Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Galamukani! Inamuthandiza Mosayembekezera

Galamukani! Inamuthandiza Mosayembekezera

Galamukani! Inamuthandiza Mosayembekezera

YOLEMBEDWA KU BENIN

▪ Mnyamata wazaka 23 dzina lake Noël, atasiya sukulu kuti akhale mlaliki wanthawi zonse wa Mboni za Yehova, achibale ake anakayikira ngati iye angathe kumapeza ndalama zogulira zofunika pamoyo. Ndipo zinalidi zovuta kuti iye apeze ntchito yamaola ochepa imene ikanamulola kulalikira. Choncho, magazini ya Galamukani! itafalitsa nkhani ya panthawi yake, yakuti “Mfundo Zisanu Zomwe Zingakuthandizeni Kupeza Ntchito,” Noël anaiwerenga bwinobwino maulendo angapo. * Kodi inamuthandiza? Inde, koma osati mmene iye anali kuyembekezera.

Mkulu wa sukulu ina imene si yaboma anaona Noël akulalikira nyumba ndi nyumba ndipo anamufunsa ngati anali wa Mboni za Yehova. Mkuluyu ankafuna mphunzitsi winanso pasukulu yakeyo, ndipo popeza anaona kuti Mboni za Yehova zimadziwa kuphunzitsa, anafunsa Noël ngati anali kudziwa winawake amene angafune ntchitoyi. Noël atanena kuti sakudziwa aliyense, mkuluyu anam’funsa kuti: “Nanga bwanji iweyo?”

Noël anali asanagwirepo ntchito ya uphunzitsi, ndipo nthawi zina ankachita chibwibwi. Mkuluyo analonjeza kuti, “Ukapeza satifiketi, udzalembedwa ntchito.” Ku Benin, kukhala ndi chibwibwi ndi vuto chifukwa bungwe loona za maphunziro limafuna kuti aphunzitsi ayesedwe kaye kuti aone ngati alibe vutoli.

Noël anali atapita patsogolo m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, yomwe imachitika mlungu uliwonse m’mipingo ya Mboni za Yehova ndipo cholinga chake ndi kuthandiza anthu kukhala ndi luso lolankhula pagulu. Ndipo ankatha kukamba nkhani za onse mumpingo wakwawo. Komabe anali ndi mantha atapita ku mayeso.

Kumayesoko, anamupatsa magazini n’kumuuza kuti awerenge mokweza ndime imene inali ndi mizere yofiira. Noël anangoti kukamwa yasaa, ataona nkhani ija yakuti “Mfundo Zisanu Zomwe Zingakuthandizeni Kupeza Ntchito.” Iye anawerenga ndimeyo mosachita chibwibwi ndipo analandira satifiketi.

Pambuyo pake, woyesa mayesoyo ananena kuti amakonda kuwerenga magazini a Mboni za Yehova. Iye anafotokoza kuti: “Magazini amenewa amathandiza munthu kudziwa zambiri komanso amalembedwa bwino mwakuti nthawi zambiri ndimawagwiritsa ntchito pamayeso.”

Noël anayamba ntchito ya uphunzitsi, ndipo mkulu wa sukulu uja anamuuza Noël kuti asayiniranenso kuti adzagwirenso ntchito chaka chotsatira. Koma Noël anali ndi zolinga zina. Iye anali ataitanidwa kukagwira ntchito pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova, kumene akugwira ntchito panopa.

[Mawu a M’munsi]