Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ngalande za ku Britain Zikuchititsabe Chidwi

Ngalande za ku Britain Zikuchititsabe Chidwi

Ngalande za ku Britain Zikuchititsabe Chidwi

YOLEMBEDWA KU BRITAIN

Chakumayambiriro kwa zaka za m’ma 1800, ku England, Scotland, ndi ku Wales kunali ngalande zosiyanasiyana zomwe atati aziphatikize pamodzi zingakhale zazitali pafupifupi makilomita 6,000. Kodi ngalandezi zinali za ntchito yanji, nanga masiku ano ndani amazigwiritsira ntchito?

KU BRITAIN kunkafunika njira yotsika mtengo komanso yofulumira yothandiza pa za mtengatenga ndi mtokoma chifukwa cha kukwera kwa ntchito za mafakitale m’zaka za m’ma 1700. Poyamba, katundu ankayenda naye pa magulu a mahatchi omwe nthawi zina ankakoka magaleta m’misewu imene inali yovuta kudutsamo nthawi yamvula. Misewuyo inkakhala yokumbika komanso yamatope kwambiri. Koma atayamba kupanga ngalandezi, zinali zosavuta kutenga katundu wambiri, mwina mpaka matani 30, pogwiritsira ntchito boti. Boti lotereli linkakokedwa ndi hatchi imodzi yokha.

Mu 1761, kalonga wa ku Bridgewater anakonza ngalande yoti azigwiritsira ntchito ponyamula malasha kuchokera ku migodi yake n’kumakawagulitsa ku Manchester, mzinda womwe unali pamtunda wa makilomita 16. Zitatero, kalongayu anayamba kupeza ndalama zambiri komanso mtengo wa malasha ku Manchester unatsika ndi theka. Pofika m’chaka cha 1790, anakonza ngalande zapamwamba kwambiri (zotchedwa Grand Cross) zomwe zinalumikiza mitsinje inayi ikuluikulu. Zinalumikizanso madoko angapo ndi chigawo chimene ntchito zambiri zamafakitale zinkachitikira ku England. Apa m’pamene panayambira ngalande zoterezi ku Britain.

Kamangidwe Ndiponso Ntchito za Ngalandezi

Akatswiri osiyanasiyana a luso la zomangamanga, anakonza njira zapamwamba kwambiri zothandiza kupatutsa madzi kuti akafike m’madera osiyanasiyana, ngakhale opezeka m’zigawo zokwera. Mmodzi wa akatswiriwa anali James Brindley, yemwe anadziphunzitsa yekha ntchitoyi. Akafuna kukonza ngalande, iye sankachita kulemba papepala kapena kujambula mapulani a ngalande imene akufuna kukonza. Mpaka pano, anthu amagoma akaona ngalande zosiyanasiyana ndiponso milatho imene akatswiriwa anapanga.

Panthawiyi kunali maboti opanda madenga, a mamita 20 m’litali ndiponso mamita awiri m’lifupi, n’cholinga choti azinyamula katundu wolemera monga malasha, laimu, miyala, dongo lopangira zinthu zadothi, zitsulo, njerwa ndiponso ufa. Maboti amenewa ankakokedwa ndi mahatchi amene ankayenda m’tinjira ta m’mphepete mwa ngalandezo. Iwo anapanganso maboti othamanga kwambiri amene ankanyamula katundu wofunika msangamsanga kapena wosachedwa kuwonongeka. Mabotiwa ankayenda osapumira, moti anthu ogwira ntchito m’mabotiwo ankachezera usiku onse.

M’ngalande zina, magulu a mahatchi, ankakoka maboti omwe ankanyamula anthu okwana 120 ndipo ankathamanga pa liwiro la makilomita pafupifupi 15 pa ola limodzi. Mahatchiwa ankasinthidwa pakapita maola angapo. Panali lamulo lakuti mabotiwa azikhala patsogolo pa maboti ena. Motero pangalande yotchedwa Bridgewater, mabotiwa ankakhala ndi chimpeni chachikulu kutsogolo chomwe chinkadula chingwe chokokera boti lililonse limene lingapezeke kutsogolo kwake. Chifukwa cha kumangidwa kwa ngalandezi, anthu wamba anayamba kumayenda maulendo aataliatali mosavutikira komanso popanda kuwononga ndalama zambiri.

