Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Anandithandiza Kugonjetsa Mayesero

Mulungu Anandithandiza Kugonjetsa Mayesero

Mulungu Anandithandiza Kugonjetsa Mayesero

Yosimbidwa ndi Vazir Asanov

Ndinamangirira Baibulo pachifuwa changa ndi kuvala mofulumira ndipo kenako ndinadumpha kuchoka pa bedi lomwe ndinagona n’kutulukira pa zenera. Koma ndisanachite zimenezi, ndinamanga zovala zanga ndi kuziika pa bedi bwinobwino n’kuzifundisa bulangete kuti zioneke ngati pali munthu akugona. Nditatuluka, ndinathamangira ku Nyumba ya Ufumu, kwinaku ndikupemphera kwa Mulungu kuti andithandize. Zimenezi zinachitika mu 1991, ndili ndi zaka 14.

NDINABADWIRA m’banja la mtundu wa Kurds, mumzinda womwe uli kum’mwera kwa dziko limene tsopano limatchedwa Kazakhstan. Panthawiyo dzikoli linali m’gulu la mayiko ang’onoang’ono 15 omwe ankapanga dziko la Soviet Union. Makolo ndiponso abale anga, ankandiuza kuti amafuna kuti tsiku lina m’tsogolo ndidzakhale mtsogoleri komanso mpulumutsi wa anthu amtundu wanga. Zimenezi zinachititsa kuti ndikule ndi maganizo odana kwambiri ndi anthu omwe amadana ndi mtundu wathu, moti ndinali wokonzeka kupha anthu amenewa kuti ndipulumutse mtundu wathu umene unali kuponderezedwa.

Chakumapeto kwa zaka za m’ma 1980, ine, mayi anga ndi mng’ono wanga tinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Komabe, bambo anatiletsa kugwirizana ndi Akhristu. Ngakhale zinali choncho, ndinapitirizabe kuphunzira. Mu mtundu wa Kurds, n’zosatheka kuti mwana asamvere bambo ake. Ngakhale kuti ndinkakonda kwambiri bambo anga, ndinkakondanso choonadi cha m’Baibulo chimene ndinali kuphunzira.

Kutsutsidwa Kunyumba ndi Kusukulu

Tsiku lina, aphunzitsi anaona magazini ya Nsanja ya Olonda m’chikwama changa ndipo anakauza makolo anga. Bambo anga anakwiya ndipo anandimenya kwambiri mpaka ndinatuluka magazi mphuno. Iwo anakalipa kuti: “Kodi ukupitirizabe chipembedzo chako chija?”

Zitachitika izi, bambo anga anauza banja lathu lonse kuti sindinenso mwana wawo. Zinandiwawa kwambiri kumva zimenezi. Anzanganso ambiri kusukulu anayamba kundisala, ndipo ena mwa iwo ankachita kundinyoza poyera. Aphunzitsi ankandichotsera malikisi ndipo nthawi zambiri ankanyoza chipembedzo changa m’kalasi. Ankachita zimenezi pofuna kuti ndisiye chipembedzo changa n’kutengera maganizo awo akuti kulibe Mulungu.

Ngakhale kuti ndinkatsutsidwa chonchi, ndinkayesetsa kupita ku misonkhano yachikhristu ndi kuuza ena za chipembedzo changa chatsopanocho. Pasanapite nthawi, bambo anadziwa kuti sindinasiye kugwirizana ndi Mboni ndiponso kuwerenga Baibulo. Tsiku lina Lamlungu, ndinayesa kupeza njira yochokera panyumba kuti ndipite ku misonkhano. Nthawi yomweyo bambo anandilamula kuti ndikagone. Iwo ananena mwamphamvu kuti: “Kuyambira lero, Lamlungu lililonse nthawi ngati ino uzikhala utagona.” Iwo anandichenjeza kuti ngati sindimvera adzandikhaulitsa, ndipo sindinakayikire zimenezi.

Ndikulira, ndinachonderera Yehova, Mulungu woona, kuti afewetse mtima wa bambo, koma iwo anauma mtima ndipo sanafune kusintha. Ndinakumbukira kuzunzika kwa Aisiraeli ku Iguputo. Zochita za bambo zinandikumbutsa za Farao, amene sanalole Aisiraeli kupita kukapembedza Yehova.—Eksodo 5:1, 2.

Kusankha Zochita

Tsiku lina Lamlungu, ndinaganiza zopita ku msonkhano. Nditagona pa bedi, mtima wanga unali kugunda chifukwa cha mantha kwinaku ndikupemphera kwa Yehova chamumtima. Bambo ndi mayi atalowa m’chipinda changa, ndinanamizira kugona tulo. Bambo ananena monyadira kuti: “Taona, mwana wanga ndi womvera.” Anandipsompsona ndipo kenako anatuluka mwakachetechete. Ndipo ine ndinapitiriza kupemphera ndi mtima wonse.

