha zochita. Mwachidule tingati timafunika kukambirana nawo mowafika pamtima.”—2 Timoteyo 3:14.

Kumvetsera n’kofunika kwambiri makamaka ngati simukumvana. (Miyambo 17:27) Danielle wa ku Britain anaona kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Iye anati: “Tsiku lina ndinamukhazika pansi mwana wanga kuti ndimulangize pofuna kuti asamachite makani ndikamamuuza zinthu. Koma iye anandiuza kuti amachita makani chifukwa choti nthawi zonse ndimamulankhula mokalipa komanso mongomulamula. Titakambirana bwino komanso kumvetserana tinathetsa nkhaniyi. Iye anafotokoza mmene ndimalankhulira komanso mmene zimam’khudzira, ndipo nane ndinamufotokozera maganizo anga.”

Danielle anaona kuti kukhala “wofulumira kumva” kunamuthandiza kumvetsa bwino nkhaniyo. Kenako anati: “Panopo ndimakhala wodekha polankhula ndi mwana wanga ndipo ndimamulankhula ndikakhala kuti sindinakwiye.” Iye anapitiriza kuti: “Tsopano timagwirizana.”

Lemba la Miyambo 18:13 limati: “Wobwezera mawu asanamvetse apusa, nadzichititsa manyazi.” Bambo wina wa ku Australia dzina lake Greg anaonanso kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Iye anati “Nthawi zambiri timayambana ndi ana athu chifukwa chakuti timafulumira kuwauza zochita m’malo momvetsera ndi kuvomereza maganizo a anawo.” Iye anapitiriza kuti: “Koma panopa taona kuti ngakhale pamene sitikugwirizana ndi maganizo awo, tisafulumire kuwauza zochita. M’malo mwake timawalola kufotokoza maganizo awo.”

Kodi Tiziwapatsa Ufulu Wochuluka Bwanji?

Makolo ambiri amayambana ndi ana awo pankhani ya ufulu umene amafunika kuwapatsa. Kodi achinyamata afunika kuwapatsa ufulu kufika pati? Bambo wina anati: “Nthawi zina ndimaona kuti mwana wanga ndi wovuta chifukwa kungom’patsa ufulu pang’ono amazolowera n’kumangochita zofuna zake.”

N’zoona kuti kupereka ufulu wopanda malire kwa ana n’koopsa. Baibulo limanena kuti “mwana wom’lekerera achititsa amake manyazi.” (Miyambo 29:15) Nthawi zonse ana, kaya akhale a msinkhu wotani, safunika kuwalekerera. Ndipo makolo amafunika kuti azilangiza anawo mwachikondi komanso mosasinthasintha mfundo zawo. (Aefeso 6:4) Ngakhale zili choncho, ana amafunikanso kuwapatsa ufulu wogwirizana ndi msinkhu wawo kuti adzathe kuchita zinthu mwanzeru m’tsogolo.

Mwachitsanzo, taganizirani mmene inuyo munaphunzirira kuyenda. Muli wakhanda ankakunyamulani kulikonse. Koma kenako, mutakula pang’ono munayamba kukwawa mpaka kufika poyenda. Pamsinkhu umenewu mwina munkakonda kuyendayenda, motero makolo anu ankakuyang’anira kwambiri komanso kukuikirani malire kuti musafike malo oopsa. Komabe, makolowo ankakulolani ndithu kuyenda nokha ndipo m’kupita kwa nthawi munaphunzira kuyenda bwinobwino ngakhale kuti munagwapo kangapo.

Umu ndi mmenenso zilili ndi nkhani yopereka ufulu kwa mwana. Tinganene kuti poyamba makolo amanyamula ana awo kulikonse. Iwo amatero powasankhira zochita nthawi zonse. Koma anawo akayamba kukula tingati makolo amawalola kukwawa. Iwo amawapatsa ufulu wosankha zochita zinazake. Komabe amawaikira malire kuti asachite zinthu zimene zingawabweretsere mavuto. Anawo akamasinkhuka, makolo amawalola kuyenda okha, kapena kuti kusankha okha zochita. Kenako akakula amatha ‘kunyamula katundu wawo’ paokha.—Agalatiya 6:5.

Chitsanzo Chabwino cha M’Baibulo

Zikuoneka kuti Yesu ali kamnyamata, makolo ake ankamupatsa ufulu koma iye sanapezerepo mwayi wochita zofuna zake. Iye ‘anapitiriza kumvera’ makolo ake ndipo “anali kukulabe m’nzeru ndi mu msinkhu, komanso mu chiyanjo cha Mulungu ndi cha anthu.”—Luka 2:52.

Makolo ayenera kutengapo phunziro pa nkhani imeneyi. Pamene ana awo akukula, ayenera kuwapatsa ufulu. Taonani zimene makolo ena ananena pankhani imeneyi.

“Poyamba ndinkalowerera kwambiri zochita za ana anga. Koma kenako ndinayamba kuwaphunzitsa mfundo zina n’kumawalola kusankha zochita pa zimene aphunzirazo. Nditachita zimenezi, ndinaona kuti anawo anayamba kusamala kwambiri posankha zochita.”—Anatero Soo Hyun, wa ku Korea.

“Ine ndi mwamuna wanga timada nkhawa ndi nkhani yowapatsa ufulu ana athu. Koma zimenezi sizitiletsa kuwapatsa ufulu wogwirizana ndi khalidwe limene akusonyeza.”—Anatero Daria, wa ku Brazil.

