Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Vuto Lokhala Alubino

Vuto Lokhala Alubino

Vuto Lokhala Alubino

YOLEMBEDWA KU BENIN

“AKANDIPATSA fomu kuti ndilembepo mtundu wanga, ndimalemba kuti ndine wakuda ngakhale kuti thupi langa ndi loyera kuposa la mzungu,” anatero John. Iye amakhala kumadzulo kwa Africa cha kumalire kwa dziko la Benin ndi Nigeria. John ndi alubino. Munthu akakhala alubino, khungu, maso kapena tsitsi zimasintha mtundu. Kodi zimenezi ndi zofala motani? Kodi zimakhudza bwanji moyo wa munthu? Kodi n’chiyani chingathandize anthu oterewa kuti azikhala mosangalala? *

Ngakhale kuti anthu akuda ndi amene amaonekera kwambiri akakhala alubino, vutoli limakhudza anthu a mitundu yosiyanasiyana ndiponso a m’mayiko osiyanasiyana. Ofufuza apeza kuti pafupifupi munthu mmodzi pa anthu 20,000 alionse amakhala alubino.

Vutoli limakhala la kumtundu ngakhale kuti nthawi zina sipakhala wachibale wina wodziwika amene anakhalapo alubino. Umu ndi mmene zinalili ndi John. Achibale ake amanena kuti sakudziwa munthu aliyense pa mtundu wawo amene anali alubino.

Anthu ambiri amati Apwitikizi akale ofufuza malo m’zaka za m’ma 1600 ndi amene anayambitsa dzina lakuti “alubino.” Pamene ankadutsa kumadzulo kwa Africa, anaona kuti pakati pa anthu okhala m’madera a m’mphepete mwa nyanja panali anthu akuda komanso oyera. Iwo anaganiza kuti ndi anthu a mitundu iwiri yosiyana moti anthu akudawo ankawatcha a Niguro ndipo oyerawo ankawatcha alubino.

Khungu ndi Maso Zimasintha Mtundu

Anthu ambiri oyera akapsa ndi dzuwa, khungu lawo limaderako pang’ono chifukwa cha mphamvu ya thupi yoteteza khungu ku dzuwa. Vuto limene John ali nalo lokhudza khungu, maso ndiponso tsitsi lake n’lofala kwambiri. * M’thupi lake mulibe mphamvu imene imachititsa kuti khungu lizioneka lakuda. Kodi vuto limeneli limakhudza bwanji khungu? Anthu otere sakhala ndi mphamvu yoteteza khungu ku dzuwa choncho khungu lawo limapsa. Kupsa ndi dzuwa pakokha n’kosautsa, ndipo anthu amene ali ndi vuto limeneli akapanda kuteteza bwino khungu lawo amadwala khansa ya pakhungu. Izi zimachitika kawirikawiri m’madera otentha.

Kuti alubino adziteteze, chofunika kwambiri ndi kuteteza khungu lawo ndi zovala zoyenera. Mwachitsanzo, John ndi mlimi. Motero akamagwira ntchito kumunda amavala chipewa cha khonde lalikulu komanso malaya aatali manja. Ngakhale kuti amachita zimenezi, iye anati: “Nthawi zina thupi lonse limakhala lili juu kutentha. Ndikafika kunyumba ndimayamba kukanda mikono mpaka khungu limasupuka.”

Kudzola mafuta oteteza ku dzuwa ndi njira inanso yodzitetezera. Mafutawo afunika kukhala ndi mphamvu yokwanira yoteteza ku dzuwa ndipo angamawadzole asanapite padzuwa komanso pambuyo pokhala pa dzuwa malinga ndi malangizo ake.

Vuto limeneli limakhudza maso m’njira zosiyanasiyana. Mbali yakuda ya diso lathu imakhala ndi mphamvu yodziteteza ku dzuwa. Koma m’maso mwa anthu amene ali ndi vuto limeneli simukhala mwakuda moti dzuwa limalowa n’kumachititsa kuti azimva kupweteka. Kuti maso awo asawonongeke ambiri amavala zipewa kapena magalasi oteteza maso awo. John ananena kuti masiku ena amakhala bwinobwino popanda kuvala zotetezera maso ake. Koma ananenanso kuti usiku amavutika ndi kuwala kwa magetsi a galimoto.

