Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Malangizo Othandiza Kupirira Chisoni

Malangizo Othandiza Kupirira Chisoni

Malangizo Othandiza Kupirira Chisoni

▪ Bambo a mayi wina anamwalira pamene mayiyo anali ndi zaka 12 zokha. Mayiyu analimbana ndi nkhawa komanso kuvutika maganizo kwa zaka zambiri zitachitika izi. M’kalata yake yopita ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Canada, iye anafotokoza kuti:

“Ndinali wachisoni kwambiri mpaka pamene ndinawerenga kabuku kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira ndipo kanandithandiza kupirira chisoni. Ndimalirabe ndikakumbukira bambo anga. Koma ndikangowerenga, kusinkhasinkha, kupemphera ndi kulira powerenga kabukuka ndi malemba ake, chisoni changa chimachepa, ndipo malonjezo a Mulungu amanditonthoza.

“Mawu ndi malemba a m’kabukuka ndimawakonda kwambiri, chifukwa anandithandiza kuumbanso mtima wanga utasweka. Panopa mtima wanga uli m’malo. Ndikuona kuti kabuku kameneka ndi kabwino kwambiri chifukwa kali ndi malangizo othandiza kupirira chisoni.”

Kodi pali munthu yemwe mumamukonda koma anamwalira? Kodi mudakali ndi chisoni? Kodi mukufuna thandizo kuti mulimbane ndi chisoni chanu? Kodi Baibulo limapereka chiyembekezo chotani chokhudza akufa? Mwina inuyo kapena munthu wina amene mukumudziwa angatonthozedwe atawerenga kabuku kamasamba 32 kakuti Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Ngati mukufuna kuitanitsa kabukuka, lembani m’mizere ili pansiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire kabuku kamene kasonyezedwa panoka.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo panyumba kwaulere.