Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndisagonje Poyesedwa?

Kodi Ndingatani Kuti Ndisagonje Poyesedwa?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Ndisagonje Poyesedwa?

Karen wangofika kumene ku phwando ndipo pasanathe mphindi 10, akuona anyamata awiri akufika atanyamula zimapepala zikuluzikulu zingapo. Zimene zili m’mapepalamo n’zodziwikiratu. Asanabwere ku phwandoku, Karen anamva anyamatawo akunena kuti kuphwandoku kukakhala “mowa kutapa kutaya.” Koma Karen sanauze makolo ake zimenezi. Iye anazinamiza kuti anyamatawo amangonena zocheza. Ndiponso iye anaganiza kuti kunyumba kumene kukachitikire phwandoli sikungalephere kupezeka anthu ena achikulire.

Mwadzidzidzi, Karen akumva mnzake akulankhula kumbuyo kwake: “N’chifukwa chiyani wangoima pamenepa, ndiwe wogona eti?” Potembenuka, Karen akuona mnzake Jessica atanyamula mabotolo awiri a mowa, otsegula kale. Ndipo Jessica akumupatsa Karen botolo linalo n’kumuuza kuti, “Usamakhale ngati ndiwe mwana, kumasangalalako nthawi zina!”

Karen akufuna kukana. Koma mosiyana ndi mmene iye amayembekezera, zikumuvuta kukana mowawo. Sikuti iye wakopeka ndi mowawo. Koma kungoti Karen sakufuna kukhumudwitsa mnzakeyo ndiponso sakufuna kuoneka wogona monga mmene Jessica anamutchulira. Ndipotu, Jessica ndi mtsikana wabwino. Ndiye ngati iyeyu akumwa, vuto ndi chiyani? Karen akuganiza kuti, ‘Uwutu ndi mowa chabe, sikuti ndikumwa mankhwala osokoneza bongo kapena kuchita chiwerewere.’

MUNTHU akakhala wachinyamata, amayesedwa m’njira zosiyanasiyana. Nthawi zambiri amayesedwa ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi mnzake. Ramon * wazaka 17 akunena kuti: “Kusukulu, atsikana amachita kukuyamba dala. Amakonda kukugwiragwira kuti aone zimene ungachite. Ndipo ngakhale utawaletsa chotani, iwo samva.” Deanna, yemwenso ali ndi zaka 17, anakumana ndi zofananazi. Iye akuti: “Mnyamata wina anangobwera n’kundikumbatira m’khosi. Ndinamenya mkono wakewo, ndi kum’kalipira kuti, ‘Tandisiye! Sindikukudziwa n’komwe!’”

Inunso mungathe kuyesedwa, ndipo zingaoneke ngati mayeserowo sakutha. Mkhristu wina ananena kuti mayesero ali ngati munthu amene akugogodabe pa chitseko ngakhale kuti inuyo simukumuyankha.” Kodi mumamva kugogoda kotereku mobwerezabwereza? Mwachitsanzo, kodi ndi ziti pa zinthu zotsatirazi zimene zimakuyesani?

□ Kusuta

□ Kumwa mowa

□ Mankhwala osokoneza bongo

□ Kuonera zolaula

□ Kuchita chiwerewere

□ Zinthu zina ․․․․․

Ngati mwapeza chinthu chimene chimakuyesani pa zinthu zimene zili pamwambazi, musafulumire kuganiza kuti mukulephera kukhala Mkhristu. Mungathe kuphunzira kuthetsa zikhumbo zoipa komanso kusagonja poyesedwa. Kodi mungachite motani zimenezi? Choyamba, n’kofunika kudziwa zinthu zimene zimachititsa kuti muziyesedwa. Taonani zinthu zitatu izi.

1. Uchimo. Anthu onse ochimwa amakhala ndi maganizo ofuna kuchita zoipa. Ngakhale mtumwi Paulo, yemwe anali Mkhristu wokhwima mwauzimu anavomereza kuti: “Pamene ndikufuna kuchita chinthu chabwino, choipa chimakhala chili nane.” (Aroma 7:21) Apa zikuonekeratu kuti ngakhale munthu wa makhalidwe abwino kwambiri, nthawi zina angathe kukhala ndi “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso.” (1 Yohane 2:16) Komabe kulakalaka zinthu zimene zimakuyesani n’koopsa, chifukwa Baibulo limati: “Chilakolako chikatenga pathupi, chimabala tchimo.”—Yakobe 1:15.

2. Ziyeso Zochokera Kwina. Ziyeso zili paliponse. Trudy akuti: “Nthawi zambiri anthu kusukulu ndi kuntchito, amangokamba nkhani za kugonana. Pa TV ndi m’mafilimu, amalimbikitsa kugonana ndipo amazionetsa ngati zosangalatsa. Sasonyeza kuipa kwake.” Trudy akudziwa kuti zimenezi zili ndi mphamvu yokopa munthu chifukwa zinamuchitikirapo. Iye akuti: “Ndinali pachibwenzi ndili ndi zaka 16 ndipo ndinkaganiza kuti palibe vuto. Mayi anga anandikhazika pansi n’kundiuza kuti ngati sindisintha, nditenga pathupi. Sindinakhulupirire kuti mayi anga angaganize choncho. Koma patangotha miyezi iwiri, ndinapezeka kuti ndili ndi pathupi.”

