Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi Champhamvu Kuposa Mphepo Yamkuntho

Chikondi Champhamvu Kuposa Mphepo Yamkuntho

Chikondi Champhamvu Kuposa Mphepo Yamkuntho

Mphepo zamkuntho zotchedwa Katrina ndi Rita zitawomba ku gombe lotchedwa Gulf Coast ku United States mu 2005, zinawononga kwambiri zinthu ndipo anthu ambiri anafa. Mboni za Yehova zambirimbiri zinakhudzidwanso ndi tsokali.

Motsogoleredwa ndi ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku United States, makomiti opereka chithandizo pakagwa tsoka anayamba kuthandiza anthu mwamsanga. Ku Louisiana, anakhazikitsa malo 13 operekera chithandizo, nyumba 9 zosungira katundu ndiponso malo 4 omwetsera mafuta. Maguluwa ankagwira ntchito m’dera lalikulu kwambiri lokwana makilomita 80,000. Pafupifupi Mboni 17,000 zochokera m’madera onse ku United States ndiponso m’mayiko ena 13, zinadzipereka pa ntchito yopereka chithandizo ndi kumanganso nyumba. Zotsatira zake zinasonyeza kuti chikondi chachikhristu ndi champhamvu kuposa masoka achilengedwe.—1 Akorinto 13:1-8.

Anthu ongodziperekawa anakonza nyumba zoposa 5,600 za Mboni zinzawo ndiponso Nyumba za Ufumu 90, zomwe Mboni za Yehova zimachitira misonkhano yawo. Chiwerengerochi chikuimira pafupifupi nyumba zonse zowonongeka zimene zinakonzedwa. Potsatira lemba la Agalatiya 6:10 limene limalimbikitsa Akhristu kuti ‘azichitira onse zabwino,’ Mboni za Yehova zinathandizanso anthu ambiri omwe si Mboni.

NGAKHALE kuti anthu ongodziperekawa anadzimana zinthu zina kuti athe kugwira nawo ntchitoyi, iwo anapeza madalitso ambiri. Tamvani zimene Mboni zokwana 7, zimene zinkayang’anira ntchitoyi, zinanena.

“Ntchito Yosangalatsa Kwambiri M’moyo Wanga”

Robert: Kugwira ntchito m’komiti yopereka chithandizo pakagwa tsoka kwakhala kosangalatsa kwambiri m’moyo wanga. Ndili ndi zaka 67 ndipo ndine wamkulu m’zaka kuposa anzanga m’komitiyi. Ndinagwira ntchito ndi gulu longodzipereka, ndipo pagululi panali Mboni zachinyamata zambiri zokonda zinthu zauzimu. N’zolimbikitsa kwambiri kuona achinyamata akusonyeza mtima wodzipereka chifukwa chokonda Yehova ndi Akhristu anzawo.

Mkazi wanga Veronica wakhala akundithandiza kwambiri. Iye anavomereza maganizo anga akuti ndisiye ntchito yomwe ndakhala ndikugwira kwa zaka zoposa 40, n’cholinga chakuti tidzagwire ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi masoka. Panopa, timagwira ntchito yoyeretsa maofesi kamodzi pamlungu. Taphunzira kugwiritsa ntchito ndalama zochepa ndipo sitifuna zambiri pamoyo. Kugwira ntchito limodzi ndi abale ndiponso alongo kwatithandiza kumvetsadi chimene kuika Ufumu wa Mulungu patsogolo m’moyo kumatanthauza. (Mateyo 6:33) Mobwerezabwereza, taona kuti Yehova amasamalira bwino anthu ake.

Frank: Ndimayang’anira dipatimenti ya zakudya ku malo operekera chithandizo mu mzinda wa Baton Rouge. Poyamba, tinkagwira ntchito Lolemba mpaka Lamlungu kwa maola 10 kapena 12 tsiku lililonse, kuti tithe kudyetsa anthu odzipereka kudzagwira ntchito. Komabe, madalitso amene tinapeza anali ambiri. Mwachitsanzo, tinaona ndi maso athu mphamvu ya chikondi chachikhristu.

Anthu ambiri ongodzipereka omwe anathandiza pantchito yokonza zakudya kwa mlungu umodzi kapena kuposa, anapempha kuti abwerenso kudzagwira ntchito. Ena ankatilembera mapositikadi komanso kuimba foni pofuna kuyamikira mochokera pansi pa mtima mwayi womwe anali nawo wogwira nafe ntchito. Ineyo ndiponso mkazi wanga Veronica, takhudzidwa mtima kwambiri poona mzimu wawo wodzipereka.

