Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Tsogolo la Dzikoli Lili M’manja mwa Ndani?

Kodi Tsogolo la Dzikoli Lili M’manja mwa Ndani?

Kodi Tsogolo la Dzikoli Lili M’manja mwa Ndani?

MAGAZINI ya National Geographic ya October 2007 inanena kuti: “Vuto la kutentha kwa dziko limene anthufe tikukumana nalo ndi lalikulu kwambiri ndipo silinachitikepo.” Magaziniyo inanenanso kuti ngati tikufuna kuthetsa vutoli bwinobwino, tifunika “kuchitapo kanthu mwamsanga komanso motsimikiza, ndiponso ndi uchikulire umene anthufe kapena zamoyo ngati ifeyo sitinauonetsepo.”

Koma kodi anthu angathetsedi vutoli mwauchikulire? Pali zinthu zambiri zimene zingalepheretse zimenezi, monga kupanda chidwi kwa anthu, dyera, umbuli, zolinga za mabungwe, kududukira chuma m’mayiko osauka ndiponso maganizo akuti zonse zili bwino, tingozisiya mmene zililimu. Anthu amene amaganiza choncho safuna kusintha moyo wawo umene umawonongetsa zinthu zambiri zachilengedwe.

Pofotokoza mosapsatira mawu ngati anthufe tingathetse mavuto athu a chikhalidwe, moyo komanso okhudza boma, mneneri wa Mulungu kalelo analemba kuti: “Njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Kuyambira kale, mbiri ya anthu yomvetsa chisoni yasonyeza kuti mawuwa ndi oona. Ndipo masiku ano tikukumana ndi mavuto oopsa amene kale sitinkawaganizira. Izi zili choncho ngakhale kuti sayansi ndi luso la zopangapanga lapita patsogolo kwambiri. Ndiyeno tingakhulupirire bwanji kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo?

Kunena zoona, anthu akhala akukambirana zambiri pofuna kuthetsa vuto la kusintha kwa nyengo ndi zizolowezi zina zowononga zachilengedwe, koma palibe zimene achitapo. Mwachitsanzo, kodi mayiko anachita chiyani mu 2007 atamva kuti njira ya panyanja ya Northwest Passage kumpoto kwa dziko lapansi yatseguka kwa nthawi yoyamba, motero kuti sitima za pamadzi zingathe kudutsa? Ndemanga ya m’magazini ya New Scientist inati: “Iwo mopanda manyazi anathamangira kumeneko pofuna kuti madera amenewo akhale awo kuti aziboolako zitsime za mafuta ndi gasi.”

Zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, Baibulo linanena zoona kuti nthawi idzafika pamene anthu adzakhala ‘akuwononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:18) Choncho, n’zosachita kufunsa kuti dzikoli likufunikira mtsogoleri amene ali ndi nzeru ndiponso mphamvu zoti angathe kukwaniritsa zofunika zonse, komanso anthu amene angamumvere. Kodi mtsogoleri wakhama ndi waluso pandale kapena wasayansi angakwanitse zimenezo? Baibulo limayankha kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.”—Salmo 146:3.

Tsogolo la Dzikoli Lili M’manja mwa Mtsogoleri Wodalirika

Pali Mtsogoleri mmodzi yekha amene mosakayikira adzathetsa mavuto onse a dzikoli. Za Mtsogoleri ameneyu, Baibulo linati: “Mzimu wa Yehova [Mulungu] udzam’balira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova . . . Ndi chilungamo adzaweruza aumphawi, . . . nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yake.”—Yesaya 11:2-5.

Kodi pamenepa akunena za mtsogoleri uti? Si wina ayi koma Yesu Khristu, amene potikonda anapereka moyo wake m’malo mwa ife. (Yohane 3:16) Panopa Yesu ndi mngelo wamphamvu, ndipo Mulungu wamupatsa mphamvu ndi udindo wolamulira dziko lapansili.—Danieli 7:13, 14; Chivumbulutso 11:15.

Popeza kuti Yesu amadziwa bwino kwambiri chilengedwe chonse kuyambira kale asanabwere pa dziko lapansi, iye ndi woyenerera kwambiri kukhala mtsogoleri. Pajatu kalekalelo pamene Mulungu anali kulenga kumwamba ndi dziko lapansi, Yesu anali “mmisiri” wake. (Miyambo 8:22-31) Tangoganizani! Yesu, amene anathandiza nawo kupanga dziko lapansi ndi zamoyo zonse, ndi amenenso adzatsogolera ntchito yokonza zonse zimene anthu awononga chifukwa cha kupanda nzeru kwawo.

Nanga kodi Khristuyo adzalamulira anthu otani? Adzalamulira anthu ofatsa ndi olungama amene amadziwadi Yehova, Mulungu woona, ndipo amamvera Yesu Khristu monga Wolamulira. (Salmo 37:11, 29; 2 Atesalonika 1:7, 8) Yesu ananena kuti iwo “adzalandira dziko lapansi,” limene lidzakhala paradaiso.—Mateyo 5:5; Yesaya 11:6-9; Luka 23:43.

Kodi mufunika kuchita chiyani kuti mudzakhalepo pamene malonjezo a m’Baibulowa akukwaniritsidwa? Yesu mwini wakeyo akuyankha kuti: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”—Yohane 17:3.

N’zoona kuti dziko lapansili lingaoneke ngati lili pa mavuto aakulu, koma lidzakhalapobe monga mudzi wa anthufe. M’malomwake, amene ali pa mavuto aakulu ndi anthu amene salemekeza chilengedwe ndiponso safuna kumvera Yesu Khristu, chifukwa iwo adzawonongedwa. Choncho, Mboni za Yehova zikukulimbikitsani kuphunzira choonadi chimene chimatsogolera ku moyo wosatha.

[Bokosi patsamba 8]

SAYANSI SINGATHETSE VUTOLI

Anthu ambiri amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa mwauchidakwa, ndi kusuta fodya, ngakhale kuti amadziwa kuti kuchita zimenezi kungawononge maganizo ndi matupi awo. Iwo saona moyo ngati mphatso yopatulika yochokera kwa Mulungu. (Salmo 36:9; 2 Akorinto 7:1) Chomvetsa chisoni n’chakuti anthu ambiri ali ndi maganizo ngati amenewa osaona dziko lapansi ngati mphatso yopatulika, choncho amawononga zachilengedwe.

Nanga kodi n’chiyani chingathetse vutoli? Kodi ndi sayansi kapena maphunziro? Ayi ndithu. Tikutero chifukwa chakuti vutoli ndi lauzimu, ndipo likufunika kuthetsedwa m’njira yauzimu. Baibulo limasonyezanso zimenezi. N’chifukwa chake limalonjeza kuti nthawi idzafika pamene anthu ‘sadzaipitsa kapena kusakaza’ dziko lapansi popeza kuti dziko “lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.

[Chithunzi patsamba 9]

Muulamuliro wa Khristu anthu olungama adzagwira nawo ntchito yosandutsa dziko lapansi kukhala paradaiso