Anthu ambiri amanena kuti maso alubino amakhala ofiira, koma zimenezi si zoona. Mbali yakuda ya maso a anthu otere imakhala yotuwirapo, yakhofi kapena ya buluu. Nanga n’chifukwa chiyani maso awo amaoneka ofiira? Buku lina linati: “Akakhala malo owala, maso awo amaoneka ofiira chifukwa choti alibe mphamvu imene imachititsa kuti maso azioneka akuda. Kufiira kumeneku kumachokera mkati mwa diso.” Tingati zimenezi n’zimenenso zimachititsa kuti nthawi zina pachithunzi munthu azioneka kufiira maso ngati pojambula chithunzicho anagwiritsa ntchito fulashi.—Facts About Albinism.

Alubino ambiri amavutika maso. Vuto limodzi limene amakhala nalo ndi lakuti mitsempha yochokera m’maso silumikizana bwino ndi ubongo. Izi zimachititsa kuti asamaone bwino chifukwa diso lina siligwirizana bwino ndi linzake poona chinthu chinachake. Vutoli lingathe ngati atamagwiritsa ntchito magalasi kapena ngati atachitidwa opaleshoni.

M’mayiko ambiri thandizo la kuchipatala silipezeka ndipo ngati litapezeka limakhala lokwera mtengo kwambiri. Kodi n’chiyani chimamuthandiza John pa vuto lake la masoli? Iye anati: “Ndimakhala wosamala kwambiri. Polumpha msewu ndimayang’ana komanso ndimamvetsera mosamala. Ndikamva kulira kwa galimoto iliyonse imene ndikutha kuiona, sindiyerekeza dala kulumpha msewu.”

Vuto lina limene alubino amakhala nalo ndi kuyendayenda kwa maso. Izi zimachititsanso kuti azivutika kuona bwino zinthu. Nthawi zina amangoona zinthu zimene zili pafupi kwambiri koma nthawi zina amaona zimene zili patali zokha. Kuvala magalasi kumathandiza kuti aziona bwino koma sikuthetsa chimene chimayambitsa vutolo. Anthu ena amene ali ndi vuto limeneli amagwira m’munsi mwa diso lawo akamawerenga kuti lisamayendeyende. Nthawi zina amaweramitsa mutu wawo ndipo zimawathandiza.

Vuto limene John ali nalo ndi lakuti saona patali. Iye ndi wa Mboni za Yehova ndipo ananena kuti: “Ndikafuna kuwerenga ndimaika buku pafupi kwambiri ndi maso anga. Bukulo likangofika malo oyenera ndimatha kuwerenga mofulumira kwambiri. Izi zimandithandiza powerenga Baibulo tsiku lililonse.” Iye anapitiriza kuti: “Ndikapatsidwa nkhani kumpingo ndimaikonzekera kwambiri kuti ndizingokamba mosadalira kwambiri zimene ndalemba. Ndine wosangalala kwambiri chifukwa magazini a Nsanja ya Olonda a zilembo zazikulu alipo m’Chiyoruba chimene ndimalankhula.”

Ana amene ndi alubino okhala ndi vuto la maso amavutika kwambiri kusukulu. Makolo ena a ana amenewa amakaonana ndi aphunzitsi a mwana wawo komanso akuluakulu apasukulupo kuti mwana wawo athandizidwe moyenera. M’masukulu ena mumakhala bolodi ndi mapepala amitundu yoyenera, mabuku a zilembo zikuluzikulu komanso matepi oti ana azimvetsera. Ngati patakhala mgwirizano pakati pa makolo, aphunzitsi komanso akuluakulu a pa sukulu, mwana yemwe ali ndi vuto limeneli atha kumakhoza bwino kusukulu.

Anthu Amawasala

Alubino ambiri sada nkhawa ndi vuto lawo. Koma ambiri amada nkhawa chifukwa chakuti anthu amawasala. Izi zimakhala zosautsa kwambiri makamaka kwa ana.

