Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mabanja Ali pa Vuto

Mabanja Ali pa Vuto

Mabanja Ali pa Vuto

“Ayi ndithu, ndapirira kokwanira.” Kodi munamvapo munthu wapabanja akunena zimenezi? Ngati muli pa banja, kodi nanunso munakhalapo ndi maganizo oterewa?

ANTHU ena amalowa m’banja atadziwana bwino pachibwenzi n’kuyamba kukondana kwambiri. Ena amalowa m’banja chifukwa chongotengeka mtima atakhala pachibwenzi kwa kanthawi kochepa chabe. Anthu onsewa amaganiza kuti akalowa m’banja adzakhala osangalala kwambiri. Koma mlangizi wina wa zam’banja anati: “Anthu ambiri amabwera kudzandiuza kuti akuona kuti banja lawakanika. Amakhala atatopa ndi mwamuna kapena mkazi wawo, banjalo ngakhalenso moyo wawo umene.” Ngakhale kuti anthuwa amakhala nyumba imodzi, umboni woti ali pabanja ndi mtchatho wokha basi.

Mabanja ena amatha chifukwa choti mavuto osiyanasiyana amene amakhalapo tsiku ndi tsiku amafika powakulira kwambiri. Mavutowa amabwera chifukwa chogwira ntchito yovuta, monga yogwira usiku nthawi zina, kapena yoweruka mochedwa kwambiri. Zimenezi zingachititse kuti ngakhale banja lolimba lisamakhale ndi nthawi yokwanira yocheza limodzi bwinobwino. Mavuto azachuma, kulera ana, kusamuka, kusintha ntchito, ndiponso matenda angasokonezenso chikondi ndi kupatsana ulemu pakati pa mwamuna ndi mkazi. Mwachidule, tingati m’kupita kwa nthawi mavuto a m’banja angasokoneze mgwirizano wa pakati pa mwamuna ndi mkazi wake.

Amayi ambiri apantchito amakhala ngati kuti analembedwanso ntchito ina kunyumba. Motero amatha kunyalanyaza zinthu zina zonse n’kumangoganizira za ntchito yawo yolembedwa ndi ana awo basi. Komanso, chifukwa chotopa, okwatirana ambiri amalephera kupeza nthawi yokwanira yokambirana zinthu bwinobwino. Motero ambiri amakhala opanikizika kwambiri komanso osungulumwa. N’chifukwa chiyani mabanja ambiri ali pamavuto otere? Kodi mungatani kuti banja lanu liziyenda bwino n’kukhala losangalala?