Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Bukuli Ndi Labwino Kwambiri!”

“Bukuli Ndi Labwino Kwambiri!”

“Bukuli Ndi Labwino Kwambiri!”

▪ Mkulu wa gulu lina lochita kafukufuku wa zam’banja ananena mawu amenewa pofotokoza za buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Banja lina limene analifunsa pa kafukufukuyu linamupatsa bukuli ndipo linamuuza kuti kuphunzira bukulo kunawathandiza kukonzekera bwino ukwati wawo.

Mkuluyo analemba kalata yoyamikira banjalo chifukwa cha “mphatso yabwino kwambiri” imene linamupatsa. Kenako ananena kuti m’pofunika kuti banja ngati limeneli liziphunzitsa ena “zinthu zimene zingathandize kuti mabanja akhale olimba komanso kuti aziyenda bwino.” Iye anali ndi chikhulupiriro chakuti buku ngati la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja lingathandize mabanja kuthetsa mavuto awo. Iye ananena kuti banjali likuyenda bwino chifukwa chakuti lili ndi chikhulupiriro cholimba komanso limadalira thandizo la Mulungu.

Iye ananena kuti bukulo amalisiya patebulo lake nthawi zonse ndipo amaligwiritsa ntchito ophunzira akamufunsa malangizo okhudza banja. Pomaliza anati: “Sindinaonepo buku ngati limeneli. Bukuli ndi labwino kwambiri!”

Buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja lathandiza mabanja ambirimbiri padziko lonse lapansi. Lingakuthandizeninso kuti muzitsatira mfundo za m’Baibulo zimene zingapangitse kuti banja lanu likhale losangalala.

Ngati mukufuna kuitanitsa buku la masamba 192 limeneli, lembani m’mizere ili pansiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire buku limene lasonyezedwa panoli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo panyumba kwaulere.