Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Ndi Wotani?

Kodi Mulungu Ndi Wotani?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Ndi Wotani?

BAIBULO limati: “Mulungu ndiye Mzimu, ndipo onse omulambira ayenera kumulambira ndi mzimu ndi choonadi.” Mawu amenewa akufotokoza mfundo yosavuta kumva ya mmene Mulungu alili. Iye ndi mzimu. (Yohane 4:19-24) Ngakhale zili choncho, Baibulo limamufotokozanso ngati munthu. Iye dzina lake ndi Yehova.—Salmo 83:18.

Anthu ena owerenga Baibulo amati nkhani ya mmene Mulungu alili imawasokoneza kwambiri. Popeza kuti Mulungu ndi mzimu ndipo saoneka, komanso alibe thupi ngati la anthu, n’chifukwa chiyani mavesi ambiri m’Baibulo amanena ngati kuti Mulungu ali ndi maso, makutu, mphuno, mtima, mikono, manja, zala ndi mapazi? * Ena angaganize kuti Mulungu ali ndi thupi ngati la anthu chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu. Kuona bwino zimene Baibulo limanena kungathetse maganizo olakwika amenewo.—Genesis 1:26.

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amafotokozedwa Ngati Munthu?

Pofuna kuthandiza anthu kumvetsa mmene Mulungu alili, olemba Baibulo anauziridwa kufotokoza Mulungu Wamphamvuyonse ngati munthu. Kumufotokoza Mulungu ngati munthu kumasonyeza kuperewera kwa chinenero cha anthu pofotokoza bwinobwino mmene Yehova, Mulungu woona, alili. Anachita zimenezi kuti apereke chithunzi cha zinthu zakumwamba ndi kuzifotokoza mwanjira imene anthu angathe kumvetsa bwino. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti mawuwo tiziwatenga mmene alili. Mwachitsanzo, mawu a m’Baibulo onena za Mulungu akuti iye ndi “Thanthwe,” “dzuwa” ndi “chikopa,” sitiwatenga mmene alili.—Deuteronomo 32:4; Salmo 84:11.

Mofanana ndi zimenezi, pofuna kunena mfundo yakuti munthu mwapang’ono chabe ali ndi makhalidwe ngati amene Yehova ali nawo mopanda malire, Baibulo limanena kuti munthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu. Apa n’zoonekeratu kuti Baibulo silitanthauza kuti anthu ndi mizimu kapenanso kuti Mulungu ali ndi thupi ngati la anthu.

Kodi Mulungu Ndi Mwamuna Kapena Mkazi?

Monga taonera kuti mawu ofotokoza Mulungu ngati munthu sitiyenera kuwatenga mmene alili, mawu amene amafotokoza Mulungu ngati mwamuna sitiyeneranso kuwatenga mmene alili. Zolengedwa zimene timaziona ndi zimene timasiyanitsa kuti ichi n’chachimuna, ichi n’chachikazi. N’chifukwa chake zinenero za anthu sizitha kufotokoza bwinobwino mmene Yehova, Mulungu Wamphamvuyonse, alili.

Pogwiritsa ntchito dzina lakuti “Atate,” Baibulo limatithandiza kumvetsa kuti Mlengi wathu ali ngati tate waumunthu amene amatikonda, kutiteteza ndi kutisamalira. (Mateyo 6:9) Choncho, sizikutanthauza kuti tiyenera kuona Mulungu, kapena zolengedwa zauzimu kumwamba, monga amuna kapena akazi. Pachikhalidwe chawo, palibe mtundu monga chachimuna kapena chachikazi. Ndipotu Baibulo limanena kuti anthu oitanidwa kukalamulira limodzi ndi Khristu mu Ufumu wakumwamba, sadzakhalanso amuna kapena akazi akadzalandira ulemerero wokhala ana auzimu a Mulungu. Mtumwi Paulo anawakumbutsa anthu amenewa kuti sipadzakhala “mwamuna kapena mkazi” pakati pawo, iwo akadzalandira ulemerero wokhala ana auzimu a Mulungu. Iwo amafotokozedwanso mophiphiritsa kuti ndiwo “mkwatibwi” wa Mwanawankhosa, Yesu Khristu. Zonsezi zikusonyeza kuti mawu ofotokoza Mulungu, Mwana wake wobadwa yekha Yesu, ndiponso zolengedwa zina zauzimu ngati anthu, sayenera kutengedwa mmene alili.—Agalatiya 3:26, 28; Chivumbulutso 21:9; 1 Yohane 3:1, 2.

Pomvetsa udindo wa mwamuna, olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu osonyeza chachimuna pofotokoza Mulungu. Poona mwamuna amene amakwaniritsa bwino udindo wake, olembawo anazindikira kuti mwamuna wotero ndi chithunzi chabwino cha Yehova, amene ngati tate, amakonda ana ake apadziko lapansi.—Malaki 3:17; Mateyo 5:45; Luka 11:11-13.

Khalidwe Lalikulu la Mulungu

Ngakhale kuti Mfumu ya chilengedwe chonse imeneyi ndi mzimu, iyo siidzikweza, si yobisika kapena yosalankhulika. Kukhala kwake mzimu sikulepheretsa anthu amtima wabwino kudziwa ndi kumvetsa chikondi chake, mphamvu zake, nzeru zake ndi chilungamo chake. Makhalidwe amenewa amasonyeza mmene iye alili ndipo amaonekera m’chilengedwe.—Aroma 1:19-21.

Khalidwe lalikulu limene limafotokoza bwino mmene Mulungu alili ndilo chikondi. Chikondi chake n’chapadera kwambiri mwakuti iye amanenedwa kuti ndiye chikondicho. (1 Yohane 4:8) Khalidwe limeneli limalamulira makhalidwe ake ena monga chifundo, kukhululuka ndi kuleza mtima. (Eksodo 34:6; Salmo 103:8-14; Yesaya 55:7; Aroma 5:8) Yehova ndi Mulungudi wachikondi ndipo amafuna kuti anthufe timuyandikire.—Yohane 4:23.

[Mawu a M’munsi]

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi Mulungu dzina lake ndani?—Salmo 83:18.

▪ Kodi makhalidwe a Mulungu tingawaone m’zinthu ziti?—Aroma 1:19-21.

▪ Kodi khalidwe lalikulu la Mulungu ndi lotani?—1 Yohane 4:8.