Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nthawi Yofikira Panyumba Ndiziiona Bwanji?

Kodi Nthawi Yofikira Panyumba Ndiziiona Bwanji?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Nthawi Yofikira Panyumba Ndiziiona Bwanji?

Munali kokacheza ndi anzanu ndiye mukufika panyumba mochedwa kwambiri usiku. Nthawi yofikira panyumba yadutsa kalekale. Muli ndi nkhawa kuti muwauza chiyani makolo anu. Mukuimirira kaye panja. Kenako maganizo akukupezani akuti, ‘Mwina bambo ndi mayi agona kalekale.’ Mukuyesa kutsegula chitseko pang’onopang’ono. Ndiyeno mutangolowa, mukuona kuti iwo akukudikirirani kwinaku akuyang’ana nthawi. Akuyembekeza kuti muwauze kumene munali.

KODI tafotokozazi zinakuchitikirani? Kodi inu ndi makolo anu mumangokhalira kukangana za nthawi yabwino yofikira panyumba? Mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Debora, anati: “Timakhala dera losaopsa, koma sindingakacheze ndi anzanga mpaka pakati pa usiku popanda makolo anga kuda nkhawa.” *

N’chifukwa chiyani kusunga nthawi yofikira panyumba kumakhala kovuta? Kodi kufuna ufulu n’kulakwa? Kodi mungatani kuti muzikwanitsa kusunga nthawiyo ngakhale ngati ili yopanikiza?

Achinyamata Amavutika

Nthawi yofikira panyumba imakhumudwitsa kwambiri, makamaka ngati ikuoneka kuti ikukulandani ufulu wocheza ndi anzanu. Mtsikana wazaka 17, dzina lake Natasha, anati: “Ndikaganiza za nthawi yofikira panyumba, zimandipweteka kwambiri. Tsiku lina bambo ndi mayi anali kudziwa kuti ndikuonera filimu ndi anzanga pafupi ndi nyumba yathu. Koma nditangochedwa ndi mphindi ziwiri zokha, iwo anandiimbira foni ndi kundifunsa kuti n’chifukwa chiyani sindinafike kunyumba.”

Mtsikana wina, dzina lake Stacy, anatchulanso vuto lina. Iye anati: “Mayi ndi bambo ankafuna kuti ndizifika panyumba iwo asanagone. Ndikachedwa, ndinkapeza akundidikirira, atatopa kotheratu.” Ndiyeno zinali kutha bwanji? “Iwo ankandiimba mlandu wowavutitsa,” anatero Stacy, ndipo anapitiriza kuti: “Zinali zokhumudwitsa kwambiri. Sindinali kumvetsa chifukwa chimene iwo ankandiyembekezera m’malo mopita kukagona.” Kusagwirizana kotere ndi makolo anu kungakuchititseni kukhala ndi maganizo ngati a mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Katie. Iye anati: “Ndingakonde kuti makolo anga azindipatsa ufulu wokwanira, kuti ndisamaone ngati ndikulimbana nawo kuti andipatse ufuluwo.”

Mwina inu mukugwirizana ndi zimene achinyamatawa akunena. Ngati zili choncho, dzifunseni funso ili:

N’chifukwa chiyani ndimakonda kuchoka panyumba? (Chongani chimodzi.)

□ Zimandipatsa ufulu.

□ Zimandithandiza kukhala wosangalala.

□ Zimandipatsa mpata wocheza ndi anzanga.

Zifukwa zimenezi ndi zabwinobwino. N’chibadwa munthu kufuna ufulu ukamakula, ndipo masewera abwino amasangalatsa. Pajanso Baibulo limalimbikitsa achinyamata kukhala ndi mabwenzi abwino. (Salmo 119:63; 2 Timoteyo 2:22) Koma zimenezi zingakhale zovuta ngati mumakhala panyumba nthawi zonse.