M’madera ena a kumadzulo kwa Africa, ana amene ali ndi vuto limeneli amasekedwa ndipo amapatsidwa mayina achipongwe. M’madera ena amapatsidwa dzina la Chiyoruba lakuti “Afini” kutanthauza kuti “chidangwaleza.” Ana ndi amene amasekedwa kwambiri poyerekeza ndi akuluakulu. Ngakhale kuti anthu ambiri a kumadzulo kwa Africa sakonda kukhala m’nyumba, anthu amene ali ndi vutoli amangobindikira m’nyumba. Izi zimachititsa kuti anthuwo azidziona ngati osafunika komanso achabechabe. John anali ndi maganizo amenewa asanaphunzire choonadi cha Mawu a Mulungu. Koma atangobatizidwa mu 1974, moyo wake unasinthiratu. Poyamba ankangobindikira m’nyumba koma tsopano anazindikira kuti ali ndi udindo wopita kukaphunzitsa anthu chiyembekezo chosangalatsa chimene waphunzira. Iye anati: “Vuto lawo lauzimu ndi lalikulu kwambiri ndikaliyerekezera ndi vuto langa lakuthupi.” Kodi anthu amamuseka akamalalikira? Iye anati: “Anthu osafuna uthenga wa m’Baibulo amandiseka chifukwa cha mmene ndimaonekera, koma izi sizichitikachitika. Sindikhumudwa nazonso chifukwa ndikudziwa kuti anthuwo amadana nane chifukwa cha uthenga umene ndimalalikira osati maonekedwe anga.”

Vuto Lokhala Alubino Lidzatha

Anthu asintha njira zosamalirira anthu amene ali ndi vuto limeneli. Achipatala apeza njira zabwino zothandizira alubino. Palinso mabungwe ena amene amakambirana ndi anthu kuti azimvetsa vuto limeneli. Koma ndi Mulungu yekha amene angathetseretu vuto lokhala alubino.

Vuto lokhala alubino ndi limodzi mwa mavuto amene anabwera chifukwa cha kupanda ungwiro kumene kunayamba chifukwa cha uchimo wa Adamu. (Genesis 3:17-19; Aroma 5:12) Posachedwapa Yehova adzachititsa kuti munthu aliyense amene amamukhulupirira, akhale ndi thupi langwiro. Izi zidzatheka chifukwa cha nsembe ya dipo imene Yesu Khristu anapereka. Iye ndi amene ‘adzachiritsa nthenda zonse.’ (Salmo 103:3) Vuto lokhala alubino lidzatheratu ndipo aliyense amene ali ndi vutoli adzaona kukwaniritsidwa kwa mawu a pa Yobu 33:25, akuti: “Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana; adzabwerera ku masiku a ubwana wake.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Kukhala alubino n’kosiyana ndi kukhala ndi matenda osintha mtundu wa khungu. Onani Galamukani! ya October 8, 2004 tsamba 28.

^ ndime 8 Onani bokosi lofotokoza mitundu yosiyanasiyana ya mavuto a anthu amenewa.

[Mawu Otsindika patsamba 29]

“Vuto lawo lauzimu ndi lalikulu kwambiri ndikaliyerekezera ndi vuto langa lakuthupi.”—John

[Bokosi patsamba 28]

MAVUTO OSIYANASIYANA A ALUBINO

Mavuto a alubino alipo osiyanasiyana:

Lokhudza khungu, tsitsi ndi maso. Vuto limeneli limachititsa kuti khungu, tsitsi ndi maso zisinthe mtundu. Pali mitundu 20 ya vuto limeneli.

Vuto lokhudza maso okha. Vuto limeneli limangokhudza maso okha koma khungu ndi tsitsi zimakhala bwinobwino.

Pali mitundu ina ya vuto la alubino imene panopo siikudziwika bwino. Mwachitsanzo Dr. Hermansky ndi Dr. Pudlak anatulukira mtundu wina wa vuto limeneli umene umachititsa kuti munthu asamachedwe kusupuka kapena kutuluka magazi. Anthu ambiri a ku Puerto Rico ali ndi vuto limeneli ndipo akuti munthu mmodzi pa anthu 1,800 alionse a kumeneku ndi alubino a mtundu umenewu.