Anakhudzidwa Kwambiri

Gregory: Ine ndi mkazi wanga Kathy tinagulitsa nyumba yathu ku Las Vegas, Nevada, ndipo tinagula lole yaing’ono yokhala ndi kalavani, imene panopa ndi nyumba yathu. Kukhala ndi moyo wosafuna zambiri kwatithandiza kugwira nawo ntchito yothandiza anthu okhudzidwa ndi tsoka ku Louisiana kwa zaka zoposa ziwiri. Kuposa kale lonse, panopa tikutha kuona ndi maso athu kukwaniritsidwa kwa mawu a m’Baibulo opezeka pa Malaki 3:10, akuti: “Mundiyese, . . . ati Yehova wa makamu, [ndipo muone] ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.”

Nthawi zambiri timangodabwa tikamva anthu akuti, “Ee! Koma ndiye ndinu odzimana bwanji!” Zaka 30 zapitazo, ine ndi Kathy tinkafuna kukatumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku United States, koma tinalephera chifukwa chakuti tinali ndi udindo wolera ana. Ntchito yopereka chithandizo pakagwa tsoka yakwaniritsa chikhumbo chathu chofuna kuchita zambiri potumikira Mulungu. Takhalanso ndi mwayi wapadera wogwira ntchito ndi Mboni zinzathu, zomwe zina ndi zaluso kwambiri. Mwachitsanzo, mmodzi wa abale ophika zakudya anakhalapo mkulu wa ophika pa lesitilanti inayake yapamwamba, ndipo m’bale winanso anagwirapo ntchito yophikira mapulezidenti awiri a ku United States.

Kwa anthu ambiri ongodzipereka, ntchito yopereka chithandizo pakagwa tsoka ndi yosaiwalika. Mwachitsanzo, pofotokoza ntchito yake yothandiza anthu okhudzidwa ndi chimphepo chamkuntho, m’bale wina wazaka 57 ankachita kuoneka kuti wakhudzidwa kwambiri. Ngakhale Mboni zina zomwe sizinakwanitse kudzathandiza zakhala zikutilimbikitsa kwambiri. Mwachitsanzo, anthu awiri ogwira ntchito yochotsa nkhungu ndi ndere m’makoma a nyumba anatibweretsera nsalu imene inalembedwa ndi kusainidwa ndi aliyense, kuphatikizapo ana, m’mipingo itatu yakwawo ku Nebraska.

‘Taona Mulungu Akusamalira Anthu Ovutika’

Wendell: Patapita tsiku limodzi mphepo yamkuntho yotchedwa Katrina itachitika, nthambi ya ku United States inandipempha kuti ndikafufuze mmene ngoziyo yawonongera Nyumba za Ufumu komanso nyumba za Mboni za Yehova ku Louisiana ndi Mississippi. Umu ndi mmene ndinayambira ntchito yanga ndiponso kuphunzira zinthu zambiri. Popeza tinakhala zaka 32 m’dera limene likufunika olengeza Ufumu ambiri, ine ndi mkazi wanga Janine tinaona Yehova akusamalira anthu ake. Koma panopa taona Mulungu akusamalira atumiki ake ambirimbiri panthawi yochepa.

Ndine tcheyamani m’komiti yopereka chithandizo pakagwa tsoka ya ku Baton Rouge. Ntchitoyi ndi yovuta, koma imandisangalatsa kwambiri. Pogwira ntchitoyi, tonse mu komitiyi taona mobwerezabwereza Mulungu akuthetsa mavuto, kutipatsa njira zochitira zinthu ndiponso kusamalira anthu ovutika m’njira imene Atate Wamphamvuyonse yekha ndi amene angathe.

Anthu ambiri amatifunsa kuti, “Kodi inuyo ndi mkazi wanu mukutha bwanji kugwirabe ntchito yothandiza anthu mpaka pano, pambuyo pa zaka zoposa ziwiri?” Zakhaladi zovuta, ndipo tasintha zinthu zambiri pamoyo wathu. Komabe, chosangalatsa n’chakuti taona ubwino wokhalabe ndi ‘diso lolunjika chimodzi.’—Mateyo 6:22.