Koma kodi mungatani kuti mupeze ufuluwo pamene akukukhwimitsirani nthawi yofikira panyumba? Taonani zotsatirazi.

Vuto loyamba: Ukamafika msanga panyumba umadziona ngati ndiwe kamwana. “Ndinkadziona ngati kamwana ndikamadodometsa aliyense pofuna kuti wina andiperekeze kunyumba nthawi yabwino,” anatero Andrea, wazaka 21.

Zimene zingathandize: Tiyerekeze kuti ndi nthawi yoyamba kutenga laisensi ya galimoto. M’madera ena, malamulo amaika malire a kumene mungapite, nthawi imene mungapite, kapena anthu amene mungayende nawo pagalimoto, mpaka mutakwanitsa zaka zoyenerera. Kodi mungaganize zosatenga laisensiyo, n’kunena kuti, “Ngati sakundipatsa ufulu wonse, basi sindidzayendetsanso galimoto”? Simungatero ngakhale pang’ono. Mudzaona kuti ndi mwayi waukulu kutenga laisensi.

Mofanana ndi zimenezi, yesetsani kuona nthawi yofikira panyumba ngati umboni wakuti mukukula n’kukhala ndi udindo. Ganizirani kwambiri za ufulu umene nthawiyo imakupatsani, osati malire amene imakuikirani. Kodi panopa simuli ndi ufulu woposa umene munali nawo muli mwana?

Chifukwa chake zimathandiza: Sizivuta kuvomereza nthawi yofikira panyumba mukamaiona ngati mpata wosonyeza mmene inu mulili, osati ngati chokulandani ufulu wanu. Ngati panopa mukusunga bwino nthawi yofikira panyumba, makolo angadzakupatseni ufulu wowonjezereka m’tsogolo.—Luka 16:10.

Vuto lachiwiri: Sumvetsa chifukwa chimene umafikira msanga panyumba. Nikki, mtsikana wina amene ankadana ndi nthawi imene ankafikira panyumba, anati: “Ndikukumbukira kuti ndinkaganiza kuti mayi anga amangokonda kukhazikitsa malamulo basi.”

Zimene zingathandize: Tsatirani mfundo imene ikupezeka pa Miyambo 15:22, yakuti: “Zolingalira zizimidwa popanda upo; koma pochuluka aphungu zikhazikika.” Kambiranani nkhaniyo ndi makolo anu modekha. Afunseni chifukwa chimene anasankhira nthawiyo. *

Chifukwa chake zimathandiza: Kumva maganizo a makolo anu kungakutseguleni m’maso. Mnyamata wina, dzina lake Stephen, anati: “Bambo anandiuza kuti mayi satha kugona mpaka nditafika bwino panyumba. Sindinaganizepo zimenezi ngakhale pang’ono m’mbuyo monsemo.”

Dziwani kuti ndi bwino nthawi zonse kukambirana modekha osati kukhadzulirana mawu, kumene kumakhala ndi mavuto ake. Natasha, tamutchula poyambirira uja, anati: “Ndimaona kuti ndikawakhadzulira mawu makolo anga, pamapeto pake amandiletsa zinthu zingapo zimene ndikufuna kuchita.”

Vuto lachitatu: Umakhala ngati kapolo. Nthawi zina makolo amanena kuti malamulo apanyumba, kuphatikizapo nthawi yofikira pakhomo, ndi oti akuthandize iweyo. Mtsikana wina wazaka 20, dzina lake Brandi, anati: “Makolo anga akamandiuza zimenezi, ndimaona ngati sakufuna kuti ndikhale ndi ufulu wosankha zimene ndikufuna kapena wonena maganizo anga.”