3. “Zilakolako za unyamata.” (2 Timoteyo 2:22) Zimenezi zingaphatikizepo chikhumbo chilichonse chimene achinyamata angakhale nacho, monga kufuna kuti anzawo awakonde kapena kudziona kuti akula. Sikuti zikhumbo zimenezi ndi zolakwika, koma akazilekerera zingawapangitse kulephera kulimbana ndi ziyeso. Mwachitsanzo, chifukwa chodziona kuti akula, achinyamata angasiye makhalidwe abwino amene anaphunzitsidwa ndi makolo awo. Izi ndi zimene zinachitikira Steve ali ndi zaka 17. Iye akuti: “Ndinapandukira makolo anga ndipo ndinayamba kuchita chilichonse chomwe anandiphunzitsa kuti ndisamachite, koma zonsezi ndinazichita nditangobatizidwa kumene.”

Kunena zoona, zinthu zitatu zimene zatchulidwa pamwambazi ndi zamphamvu kwambiri. Koma ngakhale zili choncho, mungathe kugonjetsa ziyeso. Motani?

▪ Choyamba, dziwani chiyeso chimene chimakuvutani kwambiri. (Muyenera kuti mwachita kale zimenezi pamwambapa.)

▪ Kenako, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndi nthawi iti imene ndimakonda kukumana ndi chiyeso chimenechi?’ Chongani chimodzi mwa zotsatirazi:

□ Kusukulu

□ Kuntchito

□ Ndikakhala ndekha

□ Zinthu zina

Kudziwa nthawi imene mungakumane ndi chiyeso kungakuthandizeni kupeweratu chiyesocho. Mwachitsanzo, taganizirani chitsanzo chimene chili kumayambiriro kwa nkhani ino. Kodi ndi zizindikiro zotani zimene Karen anaona zosonyeza kuti kuphwandoko zinthu sizikakhala bwino? Kodi iye akanapewa bwanji chiyesocho?

▪ Popeza kuti tsopano (1) mwadziwa chiyesocho ndipo (2) mwadziwa nthawi imene mungakumane nacho, ndinu wokonzeka kuchitapo kanthu. Choyamba, pezani njira imene mungachepetsere chiyesocho kapena kupeweratu kukumana nacho. Lembani pansipa zimene mungachite.

․․․․․

․․․․․

(Zitsanzo: Ngati mukaweruka ku sukulu mumakumana ndi anzanu omwe amakulimbikitsani kusuta, mwina mungasinthe njira yodutsa kuti musamakumane nawo. Ngati nthawi zambiri mumalandira zithunzi zolaula pa Intaneti, mungaganize zoika pulogalamu yoletsa zimenezi kuchitika. Ndiponso, mungafunike kulemba mawu okhawo amene mukufuna kufufuza pa Intaneti.)

Komabe, sikuti mungapeweretu ziyeso zonse. Posapita nthawi, mungadzakumane ndi chiyeso champhamvu kwambiri, mwina musakuyembekezera n’komwe. Kodi mungatani pamenepa?

Khalani okonzeka. Yesu “akuyesedwa ndi Satana,” sanazengereze koma anam’kana nthawi yomweyo. (Maliko 1:13) N’chifukwa chiyani? Iye ankadziwa mbali imene anali. Taganizirani izi: Yesu sanali ngati loboti. Iye akanatha kugonja poyesedwa. Koma anali atasankha kale kumvera Atate ake nthawi zonse. (Yohane 8:28, 29) Sikuti Yesu ankangonena ndi pakamwa pokha pamene anati: “Ndinatsika kuchokera kumwamba kudzachita chifuniro cha iye amene anandituma, osati chifuniro changa.”—Yohane 6:38.

M’mizere ili m’munsiyi, lembani zifukwa ziwiri zimene muyenera kupewera chiyeso chimene mumakumana nacho kawirikawiri, ndiponso zinthu ziwiri zimene mungachite kuti mupewe chiyesocho.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

Kumbukirani kuti mukagonja poyesedwa, mumakhala kapolo wa zikhumbo zanu. (Tito 3:3) Kodi inuyo mungakonde kukhala kapolo wa zikhumbo zanu? Muzichita zinthu ngati munthu wamkulu, osalola zikhumbo zanu kukulamulirani.—Akolose 3:5.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Mayina asinthidwa m’nkhaniyi.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi zolengedwa zopanda uchimo zingayesedwe?—Genesis 6:1-3; Yohane 8:44.

▪ Kodi mukakhalabe okhulupirika poyesedwa, ena zimawakhudza bwanji?—Miyambo 27:11; 1 Timoteyo 4:12.

[Bokosi patsamba 27]

YESANI KUCHITA IZI

Tengani kampasi ndipo iikeni poti muvi wake uloze kumpoto. Kenako, ikani maginito pafupi ndi kampasiyo. Kodi chikuchitika n’chiyani? Muviwo ukusokonekera ndipo ukuloza kolakwika kumene kuli maginitoko.

Chikumbumtima chanu chili ngati kampasi. Ngati chaphunzitsidwa bwino, chimaloza “kumpoto” ndipo chimakuthandizani kusankha zinthu mwanzeru. Koma mayanjano oipa ali ngati maginito ndipo ali ndi mphamvu yosokoneza chikumbumtima chanu. Ndiyeno mukuphunzirapo chiyani pamenepa? Yesetsani kupewa anthu ndi zochitika zomwe zingasokoneze chikumbumtima chanu chophunzitsidwa bwino.—Miyambo 13:20.

[Bokosi patsamba 27]

IZI ZINGAKUTHANDIZENI

Konzani zomwe mungayankhe munthu wina atakunyengererani kuti muchite zoipa. Musade nkhawa. Simungachite kufunikira kulankhula ngati mukudzionetsera. Nthawi zambiri, mungafunike kungokana mwaulemu koma motsimikiza. Mwachitsanzo, ngati mnzanu wakusukulu akukupatsani ndudu, mungamuuze kuti: “Usavutike. Sindisuta fodya!”

[Chithunzi patsamba 28]

Mukagonja poyesedwa, mumakhala kapolo wa zikhumbo zanu