Moyo wa Ogwira Ntchito M’mabotiwa

Ogwira ntchito m’maboti oyenda m’ngalandezi ankavutika kwambiri. Ntchito yawo inali yakalavulagaga ndipo nthawi zambiri inali yoika moyo pachiswe. Popeza kuti ankayendayenda, iwo analibe mwayi wopita kusukulu ndiponso wocheza ndi anthu ena.

Anthu amenewa anayamba kukongoletsa maboti awo mwaluso kwambiri. Ankajambulamo zithunzi za malo okongola, za maluwa ndiponso zithunzi zina. Zithunzizi ankazijambula kunja kwa botilo komanso mkati mwake, cha kutsogolo. Maboti amenewa ankakhala aakulu mamita atatu m’litali ndiponso mamita awiri m’lifupi moti zinali zotheka kuti wogwira ntchito m’botimo, mkazi wake komanso ana azikhalamo bwinobwino. Popeza kuti malo anali ochepa, anthu amenewa ankakhala ndi mabedi otheka kuwapinda ndipo ankalongedza bwinobwino katundu wawo m’malo osungiramo zinthu. Ankakongoletsa maalumali awo ndi nsalu zopeta bwino komanso m’malo awo ophikira ankaikamo zokongoletsera zonyezimira zadothi ndi zachitsulo. Zimenezi zinkachititsa kuti munthu akakhala m’botilo azimva ngati ali pakhomo ndithu. Azimayi a kumeneku ankagwira ntchito zambiri mwakhama. Ankaonetsetsa kuti m’botimo m’moyera nthawi zonse ngakhale kuti munkakhala modzaza katundu. Ankaonetsetsa kuti ngakhale zingwe zimene ankazikulungiza pa zopalasira mabotiwo ndi zoyera.

Ntchito ya Ngalandezo Inasintha

Mu 1825 ntchito ya ngalandezo inayamba kuchepa. Katswiri wina, dzina lake George Stephenson, anapanga njanji ya sitima zoyendera malasha yotchedwa Stockton and Darlington. Patadutsa zaka 20, anthu anayamba kugwiritsa ntchito njanji m’malo mwa ngalande, motero anasiya kukonza ngalandezo zikawonongeka. Pofuna kuti asamapikisane ndi a bizinesi ya maboti, makampani a njanji anayamba kugula ngalande. Nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha, maulendo a mungalande anayambanso kutha chifukwa anthu anakonza misewu yabwino. Palibe aliyense amene ankaganiza zoti anthu apitiriza kugwiritsa ntchito ngalande.

Koma chifukwa cha ntchito imene anthu komanso mabungwe ena akhala akugwira kwa zaka 50, ntchito ya ngalandezi siinatheretu. Ngakhale kuti maboti ena amanyamulabe katundu, anthu ena amagwiritsa ntchito mabotiwa ngati nyumba kapena zoyendera akakhala pa tchuti. Panopa n’zotheka kuyenda ulendo wokwana makilomita 3,000 kudzera mu ngalande zokongola za ku Britain. Anthu okonda maboti amenewa ayambanso kuchita zimene ankachita kale ndipo zikondwerero zawo zayambanso kutchuka kwambiri. Chifukwa cha kutchuka kwa maboti amenewa anthu ayamba kugwiritsa ntchito maboti ambiri kuposa kale. Panopa anthu akukonzanso ngalande mofanana ndi mmene ankachitira zaka 200 zapitazo.

