Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Aphunzitsi Ake Analiyamikira

Aphunzitsi Ake Analiyamikira

Aphunzitsi Ake Analiyamikira

▪ Kodi achinyamata angapeze kuti nzeru ndi malangizo odalirika? Mtsikana wina wa ku Italy wazaka 13, dzina lake Cheren, anasangalala kwambiri atawerenga buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Posachedwapa, iye anali ndi mpata wouzako anzake a m’kalasi mfundo zosangalatsa zimene anawerengazo.

Iye anati: “Ndine wasitandade 8, ndipo m’kalasi mwathu tinkakambirana za mavuto amene achinyamata amakumana nawo. Tsiku lina aphunzitsi anandiuza kuti anamva zakuti mabuku athu amakhala ndi mfundo zothandiza achinyamata. Anandipempha kuti ndiwapezere mabuku ena ndipo ndinawapatsa buku la Achichepere Akufunsa.

“Patapita masiku angapo, aphunzitsi anagwiritsa ntchito bukulo pophunzitsa ndipo tinakambirana mutu 10 wakuti, ‘Kodi Mawonekedwe Ngofunika Motani?’ Iwo anatipatsanso homuweki pogwiritsa ntchito kamutu kakuti ‘Mafunso a Kukambitsirana’ kamene kali kumapeto kwa mutuwu. Iwo anati: ‘Buku limeneli linalembedwa bwino kwambiri, ndipo n’zomvetsa chisoni kuti nonse mulibe.’

“Ndinawauza kuti nditha kubweretsa mabuku kwa onse amene akufuna, ndipo anzanga 16 anapempha kuti ndiwabweretsere. Nditabweretsa mabukuwo, ngakhale ophunzira amene poyamba ananena kuti sakuwafuna anasintha maganizo n’kundiuza kuti iwonso akufuna.”

Buku la Achichepere Akufunsa lilinso ndi mitu ina monga “Kodi Nchifukwa Ninji Ndimachita Tondovi Kwambiri?,” “Kodi Ndingadziŵe Motani Ngati Chiri Chikondi Chenicheni?,” “Kodi Nkuneneranji Kuti Ayi ku Mankhwala Oledzeretsa?,” ndi “Kodi Ndingalamulire Motani Zizolowezi Zanga za Kuwonerera TV?” Ngati mukufuna kuitanitsa bukuli, lembani m’mizere ili pansiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire buku limene lasonyezedwa panoli.

□ Lembani chinenero chimene mukufuna.