Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Madzi oundana ku nyanja ya Arctic anayamba kuphwera m’chaka cha 2007. “Aka n’koyamba kuti madziwa aphwere chonchi kuyambira pamene anthu anaika makina ounikira madziwo.” Atayeza madziwo anapeza kuti ndi ochuluka kukwana dera lalikulu makilomita 4,280,000 ndipo izi zasonyeza kuti madziwo atsika ndithu tikayerekeza ndi mmene analili mu 2005.—NATIONAL SNOW AND ICE DATA CENTER, U.S.A.

Dziko la United States ndi limene lili anthu ambiri okhala ndi zida. Pa anthu 100 alionse m’dzikolo, anthu 90 ali ndi mfuti. Dziko lachiwiri pankhaniyi ndi la India. Kumeneku anthu anayi pa 100 alionse ali ndi mfuti.”—TIME, U.S.A.

Ku Miami m’boma la Florida m’dziko la United States kwabadwa mwana wa milungu 21 ndi masiku 6. Kamwanako kakulemera magalamu 283 ndi theka. Uyu ndi mwana amene anabadwa msanga kwambiri pa ana onse amoyo obadwa masiku asanakwane. Nthawi zambiri ana amene amabadwa m’milungu 23 ali olemera magalamu 400, sakhala ndi moyo.”—REUTERS NEWS SERVICE, U.S.A.

Kusefa Madzi M’nyanja Zamchere

Pofuna kuthetsa vuto la kusowa kwa madzi m’zilumba za m’nyanja ya mchere yotchedwa Aegean, asayansi a ku Girisi apanga “chipangizo choyamba padziko lonse chomwe chimayandama panyanja n’kumasefa madzi am’cherewo koma popanda kuwononga chilengedwe.” Chipangizochi chimayendera mphepo komanso magetsi a dzuwa ndipo tsiku lililonse chimasefa madzi ambiri moti amakwanira anthu pafupifupi 300. Chimagwira ntchito bwinobwino ngakhale panyanja pataipa motani, ndipo ngakhale chitakhala kutali, anthu amatha kuona mmene chikugwirira ntchito komanso amatha kupita nacho kulikonse kumene akufuna.

Anapeza Mafupa Akale

Lipoti la bungwe lina linati: “Chifukwa choti dera la kumpoto kwenikweni kwa Siberia . . . layamba kutentha, madzi ake oundana anayamba kusungunuka moti mafupa a nyama zakalekale ayamba kuonekera. Ena mwa mafupawo ndi a mtundu winawake wa nyama zikuluzikulu zofanana ndi njovu, mafupa a zipembere ndiponso a mikango.” Lipotili, linachokera m’tauni ya Cherskiy m’dera la Sakha m’dziko la Russia. Akuti anthu okonda kutolera zinthu zotere, komanso mabungwe a sayansi akumapereka ndalama zankhaninkhani pogula mafupa oterewa, ndipo makampani ena afika m’derali n’kumafunafuna mafupawa mothandizidwa ndi anthu a konko. Lipotilo linatinso: “Madzi oundana amene anakuta derali ayamba kusungunuka mwamsanga kwambiri moti m’malo ena . . . muli mafupa amene amaonekera pamwamba pa nthaka.—Reuters.

Apolisi Apeza Ntchito Yabwino ya Mowa

M’mbuyo monsemu apolisi oona za anthu olowa m’dziko la Sweden ankati akalanda mowa kwa anthu ofuna kulowetsa mowawo mozembetsa ankangoutaya. Lipoti la bungwe lina linati masiku ano mowa wozembetsawu “ukuthandiza boma pa nkhani ya mafuta a basi, sitima ndi zinthu zina zotero.” Lipotilo linachokera ku Stockholm ndipo linati m’chaka cha 2006, mowa wochuluka pafupifupi magaloni 185,000 umene analanda anausaundutsa mafuta “n’kumawathira m’mabasi, m’mathiraki ndiponso m’sitima zapamtunda.” Lipotilo linati “malonda a mafutawa ndi opindulitsa kwambiri chifukwa mowawo amangolanda.” Ubwino wina wa mafutawa ndi wakuti satulutsa utsi woononga chilengedwe.—Associated Press.

“Anthu Sakumasukirana Masiku Ano”

Nyuzipepala ina ya ku Australia inati: “Njira zotumizirana mauthenga pa kompyuta ndiponso pa telefoni zam’manja zachititsa kuti anthu ambiri padziko lonse asamamasukirane. Malinga ndi zimene katswiri wa zamaganizo, dzina lake Robin Abrahams ananena, anthu ambiri masiku ano samasuka akakhala pagulu kusiyana ndi kale. Dr Abrahams anati: “Kupita patsogolo kwa luso la zopangapanga kukuchititsa kuti anthu asamataye nthawi ndi zinthu zovuta komanso kuti azikhala ndi moyo wodzipatula. M’malo molankhulana, anthu amangotumizirana mauthenga.”—Sunday Telegraph.