Bambo ndi mayi atangochoka m’chipinda changacho, ndinanyamuka n’kutenga nsapato kunsi kwa bedi ndi kudumphira pa zenera, monga ndafotokozera poyamba paja. Maola awiri amene ndinali ku msonkhano anadutsa mofulumira, ndipo sindinadziwe kuti ndikapita kunyumba chikachitike n’chiyani. Mayi anadziwa kuti zimene zinali pa bedipo ndi zovala zanga osati ineyo, koma mwamwayi sanauze bambo. Komabe anandichenjeza kuti ndikadzachitanso zimenezi, iwo adzanena kwa bambo.

Mu 1992, ndinauza mayi ndi bambo kuti mnzanga wina akupita ku mwambo wapadera ndipo wandipempha kuti ndipite naye. Koma pansi pa mtima, ndinkadziwa kuti mwambo wapaderawo unali msonkhano wa Mboni za Yehova womwe unachitikira mu mzinda wa Taraz, pamtunda wa makilomita 100 kuchokera kwathu ku Karatau. Ndinali kukabatizidwa kumsonkhanowu posonyeza kudzipereka kwanga kwa Yehova. Ndinapempha mayi kuti nditenge chidebe chimodzi cha mbewu ya mpendadzuwa mu nkhokwe. Atandiloleza, ndinakazinga mbewuzo ndi kukazigulitsa ku msika. Umu ndi mmene ndinapezera ndalama zokwanira zopitira ku msonkhano.

Nditabwerako, bambo anandifunsa ngati ndinasangalala limodzi ndi mnzangayo, ndipo ine ndinavomera. Ndinaona kuti Yehova wandithandiza, chifukwa bambo sanandifunsenso za nkhaniyi. Choncho, ndinakonda kwambiri mawu a pa Miyambo 3:5, 6, akuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.”

Ndinafooka Mwauzimu

Nditabatizidwa, bambo sanasiye kunditsutsa. Chifukwa choti ndinapitiriza kugwirizana ndi Mboni, iwo ankandimenya koopsa, pagulu komanso tikakhala patokha. Pafupifupi tsiku lililonse, ndinkanyozedwa ndiponso kukakamizidwa kuti ndisiye chipembedzo changa, moti nthawi zambiri ndinkakhalira kulira. Panthawiyi n’kuti dziko la Kazakhstan litatsala pang’ono kulandira ufulu wodzilamulira, kuchoka mu Soviet Union. Mayi ndi bambo komanso achibale ena, anayesetsa kundilimbikitsa kuti ndingachite bwino kwambiri nditalowa ndale. Iwo ankaganiza kuti ndikutaya mwayi.

Mkulu wanga anali atachita zambiri pa zamasewera, ndipo bambo ankanena kuti nditsatire chitsanzo chake. N’zomvetsa chisoni kuti chakumapeto kwa 1994 inenso ndinayamba kuchita nawo masewera osiyanasiyana. Popeza ndine waluso mwachibadwa, posapita nthawi ndinayamba kulandira mphoto pa masewera monga mpira wamiyendo ndi masewera ena olimbitsa thupi, ndipo ndinatchuka. Ndinayambanso kuphunzira za malamulo n’cholinga chakuti ndithandize kuteteza mtundu wathu wa Kurds. Mpaka ndinalowa ndale ndipo ndinaganiza zoyambitsa chipani cha achinyamata a mtundu wathu wa Kurds. Bambo ataona zimenezi, anayamba kunditamanda.

“Bambo, Munapambana”

Ndinali nditafooka mwauzimu ndipo ndinasiyiratu kuwerenga Baibulo komanso kupita ku misonkhano ya Mboni za Yehova. Ndinkadzilimbitsa mtima ndi maganizo akuti ndidzayambanso kutumikira Yehova ndikakula. Tsiku lina, bambo anandifunsa ngati ndinali kugwirizanabe ndi Mboni za Yehova. Poyankha ndinati: “Ayi. Bambo, munapambana. Ndikukhulupirira kuti mukusangalala tsopano, si choncho?” Bambo atamva zimenezi, anasangalala kwambiri ndipo monyadira anati: “Tsopano ndiwe mwana wanga.”

Ndinakhala zaka ziwiri osapita ku misonkhano. Nthawi zina ndinkafuna kupita, koma ndinkachita manyazi chifukwa ndinkaganiza kuti anthu kumpingoko sangamvetse chifukwa chimene ndinasiyira kusonkhana.

Komabe, ndinkadziwa kuti palibe chinthu chabwino kwambiri kuposa kutumikira Yehova. Pansi pa mtima ndinkadziuza kuti, ‘Ndimakonda Yehova.’ Kenako bambo anayamba kundikakamiza kupita ku yunivesite kuti ndikapeze maphunziro apamwamba. Ndinavomereza ndipo ndinawalonjeza kuti ndikachita bwino pamaphunzirowo. Komabe, mumtima mwanga ndinkaganiza kuti ndikangopita ku yunivesite ku Almaty, mzinda waukulu ndiponso wamakono umene uli kum’mwera kwa dziko la Kazakhstan, ndikapeza a Mboni.

