Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Mafano Polambira Mulungu?

Kodi Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Mafano Polambira Mulungu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Tiyenera Kugwiritsa Ntchito Mafano Polambira Mulungu?

“Ndinaphunzitsidwa kuti mafano angandithandize kuyandikana kwambiri ndi Mulungu.”—Mack.

“Nyumba yathu inadzaza ndi zithunzi za oyera mtima. Tinkaganiza kuti zimenezi zingathandize kuti Mulungu azisangalala nafe.”—Herta.

“Tinkagwadira mafano. Ndipo sitinkaganizira n’komwe mmene Mulungu ankaonera zimenezi.”—Sandra.

KODI inuyo mukuganiza bwanji pa zimene anthuwa ananena? Anthu ambiri amakhulupirira kuti mafano amawathandiza polambira Mulungu. Kodi maganizo amenewa ndi olondola? Funso lofunika kwambirinso ndi lakuti, kodi Mulungu amaiona bwanji nkhaniyi? Taonani zimene Mawu ake, Buku Lopatulika, amanena.

Kodi Mulungu Amaona Bwanji Kulambira Mafano?

Mafano ndi zithunzi, zizindikiro kapena chifaniziro chilichonse chimene anthu amachilemekeza kwambiri kapena kuchilambira. Amaphatikizaponso mitanda, ziboliboli, zithunzi kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu zakumwamba kapena zapadziko lapansi. * Mbendera zingathenso kukhala mafano.

Anthu anayamba kugwiritsa ntchito zinthu zimenezi kale kwambiri. N’chifukwa chake mu 1513 B.C.E., popereka Malamulo Khumi ku mtundu wa Isiraeli wongosankhidwa kumene, Mulungu anafotokoza momveka bwino maganizo ake pankhani ya kulambira mafano. Iye anati: “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chilichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo; chifukwa ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje.”—Eksodo 20:4, 5.

Onani kuti m’lembali, Mulungu akuletsa zinthu ziwiri. Choyamba, anthu ake sayenera kupanga mafano. Chachiwiri, sayenera ‘kupembedza,’ kapena kuti kugwadira, ndi kutumikira mafano. N’chifukwa chiyani Mlengi wathu amaletsa kupanga mafano? Chifukwa chimodzi chomwe sitiyenera kupangira mafano oimira Mulungu ndi chakuti, “palibe munthu anaonapo Mulungu ndi kale lonse.” Yehova ndi wosaoneka ndi maso chifukwa iye ndi mzimu ndipo amakhala ku malo a mizimu. (Yohane 1:18; 4:24) Sitiyenera kupanga mafano amtundu uliwonse chifukwa chakuti Mulungu ndi “wansanje.” Iye amati: “Ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.” (Yesaya 42:8) Pachifukwa chimenechi, n’kulakwanso kupanga mafano kuti azitithandiza polambira. Mtsogoleri wa Aisiraeli dzina lake Aroni atapanga fano, Yehova anakwiya kwambiri.—Eksodo 32:4-10.

N’chifukwa Chiyani Sitiyenera Kugwadira Mafano?

Ponena za mafano, Baibulo limati: “Pakamwa ali napo, koma osalankhula; maso ali nawo, koma osapenya; makutu ali nawo, koma osamva.” Ndiyeno limawonjezera chenjezo ili: “Adzafanana nawo iwo akuwapanga,” kutanthauza kuti anthuwo sadzakhalanso ndi moyo.—Salmo 115:4-8.

Ndiponso, kulambira mafano n’kupanda chilungamo. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ineyo ndingamve bwanji ngati nditam’patsa mwana wanga mphatso yamtengo wapatali, iye n’kukathokoza munthu wina, mwinanso chinthu chopanda moyo?’ Zimenezi zingakuthandizeni kumvetsa mmene Mlengi wathu amene anatipatsa moyo amamvera, pamene ulemu ndi kulambira zoyenera kupita kwa iye yekha, zipita kwa anthu kapena ku mafano opanda moyo.—Chivumbulutso 4:11.

Taganiziraninso izi: Anthu anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu. Ndiye akamalambira zinthu zopanda moyo, amadzichotsera ulemu wonse! (Genesis 1:27) Pofotokoza za anthu amene ankalambira mafano, mneneri Yesaya ananena kuti: “Iwo apembedza ntchito ya manja awoawo, imene zala zawozawo zinaipanga. Munthu wachabe agwada pansi, ndi munthu wamkulu adzichepetsa, koma [inu Yehova Mulungu] musawakhululukire.”—Yesaya 2:8, 9.

Chinanso chomwe chimapangitsa kuti Mulungu azinyansidwa kwambiri ndi kupembedza konyengaku ndi chakuti, kwenikweni kumakhala kupembedza ziwanda, zomwe ndi adani a Mulungu. Aisiraeli atasiya Yehova n’kuyamba kupembedza mafano, ‘anaphera nsembe ziwanda, osati Mulungu ayi,’ limatero lemba la Deuteronomo 32:17.

Kodi otsatira a Yesu Khristu akale ankalambira mafano kapena kuwagwiritsa ntchito kuti awathandize polambira? Ayi! Yohane, yemwe anali mtumwi wa Yesu analemba kuti: “Ana apamtima inu, pewani mafano.” (1 Yohane 5:21) Buku lina limati: “Palibe chinthu chimene ophunzira akale ankadana nacho kwambiri kuposa kupembedza mafano.”—Early Church History to the Death of Constantine.

Kulambira Kovomerezeka

Yesu anati: “Olambira oona adzalambira Atate ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:23) Inde, Mulungu amafuna kuti tim’dziwe mmene iye alili, kutanthauza kudziwa zimene amakonda, zimene amadana nazo, malamulo ake ndiponso cholinga chake pa ife. (Yohane 17:3) Ichitu n’chifukwa chake iye analemba Baibulo. (2 Timoteyo 3:16) Komanso popeza kuti Mulungu “sali kutali ndi aliyense wa ife,” tingathe kupemphera kwa iye nthawi iliyonse, paliponse, ndiponso popanda kuthandizidwa ndi mafano.—Machitidwe 17:27.

Sandra, yemwe tam’gwira mawu poyamba uja, anati: “Nditalowa m’Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, sindinaonemo mafano. Mbonizo zinandisonyeza m’Baibulo makhalidwe a Mulungu ndi zimene iye amafuna. Umu ndi mmene ndinadziwira mmene ndingapempherere kuti Mulungu azimva mapemphero anga. Tsopano ndikuona kuti ndikum’dziwa bwino kwambiri Mlengi ndipo iye ndi bwenzi langa lapamtima.” Inde, Sandra anazindikira kuti choonadi cha m’Baibulo chimatsitsimula kwambiri ndiponso chimamasula munthu. (Yohane 8:32) Zimenezi ndi zimene zingakuchitikireni inunso.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 8 Onani nkhani yakuti “Kodi Yesu Anaferadi Pamtanda?” mu Galamukani ya April 2006.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ N’chifukwa chiyani sitiyenera kugwiritsa ntchito mafano amtundu uliwonse polambira?—Salmo 115:4-8; 1 Yohane 5:21.

▪ Kodi Mulungu woona tiyenera kumulambira motani?—Yohane 4:24.

▪ Kodi mungatani kuti mudziwe choonadi cha Mulungu, ndipo chingakuthandizeni bwanji?—Yohane 8:32; 17:3.