“Mwana wathu amagwiritsa ntchito bwino ufulu umene ndimamupatsa. Choncho ndimaona kuti ndi bwino kumamuyamikira. Inenso ndimam’patsa chitsanzo potsatira malamulo amene ndimam’patsawo. Mwachitsanzo, ndimamuuza kumene ndikupita komanso zimene ndikukachita. Ndikakhala kuti ndichedwa ndimamuuza.”—Anatero Anna, wa ku Italy.

“Ana athu timawauza kuti timawapatsa ufulu mogwirizana ndi zochita zawo.”—Anatero Peter, wa ku Britain.

Ana Azidziwa Zotsatira za Khalidwe Loipa

Baibulo limanena kuti: “N’kokoma kuti munthu asenze goli ali wamng’ono.” (Maliro 3:27) Njira imodzi yothandizira mwana kuti adziwe zotsatira za khalidwe loipa ndiyo kumuthandiza kudziwa kuti: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”—Agalatiya 6:7.

Makolo ena amakonda kuikira kumbuyo ana awo akalakwitsa. Amatero poganiza kuti akuwakonda. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti mwana ali ndi ngongole chifukwa chochita zinthu mosasamala. Kodi mwanayo angaphunzirepo chiyani ngati makolo atangomulipirira ngongoleyo? Komano angaphunzirepo chiyani ngati makolo amuuza kuti achite zinthu zimene zingamuthandize kubweza yekha ngongoleyo?

Ngati mwana wagwa m’vuto chifukwa cha khalidwe loipa, musiyeni kuti aphunzirepo kanthu. Makolo akamapanda kuchita zimenezi ndiye kuti akulakwitsa kwambiri. Chifukwa kumeneku ndi kumuwononga mwanayo osati kumuthandiza kuti adzakhale munthu wolongosoka. Motero mwanayo amaganiza kuti nthawi zonse pazikhala munthu womuteteza ndiponso womuikira kumbuyo akalakwitsa zinthu. Ndibwino kumawasiya achinyamata kuti akolole zimene afesa ndiponso kuti aphunzire kuthetsa mavuto awo. Zimenezi zidzawathandiza kuti aphunzitse ‘luntha lawo la kuzindikira, kuti azitha kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.’—Aheberi 5:14.

“Mwana Akamakula Amasintha”

Palibe angatsutse zoti makolo amene ali ndi achinyamata amakhala pa chintchito chachikulu. Nthawi zina angafike polira akamayesetsa kulera ana awo“m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.”—Aefeso 6:4.

Mwachidule tinganene kuti makolo safunika kumangolamulira ana awo koma amafunika kuwaphunzitsa kuti akhale ndi makhalidwe abwino. (Deuteronomo 6:6-9) Komatu izi sizophweka. Greg amene tamutchula kale uja anati: “M’pofunika kuzindikira kuti mwana akamakula amasintha. Motero ifenso tiyenera kumasintha mmene timachitira naye zinthu.”

Yesetsani kutsatira mfundo za m’Baibulo zimene takambirana m’nkhani ino. Musamawakhwimitsire kwambiri zinthu ana anu. Komabe musaiwale kuti inuyo monga kholo lawo muyenera kupereka chitsanzo chabwino. Baibulo limati: “Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.”—Miyambo 22:6.

[Mawu Otsindika patsamba 7]

Mwana muzimupatsa ufulu mwapang’onopang’ono ngati mmene amaphunzirira kuyenda

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Yesu ali kamnyamata ankapatsidwa ufulu woyenerana ndi msinkhu wake

[Bokosi patsamba 7]

“Azidziwa Kuti Kholo Ndinu”

Ngakhale mwana wanu atakhumudwa nazo, sonyezanibe mphamvu zanu monga kholo. Kumbukirani kuti nzeru za achinyamata zimakhala zoperewera, n’chifukwa chake amafunika kuwathandiza.—Miyambo 22:15.

Wolemba mabuku wina dzina lake John Rosemond anati: “N’zosavuta kuti makolo ayambe kupatsa ana awo ufulu wopitirira malire poopa kuwakhumudwitsa. Komano kumeneku si kuwathandiza ayi. Ngati atakhumudwa nazo, dziwani kuti ndi nthawi yoti anawo azindikire udindo wanu osati kuusokoneza. Ngakhale atapanda kusangalala nazo, afunika kudziwa kuti inuyo ndi amene mungawathandize kuti akhale anthu olongosoka.”—New Parent Power!

[Bokosi patsamba 9]

Kuwawonjezera Ufulu

Nthawi zambiri achinyamata amafuna ufulu wopitirira malire. Makolo ena amakhwimitsa kwambiri zinthu moti sawapatsa ana awo ufulu. Komatu n’zotheka kuchita zinthu mosapitirira malire. Kodi mungachite bwanji zinthu zimenezi? Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni kupeza poyambira. Kodi mwana wanu akuchita bwino zinthu ziti?

□ Kusankha bwino anthu ocheza nawo

□ Kusankha bwino zovala

□ Kugwiritsa ntchito bwino ndalama

□ Kufika pakhomo pa nthawi yake

□ Kumaliza ntchito zapakhomo

□ Kumaliza ntchito imene wapatsidwa kusukulu

□ Kupepesa akalakwa

□ Zina ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

Ngati mwana wanu akuchita bwino zinthu zambiri zimene talemba pamwambazi, ganizirani mmene mungamupatsire ufulu wowonjezereka.

[Chithunzi patsamba 7]

Aloleni kuti afotokoze maganizo awo musanawapatse malangizo alionse

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Makolo aziphunzitsa ana kuchita zinthu zolongosoka