Titayamba ntchito yofufuza ndi kupulumutsa anthu kwa nthawi yoyamba mumzinda wa New Orleans, tinalibe nthawi yokwanira yopuma. Komanso, asilikali anali mbwee mumzindawu chifukwa cha chipwirikiti ndi ziwawa zomwe zinkachitika m’misewu. Zinali zosavuta kugwa ulesi ukangoganizira chintchito chachikulu chomwe tinali nacho.

Tinakumana ndi Mboni zambirimbiri zomwe zinataya zinthu zochuluka. Tinapemphera nawo limodzi ndi kuyesetsa kuwalimbikitsa. Kenako, mothandizidwa ndi Yehova, tinayamba kugwira ntchito. Nthawi zina, chifukwa cha zinthu zambiri zimene ndaona zikuchitika pa zaka ziwiri zimene ndakhala kuno, ndimaona ngati ndatha zaka zambirimbiri.

Nthawi ndi nthawi, makamaka pamene ndinkaona kuti ndatopa kwambiri ndiponso ndathedwa nzeru, anthu ambirimbiri ongodzipereka ankafika kudzagwira nafe ntchito, ena kwa miyezi ingapo ndipo enanso kwa nthawi yaitali ndithu. Kuona anthu ambiri, kuphatikizapo achinyamata, achimwemwe ndiponso ofunitsitsa kuthandiza kwatilimbikitsa kwambiri.

Nthawi zambiri Yehova anatithandiza. Mwachitsanzo titangofika, tinapeza kuti mitengo yagwera nyumba za abale zoposa 1,000. Popeza tinalibe zida ndiponso anthu oti agwire ntchito yoopsa yochotsa mitengoyi, ife pakomiti yathu tinangopemphera. Tsiku lotsatira, m’bale yemwe anali ndi lole ndiponso zida zomwe tinkafuna anadzipereka kutithandiza. Panthawi inanso pemphero lathu linayankhidwa patangotha mphindi 15 zokha. Ndiponso panthawi ina, zida zomwe tinkapempherera zinali m’njira tisananene n’komwe kuti ame. Ndithudi, Yehova anasonyeza kuti ndi “Wakumva pemphero.”—Salmo 65:2.

“Ndikunyadira Kukhala wa Mboni za Yehova”

Matthew: Patangopita tsiku limodzi mphepo yamkuntho ya Katrina itachitika, ndinathandiza pa ntchito yopereka kwa anthu m’deralo matani 15 a zinthu zimene abale anapereka monga chakudya, madzi ndi zinthu zina zofunika. Anthu a Yehova anasonyezadi kuti ndi opatsa.

Kuti tikwanitse kugwira ntchito imeneyi bwino, ine ndi mkazi wanga Darline tinasamukira kufupi ndi dera lomwe linakhudzidwa ndi mphepo, pamtunda wa maola awiri kuyenda pagalimoto. Mboni ya kumeneku inatilemba ntchito ya maola ochepa, n’cholinga choti tizithera nthawi yathu yambiri ku ntchito yopereka chithandizo. Mboni inanso inatipatsa nyumba. Mtima wanga umadzaza ndi chiyamiko chifukwa chokhala m’gulu la abale achikondi ngati limeneli ndipo ndikunyadira kukhala wa Mboni za Yehova.

Ted: Itangotha mphepo yamkuntho ya Katrina, ine ndi mkazi wanga Debbie, tinadzipereka kuti tigwire nawo ntchito yothandiza anthu. Patangopita masiku ochepa, ndinapeza kalavani yakale yotalika mamita 9 yoti galimoto yathu itha kukoka ndipo inkagulitsidwa pa theka la mtengo wake, chotero tinakwanitsa kuigula. Kalavaniyo inali yankho la mapemphero athu ndipo ndi imene yakhala nyumba yathu kwa zaka zoposa ziwiri.

Ntchito yathu itaima pang’ono, tinakagulitsa nyumba ndiponso katundu wathu wambiri. Zimenezi zinatipatsa mpata wokagwira ntchito ina ku New Orleans kumene ndimayang’anira ntchito yonse. Chinthu chimene chatisangalatsa kwambiri ndicho kuona mmene Yehova wasonyezera kuti ndi “Mulungu wa chitonthozo chonse” kwa anthu amene amamulambira. Kuwonjezera pa kuwonongeka kwa nyumba zawo ndiponso Nyumba za Ufumu, abale ambiri anataya mipingo ndi magawo awo amene ankalalikiramo uthenga wabwino, chifukwa cha kusamutsidwa.—2 Akorinto 1:3.

