Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Moyo M’Paradaiso

Moyo M’Paradaiso

Moyo M’Paradaiso

YESU analankhula molimba mtima kuti anthu adzakhalanso ndi moyo, ndipo anatsimikizira ophunzira ake kuti zimenezi ndi zoona. Iye anati: ‘Panthawi ya kukonzanso zinthu inu mudzapeza moyo wosatha.’ Kodi Yesu anatanthauza chiyani pamene anati “panthawi ya kukonzanso zinthu”?—Mateyo 19:25-29.

Malinga ndi nkhani imene Luka analemba yofanana ndi imeneyi, Yesu ananena kuti “m’dongosolo la zinthu likubweralo,” ophunzira ake adzalandira “moyo wosatha.” (Luka 18:28-30) Nanga n’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti “dongosolo la zinthu likubweralo” komanso “nthawi ya kukonzanso zinthu” n’chinthu chimodzi?

Zikuoneka kuti limatero pofuna kutsindika mfundo yakuti Yehova Mulungu adzaonetsetsa kuti cholinga chake choyambirira chakuti anthu akhale ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi chakwaniritsidwa. Anthu adzakhala angwiro monga mmene Adamu ndi Hava analili asanachimwe. Choncho, “m’dongosolo la zinthu likubweralo,” padzakhala “nthawi ya kukonzanso zinthu” kuti zikhale mmene zinalili m’Paradaiso wa m’munda wa Edene.

Kodi Paradaiso Adzakhalako Bwanji?

Ali padziko lapansi, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupempherera chida chimene Mulungu adzagwiritsa ntchito kuti akhazikitse chilungamo padziko lonse lapansi. Yesu ananena kuti tizipemphera motere: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mateyo 6:10) Mulungu anasankha Mwana wake kukhala Wolamulira wa Ufumu wake, umene udzakwaniritsa cholinga cha Mulunguyo chakuti dziko lonse lapansi likhale Paradaiso.

Ponena za Munthu yemwe Mulungu wasankha kuti akhale Wolamulira, Baibulo limati: ‘Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake . . . Kalonga wa mtendere. Za kuwonjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.’ (Yesaya 9:6, 7) Koma kodi boma limeneli, pansi pa ‘ulamuliro wa Kalonga,’ lidzachita bwanji chifuniro cha Mulungu?

Baibulo limayankha funsoli, kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu [ulamuliro wa Kalonga] woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.

Tiyeni tione mmene zinthu zidzakhalira padziko lapansi m’Paradaiso, “panthawi ya kukonzanso zinthu,” pamene Mwana wa Mulungu adzalamulira monga “Kalonga” mu Ufumu wa Atate wake.

Mmene Moyo M’Paradaiso Udzakhalira

Akufa adzauka

“Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.

“Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.”—Machitidwe 24:15.

Sikudzakhalanso matenda, ukalamba kapena imfa

“Pamenepo maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilume la wosalankhula lidzaimba.”—Yesaya 35:5, 6.

“Mulungu mwini adzakhala nawo. Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

Kudzakhala chakudya chochuluka

“Dziko lapansi lapereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.”—Salmo 67:6.

“M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.”—Salmo 72:16.

Anthu onse adzakhala ndi nyumba zabwino ndi ntchito zosangalatsa

“Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.”—Yesaya 65:21, 22.

Sikudzakhalanso umbanda, chiwawa kapena nkhondo

“Koma oipa adzalikhidwa m’dziko.”—Miyambo 2:22.

“Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.

Mantha adzatha, ndipo mtendere udzakhala paliponse

“Adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.”—Ezekieli 34:28.

“Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.”—Yesaya 11:9.

Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kukhala ndi moyo pa nthawi imene zinthu padziko lonse lapansi zidzakhala bwino choncho, pamene aliyense adzakonda Mulungu ndi anthu anzake. (Mateyo 22:37-39) Panthawiyo malonjezo onse a Mulungu adzakwaniritsidwa. Ndipo musakayikire zimenezi chifukwa Mulungu akuti: ‘Ndanena, ndidzachichitanso.’—Yesaya 46:11.

Pali zinthu zambiri zokhudza Yehova Mulungu ndi dziko latsopano limene walonjeza zimene mungafunike kuphunzira. Mwachitsanzo, kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti dziko latsopano layandikira kwambiri? Kodi Ufumu wa Mulungu udzachita chiyani kuti ulowe m’malo mwa maboma onse apadziko lapansi? Ndipo kodi usanachite zimenezi, padzachitika zotani? Mboni za Yehova ndi zokonzeka kukuthandizani kupeza mayankho a mafunso amenewa. Mukafuna kudziwa zambiri, onani tsamba 32 m’magazini ino.

Dziko latsopano la chilungamo limene anthu akhala akulakalaka kwa zaka zambiri latsala pang’ono kufika. Kwa anthu ena ambiri amene anamwalira, imfa si mapeto a zonse. N’zotheka iwo kukhalanso ndi moyo, ndipotu ndiye cholinga cha Mulungu. Kunena zoona, amene ali kumanda adzakhalanso ndi moyo. Inde, moyo umene adzakhale nawo ndiwo “moyo weniweniwo,” moyo “umene ukubwerawo.”—1 Timoteyo 4:8; 6:19.

[Chithunzi patsamba 7]

Paradaiso, amene anthu awiri oyambirira anamutaya chifukwa cha kusamvera, adzakhalakonso