Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kadziweni Kanyama Aka

Kadziweni Kanyama Aka

Kadziweni Kanyama Aka

YOLEMBEDWA KU BRAZIL

MUKUWONGOLA miyendo m’tchire, ndipo mwadzidzidzi mukuona tinyama tangati msulu tikubwera poteropo. Mukuchita mantha poganiza kuti mwina tinyamati n’taukali. Koma khazikani mtima m’malo. Ngakhale kuti ena amati tinyamati timaluma, kwenikweni tikukutsatirani chifukwa chochita chidwi ndi chikwama chanucho. Tinyama timeneti timangokhalira kufunafuna chakudya. Ndipotu pankhani ya zakudya, sitisankha ayi. Timadya nyongolotsi, abuluzi, akangaude, mbewa, zipatso ngakhalenso mazira a mbalame.

Tinyama timeneti timakhala tatitali mchira ndi mphuno yomwe. Timatha kuyendetsa mphunoyo mmene nkhumba imachitira. Tinyamati n’tatitali masentimita 66 ndipo mchira wakenso ndi wautali pafupifupi chimodzimodzi. Timapezeka m’madera otentha a ku America, makamaka kum’mwera cha kumadzulo kwa dziko la United States ndiponso kumpoto kwa dziko la Argentina.

Zazikazi zimayenda m’magulu ndipo mwina zimakhalapo 20, koma yaimuna iliyonse imayenda yokha. Kuti nyamazi ziziberekana, chaka chilichonse yaimuna imatsatira gulu la zazikazi zija. Pakatha milungu 7 kapena 8, zazikazi zija zimakhala zili ndi bere ndipo zimachoka pagululo n’kukamanga zisa m’mitengo. Iliyonse imabereka ana atatu kapena anayi. Pakatha pafupifupi milungu 6 zitabereka, nyamazi zimatenga anawo n’kubwereranso pagulu lija. Tianato timayenda molobodoka ndipo timangooneka ngati mpira wa chikopa chokhala ndi ubweya.

Tinyama timeneti tikamayenda m’tchire timangokhalira kununkhiza tikuyang’ana m’mwamba ndipo timakondanso kukumba pansi. Alimi amadana nato chifukwa timawononga kwambiri chimanga ndiponso timagwira nkhuku. Tinyamati timadziwanso kudziteteza tikamasakidwa. Tili ndi malo amene timabisala m’mitengo. Koma tili ndi njira inanso yodzipulumutsira. Tikamva mfuti kapena kuwomba m’manja, timanamizira kufa n’kudzigwetsa pansi. Koma mlenje akafika pamalopo amapeza kuti tathawa kalekale.

Ngati mutadzapita ku Brazil, n’kutheka kuti mukakumana nato tinyama timeneti. Ndiyetu musadzachite mantha ayi. Sitingakuvulazeni. Kungoti mwina tingadzalakelake mutatiponyerako zakudya zinazake zokoma.