‘Chikhulupiriro Chawo Chinakhudza Mitima Yathu’

Justin: Mu October 2005, panali pempho lakuti anthu ongodzipereka akagwire ntchito yothandiza anthu amene anagweredwa tsoka ku Gulf Coast. Mwamsanga, ine ndi mkazi wanga Tiffany, tinalembetsa ndipo mu February 2006 tinaitanidwa kukathandiza gulu lokhoma madenga, lomwe linali ku malo operekera chithandizo pakagwa tsoka a Kenner, ku New Orleans.

Tsiku lililonse panyumba iliyonse imene tagwira ntchito, tinkakumana ndi Mboni za kumeneko zimene chikhulupiriro chawo ndi kudalira kwawo Mulungu zinakhudza mitima yathu. Ndipo tsiku ndi tsiku tinkaona umboni wakuti kudalira zinthu zakuthupi n’kupanda nzeru. Tilibe mawu ofotokozera chimwemwe chomwe tapeza pothandiza Akhristu anzathu komanso poona zimene Yehova wathandiza anthu ake kuchita.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]

Moyo wa Ogwira Ntchito Yopereka Chithandizo

Anthu ogwira ntchito ku khitchini pamalo operekera chithandizo pakagwa tsoka amayamba ntchito yawo m’mamawa cha m’ma 4:30. Nthawi ikakwana 7 koloko, anthu onse ogwira ntchito amakumana ku malo odyera ndipo amakambirana lemba la m’Baibulo kwa mphindi 10 asanayambe kudya. Masiku ena panthawiyi, tcheyamani amalengeza anthu atsopano ndiponso amasimba nkhani zolimbikitsa zimene zachitika.

Akapereka pemphero loyamikira, onse amadya chakudya chophikidwa bwino ndipo kenako amanyamuka, ulendo ku ntchito. Ena amatsala pamalowa kuti agwire ntchito m’maofesi, ku londile kapena ku khitchini. Anthu ophika chakudya amakonza chakudya cha masana chomwe chimadzatengedwa ndi anthu a m’magulu ogwirira ntchito kutali.

Lolemba lililonse madzulo, gulu lonse limakumana kuti liphunzire Baibulo pogwiritsa ntchito nkhani ya m’magazini ya Nsanja ya Olonda yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Maphunziro amenewa amawathandiza kukhalabe olimba mwauzimu. Ndipo zimenezi zimawathandiza kukhala osangalala popirira mavuto komanso kuiona bwino ntchito yawo.—Mateyo 4:4; 5:3.

[Bokosi patsamba 19]

“Ndinali Kukuganizirani Molakwa Anthu Inu”

Mayi wina ku New Orleans anaika chikwangwani pakhomo pake cholembedwa kuti: “Mboni za Yehova Kuno Ayi.” Koma tsiku lina, gulu la anthu ongodzipereka linayamba kukonza nyumba yomwe inawonongedwa ndi mphepo yamkuntho, tsidya lina la msewu moyang’anizana ndi nyumba yake. Tsiku ndi tsiku, mayiyu ankaona kuti ogwira ntchitowo anali ogwirizana kwambiri. Iye anachita chidwi kwambiri moti anapita pamalo antchitowo kuti akaonetsetse zimene zinali kuchitika. Atadziwa kuti anthuwo anali Mboni za Yehova, iye anawauza kuti palibe munthu ndi mmodzi yemwe wa kutchalitchi kwake yemwe anayesa ngakhale kungomuimbira foni, chichitikireni mphepo yamkunthoyo. Kenako iye anati: “Ndazindikira tsopano kuti ndinali kukuganizirani molakwa anthu inu.” Zotsatira zake zinali zakuti, mayiyu anachotsa chikwangwani chija ndipo anapempha Mboni za Yehova kuti zizibwera kunyumba kwake.

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Robert ndi Veronica

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Frank ndi Veronica

[Chithunzi patsamba 17]

Gregory ndi Kathy

[Chithunzi patsamba 17]

Wendell ndi Janine

[Chithunzi patsamba 18]

Matthew ndi Darline

[Chithunzi patsamba 18]

Ted ndi Debbie

[Chithunzi patsamba 18]

Justin ndi Tiffany