Zinthu Zikhalanso Bwino

Pasanapite nthawi yaitali ndikuphunzira pa yunivesiteyo, ndinakumana ndi anthu awiri a Mboni akulalikira mumsewu wina ku Almaty. Iwo anandifunsa kuti: “Kodi mukuganiza kuti akulamulira dzikoli ndani?”

Ndinayankha kuti: “Satana Mdyerekezi, mdani wa Yehova ndi anthu onse.” (2 Akorinto 4:3, 4) Kenako ndinawafotokozera kuti ndine Mboni yobatizidwa koma ndinasiya kusonkhana.

Chakumapeto kwa chaka cha 1996, ndinayambanso kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Nditaphunzira maulendo angapo, ndinayambanso kuganizira kwambiri zotumikira Yehova, ndipo ndinayamba kuchita ntchito zonse zachikhristu limodzi ndi Mboni za ku Almaty. Mu September 1997, ndinayamba kutumikira monga mpainiya, kapena kuti mlaliki wa nthawi zonse.

M’chaka chotsatira, bambo anabwera kudzandiona. Nditawaona ndinawathamangira, ndipo tinakumbatirana. Anandipempha kuti ndiwakhululukire chifukwa cha zochita zawo m’zaka zonse za m’mbuyomo. Anandiuza kuti sankandimvetsa ndiponso sankamvetsa chipembedzo changa. Ndinawauza kuti: “Bambo, ndimakukondani kwambiri.”

Ndinasangalala kwambiri bambo atalandira mabuku ofotokoza Baibulo komanso atapempha Baibulo, ndi kunena kuti akufuna kukaliwerenga lonse. Patatha chaka, anabweranso kudzandiona ndipo panthawiyi anali limodzi ndi mayi. Titapita ku Nyumba ya Ufumu, anthu amitundu yosiyanasiyana anabwera kudzawapatsa moni mosangalala ndi kuwauza mayina awo. Bambo anachita chidwi kwambiri ndi zimenezi, moti anayamba kukonda kwambiri kuwerenga mabuku a Mboni.

Madalitso Aakulu

Mu September 2001, ndinakwatira Yelena, mtsikana wabwino kwambiri wa ku Russia. Iye anabatizidwa n’kukhala wa Mboni m’chaka cha 1997 ndipo anayamba upainiya mu May 2003. Tinasangalala kwambiri titamva kuti makolo anga anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni ndipo akuchita bwino kwambiri. Kunena zoona, sindinakhulupirire zimenezi mpaka pamene bambo anandiuza okha. Iwo anandiuza pa telefoni kuti Yehova ndi Mulungu yekhayo woona.

Ndine wosangalala kwambiri kuti kuno ku Almaty ndakhala ndi mwayi wochititsa maphunziro a Baibulo kwa anthu ochokera m’madera osiyanasiyana, monga China, Iran, Pakistan, Syria ndi Turkey. Chaposachedwapa, wansembe wina wa ku Iran anandipempha kuti ndiziphunzira naye Baibulo m’Chiperisiya, chomwe ndi chilankhulo chake. Munthu winanso amene anali mkulu wa asilikali ku Afghanistan anachita chidwi kwambiri ndi zimene anaphunzira zokhudza Yehova. Ndinalinso wosangalala kuphunzira ndi munthu wa ku Syria m’chilankhulo changa cha Chikudishi, komanso kuphunzira ndi anthu m’zilankhulo za Chikazakhi ndi Chirasha, zomwe ndinaphunzira ndili mwana.

Panopa, ine ndi Yelena tikutumikira mu mpingo wina wa chinenero cha Chikazakhi ndipo ndi umodzi mwa mipingo yoposa 35 ya Mboni za Yehova ku Almaty. Chaka chatha, ine ndi Yelena tinali ndi mwayi wogwira ntchito kwa nthawi yochepa pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova imene yangomalizidwa kumene ndipo ili pafupi ndi mzinda wa Almaty.

Kale ndinaphunzitsidwa kudana ndi anthu, koma Yehova anandiphunzitsa kukonda anthu onse. Ndaphunzira kuti sitiyenera kusiya kukonda Yehova, ngakhale achibale ndi anzathu amene angaoneke kuti akutifunira zabwino, atatikakamiza kutero. (Agalatiya 6:9) Tsopano ndine wosangalala kuti ine ndi mkazi wanga tili ndi “zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye.”—1 Akorinto 15:58.

[Mawu Otsindika patsamba 13]

Mayi anandichenjeza kuti ndikadzachitanso zimenezi, iwo adzanena kwa bambo

[Chithunzi patsamba 15]

Nyumba ya Ufumu ku Karatau, kumene ndinkasonkhana ndili wamng’ono

[Chithunzi patsamba 15]

Makolo anga, omwe tsopano satsutsa ntchito yathu

[Chithunzi patsamba 15]

Ine ndi Yelena, patsiku la ukwati wathu

[Chithunzi patsamba 15]

Ine ndi Yelena, pa ofesi ya nthambi yatsopano pafupi ndi ku Almaty