Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Angachite

Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Angachite

Ana Akamagwiritsa Ntchito Intaneti Zimene Makolo Angachite

MONGA kholo, kodi n’chiyani chingakudetseni nkhawa kwambiri pa ziwirizi: Kudziwa kuti mwana wanu watenga makiyi a galimoto yanu, kapena kudziwa kuti ali ndi mwayi wogwiritsa ntchito Intaneti mmene angafunire? Ziwiri zonsezi zikhoza kukhala zoopsa. Ndiponso zonsezi zimafuna kusamala. Makolo sangaletseretu ana awo kuyendetsa galimoto, koma angaonetsetse kuti ana awo aphunzitsidwa kuyendetsa galimoto mosamala. Makolo ambiri amachitanso zimenezi pankhani ya Intaneti. Mfundo za m’Baibulo zotsatirazi zikuthandizani.

“Yense wochenjera amachita mwanzeru.” (Miyambo 13:16) Makolo amene ana awo amagwiritsa ntchito Intaneti, amafunika kudziwako zina ndi zina za mmene Intaneti imagwirira ntchito ndi zimene ana awo amachita akamacheza, kuwerenga, kapena kuchita zinthu zina pa Intaneti. Mayi wina wa ana awiri, dzina lake Marshay, anati: “Musaganize kuti mwakula kwambiri moti simungaphunzire. Musatsalire m’mbuyo pankhani ya Intaneti.”

‘Muzimanga kampanda pa tsindwi kuti asagweko munthu.’ (Deuteronomo 22:8) Makampani a Intaneti komanso mapulogalamu ena a pakompyuta amatha kukhala ndi njira zotetezera zimene zili ngati “kampanda” koletsa zinthu zoipa zobwera mwadzidzidzi ndiponso koletsa ana kutsegula malo olakwika. Mapulogalamu ena amathanso kuletsa ana kuulula zinthu zokhudza iwowo, monga mayina kapena maadiresi awo. Koma dziwani kuti mapulogalamu amenewa salepheretsa zinthu zonse zolakwika. Ndiponso, ana akuluakulu odziwa za makompyuta amatha kuphunzira njira zozembera mapulogalamu amenewa mpaka kupeza zomwe akufuna.

“Amene amakhala pa yekha, angofuna kudzaza zilakolako zake, napsa mtima pakumva malangizo abwino alionse.” (Miyambo 18:1, Malembo Oyera) Pakafukufuku yemwe anachitika ku United Kingdom, anapeza kuti pafupifupi mwana mmodzi pa ana asanu alionse azaka za pakati pa 9 ndi 19 ali ndi Intaneti kuchipinda kwake. Kuika kompyuta pamalo oonekera kumathandiza makolo kudziwa zimene ana awo akuchita pa Intaneti ndipo zingathandize ana kupewa kutsegula malo olakwika.

“Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru, podziwombolera nthawi yoyenerera chifukwa masikuwa ndi oipa.” (Aefeso 5:15, 16) Ikani masiku amene ana azigwiritsa ntchito Intaneti, nthawi imene ayenera kuthera pa Intaneti, ndiponso malo oyenera ndi osayenera kutsegula. Kambiranani malangizo anu ndi anawo, ndipo onetsetsani kuti amvetsa bwino.

Komatu simungaone zimene ana anu amachita akachoka pa nyumba. Choncho, mufunika kuphunzitsa ana anu mfundo zabwino kuti azisankha zinthu mwanzeru akakhala kwaokha. * (Afilipi 2:12) Auzeni momveka bwino zotsatira zake ngati iwo aphwanya malamulo anu okhudza Intaneti. Ndipo akaphwanya malamulowo musazengereze kupereka chilango.

“[Mayi wabwino] ayang’anira mayendedwe a banja lake.” (Miyambo 31:27) Muziona mmene ana anu akugwiritsira ntchito Intaneti, ndipo adziwitseni kuti muzitero nthawi zonse. Kuchita zimenezi sikuona zinsinsi za ena. Kumbukirani kuti Intaneti ndi ya aliyense. Bungwe la ku United States la Federal Bureau of Investigation, limati ndi bwino kuti makolo azipitiriza kuona mmene ana akugwiritsira ntchito Intaneti ndiponso kuona maimelo ndi ma Web site amene anatsegula, popanda kuwauziratu.

“Kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza; kukupulumutsa ku njira yoipa, kwa anthu onena zokhota.” (Miyambo 2:11, 12) Kuyang’anira ana kuti mudziwe zimene akuchita kuli ndi malire ake. Koma mfundo zimene mumawaphunzitsa ndi chitsanzo chanu chabwino zingathandize kwambiri kuteteza ana anu. Choncho, muzikhala ndi nthawi yokambirana ndi ana anu za mavuto amene angakumane nawo pa Intaneti. Kulankhulana ndi ana anu momasuka ndiyo njira yabwino kwambiri yowatetezera ku mavuto a pa Intaneti. Bambo wina wachikhristu dzina lake Tom, anati: “Tinakambirana ndi ana athu aamuna awiri za anthu oipa amene amapezeka pa Intaneti. Tinawafotokozeranso kuti zolaula ndi chiyani, chifukwa chake ayenera kuzipewa, ndiponso chifukwa chake sayenera kulankhula ndi anthu osawadziwa.”

Mungateteze Ana Anu

Kuteteza ana anu ku mavuto a pa Intaneti kumafuna khama, ndipotu njira zogwiritsira ntchito Intaneti zikusintha tsiku ndi tsiku. Luso latsopano lingakhale ndi ubwino wake komanso mavuto amene ana sanakumanepo nawo. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukonzekera mavuto amene angabwere m’tsogolo? Baibulo limati: “Nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza.”—Mlaliki 7:12.

Thandizani ana anu kukhala anzeru. Athandizeninso kudziwa mmene angapewere mavuto a pa Intaneti ndiponso kudziwa kuigwiritsa ntchito mwanzeru. Mukatero, Intaneti idzakhala chida chomwe sichingaike pa ngozi ana anu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Makolo ayenera kukumbukira kuti ana ambiri amatha kugwiritsa ntchito Intaneti kudzera pa foni za m’manja, zipangizo zina za m’manja, ngakhalenso zipangizo zosewerera magemu apavidiyo.

[Mawu Otsindika patsamba 8]

Ku United Kingdom, 57 peresenti ya ana azaka za pakati pa 9 ndi 19 amene amagwiritsa ntchito Intaneti mlungu uliwonse aonerapo zinthu zolaula. Koma 16 peresenti yokha ya makolo ndi imene imakhulupirira kuti ana awo aonerapo zolaula pa Intaneti

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Akatswiri akukhulupirira kuti anthu pafupifupi 750,000 ogona ana amakhala pa Intaneti tsiku ndi tsiku, akufufuza m’malo ochezera a pa Intaneti ndiponso m’masamba othandiza anthu kupeza zibwenzi

[Mawu Otsindika patsamba 9]

Ku United States, 93 peresenti ya ana azaka za pakati pa 12 ndi 17 amagwiritsa ntchito Intaneti

[Chithunzi patsamba 8, 9]

Kodi mungaphunzitse mwana wanu kugwiritsa ntchito Intaneti mosamala?