Ngakhale zili choncho, ndi anthu ochepa chabe amene amasangalala poyenda m’ngalandezi paboti. N’chifukwa chiyani zili choncho? Chifukwa chakuti kukonzanso ngalandezi kunathandiza kuti anthu azipita kukacheza m’madera osiyanasiyana. Pofuna kusangalala, anthu amatha kupita kukaona malo ochititsa chidwi amene poyamba sankadziwika m’matawuni ndi m’midzi. Anthu oyenda pansi, okwera njinga komanso asodzi amayenda m’tinjira ta m’mphepete mwa ngalandezi. M’ngalandezi, komanso m’madamu amene amangidwa pofuna kusungira madzi oti aziyenda m’ngalande zimenezi, mumapezeka nyama, zomera komanso mbalame zosiyanasiyana.

Ntchito yokonza ngalande ku Britain inasintha zinthu kwambiri, koma osati m’njira imene anthu ankaganizira. Inde, ngalandezi zinabweretsa chitukuko, koma zinabweretsanso moyo wopanikiza. Komano n’zochititsa chidwi kuti panopa anthu amaona ngalandezi ngati malo okasangalala.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 14]

KUYENDA M’NGALANDE ZA PANSI PA NTHAKA

Ngalande zambiri za pansi pa nthaka zilibe tinjira m’mphepete mwake. Motero maboti a injini asanabwere, panali njira imodzi yokha yoyendera ndi boti m’ngalande zimenezi. Njira imeneyi inali yoopsa chifukwa ankatenga matabwa awiri n’kuwakhomerera kumbuyo kwa botilo, kudzanja lamanja ndi lamanzere. Ndiyeno anthu ankagona chagada, atagwira matabwawo mwamphamvu, miyendo yawo ataponda khoma la ngalandeyo. Kenaka ankayendetsa miyendoyo cham’mbali n’kumakankhira botilo kutsogolo. Ngakhale kuti ankayenda mu mdima; ankayatsa kandulo imodzi yokha moti zinali zosavuta kuphuluza n’kugwera m’madzimo. Nthawi zina akagwa ankavulala kwambiri mpaka kufa chifukwa botilo linkawakanikizira ku khoma la ngalandeyo. Panthawi inayake ku Britain kunali ngalande zosiyanasiyana moti atati aziphatikize pamodzi zingakhale zazitali makilomita 68. Zina mwa ngalandezi zinali zazitali kwambiri ndipo zinkakhala ndi akatswiri odziwa kukankha boti ndi miyendo. Ngalande yaitali kwambiri inali ya makilomita asanu. Panopa anaitseguliranso ku Standedge, mumzinda wa Yorkshire.

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy of British Waterways

[Bokosi/Zithunzi patsamba 15]

KUDUTSA M’MALO OKWERA

Poti madzi sayenda mokwera mtunda, kodi akatswiri aja ankatani ngati ngalande imene akumanga yafika pamtunda? Ankatha kuiyendetsa mozungulira mtundawo, ngakhale kuti zimenezi zinkachititsa kuti ngalandeyo italike. Nthawi zina ankakumba kuti ngalandeyo iyende pansi panthaka. Nthawi zinanso ankapanga zitseko zotchingira madzi a m’ngalandeyo. Zitseko zimenezi zinkatchinga madzi pakati pa zigawo ziwiri za ngalande zimene zikulephera kulumikizana chifukwa cha mtunda. Kuti boti lifike m’ngalande yachiwiriyo ankatseka zitseko zolowera m’ngalande ziwiri zonsezo. Kenako ankawonjezera kapena kuchotsa madzi pamene pali botilo kuti likwere kapena litsike mogwirizana ndi kukwera kwa ngalande imene likufuna kulowamoyo.

