Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Fotokozani Fanizoli

1. M’fanizo lopezeka pa Luka 18:9-14, kodi Mfarisiyo anali munthu wotani?

(Chongani yankho kapena mayankho olondola m’mabokosiwa.)

□ Wodzichepetsa □ Wolapa □ Wodzikweza

2. Kodi wokhometsa msonkhoyo anali munthu wotani?

(Chongani yankho kapena mayankho olondola m’mabokosiwa.)

□ Wodzichepetsa □ Wolapa □ Wodzikweza

3. Kodi ndani pa awiriwa amene anali wolungama kwambiri?

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mufunika kupewa kunena kapena kuchita chiyani kuti musafanane ndi Mfarisi uja? Kodi mungatsanzire bwanji wokhometsa msonkho uja?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

MASAMBA 8 ndi 9 Kodi tsogolo la dzikoli lili m’manja mwa ndani? Yesaya 11: ․․․

TSAMBA 20 Kodi Mulungu amaona bwanji kulambira mafano? Eksodo 20: ․․․

TSAMBA 21 Kodi mtumwi Yohane anachenjeza kuti tifunika kupewa chiyani? 1 Yohane 5: ․․․

TSAMBA 27 Kodi nthawi zina ngakhale munthu wamakhalidwe abwino kwambiri angakhale ndi chiyani? 1 Yohane 2: ․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?

Kuti mupeze yankho, onani pa zokuthandizani. Onaninso malembawo. Kenaka lembani mayina olondola pa mizereyi.

4. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinkatha kunena miyambi zikwi zitatu, ndipo nyimbo zanga “zinali chikwi chimodzi mphambu zisanu.”

Werengani 1 Mafumu 4:30-32.

5. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinali mfumu yomaliza ya ufumu wogwirizana wa Isiraeli.

Werengani 1 Mafumu 12:1-3, 16-20.

6. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Gulu langa la asilikali linagonjetsa gulu lalikulu la asilikali a Yerobiamu chifukwa ‘tinatama Yehova.’

Werengani 2 Mbiri 13:13-20.

▪ Mayankho ali pa tsamba 19

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Wodzikweza.

2. Wodzichepetsa ndi wolapa.

3. Wokhometsa msonkho.

4. Solomo.—Mateyo 1:6.

5. Rehabiamu.—Mateyo 1:7.

6. Abiya.—Mateyo 1:7.