Komano nthawi zina ankalephera kubwezeretsa zitseko zotchingira madzi a mungalande. Izi n’zimene zinachitika ku Scotland, kumene anachita ntchito yaikulu yolumikiza ngalande ziwiri zakalekale za pakati pa mzinda wa Glasgow ndi Edinburgh. Zinali zovuta kumanganso zitseko 11 zotchingira madzi za ku Falkirk, zomwe kale ankagwiritsa ntchito polumikiza ngalande ya Union ndi ngalande yotchedwa Forth and Clyde, yomwe ndi ngalande yakale kwambiri padziko lonse yolumikiza nyanja ziwiri. Pofuna kuti athetse vuto limeneli anakonza chipangizo chonyamulira maboti n’kuwatukula m’mwamba. Chipangizochi n’chachitali mamita 35 ndipo chimatha kunyamula maboti 8 nthawi imodzi, anayi mbali iliyonse. Ntchito imeneyi imatenga mphindi 15 basi.

Nyuzi ina ya ku London inafotokoza kuti popanga chipangizo chimenechi panagona “luso lodabwitsa kwambiri.” Chipangizochi chimaonekera m’madzi a damu lalikulu lozungulira, lomwe amatha kuimikamo maboti 20.—The Times.

[Mawu a Chithunzi]

Top right: Courtesy of British Waterways

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 16, 17]

TIMAKONDA MABOTI A M’NGALANDEZI

Ngakhale kuti ndife achikulire ndithu, pa zaka zingapo zapitazi ine ndi mkazi wanga takhala tikukwera maboti a m’ngalande zimenezi tikakhala pa tchuti. Ulendo wake sukhala ngati wa pagalimoto chifukwa umakhala wapang’onopang’ono komanso wa phee. Tikakwera maboti amenewa, timayenda pa liwiro la makilomita asanu okha basi pa ola limodzi. N’chifukwa chiyani timayenda pang’onopang’ono chonchi? Timaopa kuti tingachititse mafunde amene angawononge makoma a ngalandezi. Motero, nthawi zambiri ngakhale anthu amene amayenda pansi atatenga agalu awo amatha kutipitirira.

Ubwino wina woyenda pang’onopang’ono ndi wakuti timatha kuona malo bwinobwino komanso kupereka moni kwa anthu amene tikukumana nawo. Ndipotu malo ena amene timaona ndi okongola kwambiri. Timakonda kuchita hayala maboti a ku South Wales ndipo timayenda nawo m’ngalande ya Monmouthshire ndi ya Brecon. Ngalandeyi ndi yaitali makilomita 50 ndipo imachokera ku Wales mpaka kukafika ku mapiri a Brecon, omwe ndi aatali mamita 886. Timasangalala kwambiri tikafika pa zitseko zotchingira madzi, n’kuima kuti boti lathu likwere kapena litsike mogwirizana ndi kukwera kwa ngalande imene tikufuna kulowamoyo.—Onani bokosi la patsamba 15.

Mabotiwa amakhala ndi zinthu zonse zofunikira pa ulendowo ndipo timakhala momasuka kwabasi. Ena amakhala ndi zipinda ziwiri zogona zokhala ndi bafa komanso chimbudzi. Amakhalanso ndi zipangizo zotenthetsera m’zipindazo madzulo kukazizira. Nthawi zambiri timaphika tokha chakudya ndipo ngati sitikufuna kuphika timakadya ku malo odyera a m’mphepete mwa ngalandezo.

Zimasangalatsa kwambiri kuyenda m’ngalandezi nthawi ya m’mawa chifukwa m’madzimo mumaoneka zithunzithunzi za mitengo ndi mapiri a m’mphepete mwa ngalandezo. Kumakhala kuli zii moti mumangomva kulira kwa mbalame basi. Mbalame zina za mtundu wa akakowa zimangokhala phee m’mbali mwa ngalandezo ndipo nthawi zina zimayenda pang’onopang’ono kutsogolo kwathu.—Nkhaniyi tachita kutumiziridwa ndi munthu wina.

[Mawu a Chithunzi]

Courtesy of British Waterways

Top right: By kind permission of Chris & Stelle on Belle (www.railwaybraking.com/belle)

[Mawu a Chithunzi patsamba 13]

Courtesy of British Waterways