Zimene zingathandize: Mungatsatire uphungu wa Yesu umene ukupezeka pa Mateyo 5:41, wakuti: “Winawake waudindo akakulamula kumunyamulira katundu mtunda wa kilomita imodzi, umunyamulire makilomita awiri.” Ashley ndi mchimwene wake anapeza njira yothandiza pogwiritsa ntchito mfundo imeneyi. Iye akuti: “Nthawi zambiri timayesetsa kufika panyumba kutatsala mphindi 15 kuti nthawi yeniyeni yofikira panyumba ikwane.” Kodi inu simungachitenso zimenezi?

Chifukwa chake zimathandiza: Zimasangalatsa kwambiri kuchita zinthu chifukwa chakuti tikufuna, kusiyana ndi kungochita chifukwa chakuti palibe mochitira. Ndipotu taganizirani izi: Ngati mwasankha kufika panyumba mofulumira, ndiye kuti winawake sakukulamulirani pa zimene mukuchita ndi nthawi yanu. Musaiwalenso mfundo yakuti: “Chabwino chimene ungachite chisakhale chokukakamiza, koma uchite mwa kufuna kwa mtima wako.”—Filemoni 14.

Kufika panyumba mofulumira kumachititsanso makolo anu kukukhulupirirani, ndipo zikatero angakupatseni ufulu wowonjezereka. Wade, wazaka 18, akuti: “Makolo akayamba kukukhulupirira, amakuwonjezera ufulu.”

Lembani vuto lina limene mumaliona.

․․․․․

N’chiyani chingakuthandizeni kulithetsa?

․․․․․

Mukuganiza kuti zimenezi zingathandize chifukwa chiyani?

․․․․․

Tsiku lina mudzachokeratu panyumba ya makolo anu ndipo mudzakhala ndi ufulu wonse. Koma panopa, mtima m’malo. Tiffany, yemwe ali ndi zaka 20, akuti: “Panopa simungakhale ndi ufulu wonse umene mukufuna, koma ngati mukutsatira zimene makolo anu akukuuzani, sikuti zaka zonse za unyamata wanu zidzakhala zosasangalatsa.”

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mayina m’nkhani ino asinthidwa.

^ ndime 21 Kuti mumve zambiri, onani nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa . . . N’chifukwa Chiyani Amandiikira Malamulo Ambirimbiri?” mu Galamukani! ya December 2006.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi nthawi yanu yofikira panyumba, imasonyeza bwanji kuti makolo anu amakukondani?

▪ Ngati mwalephera kusunga nthawi yofikira panyumba, mungatani?

[Bokosi patsamba 27]

ZIMENE ANZANU ENA ANENA

“Ndimaona kuti nthawi yofikira panyumba imene ndinapatsidwa ndi yabwino, chifukwa ngati sindigona mokwanira ndimafulumira kukwiya.”—Gabe, wazaka 17.

“Nthawi yofikira panyumba yandipulumutsa nthawi zambiri. Mwachitsanzo, tsiku lina ana anzanga omwe sanafike msinkhu womwa mowa, anabweretsa mowa pachisangalalo. Ine ndi mnzanga wina titangoona mowawo, tinatsanzika ponena kuti nthawi yathu yopitira kunyumba yakwana.”—Katie, wazaka 18.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 28]

NGATI MUKUFUNA KUTI AKUWONJEZERENI NTHAWI . . .

▪ Kambiranani nkhaniyo panthawi yoyenera.—Mlaliki 3:1, 7.

▪ Muzisunga nthawi yanu yofikira panyumba kuti mukhale ndi mbiri yabwino.—Mateyo 5:37.

▪ Pemphani makolo anu kukuwonjezerani nthawi yofikira panyumba masiku ena kuti iwo aone kuti ndinu wodalirika.—Mateyo 25:23.

[Bokosi patsamba 29]

MAWU KWA MAKOLO

▪ Nthawi yofikira panyumba imene munaikira mwana wanu yadutsa ndipo papita mphindi 30 koma iye sakufikabe. Kenako mukumva chitseko chikutseguka pang’onopang’ono. ‘Akuganiza kuti ndagona kale,’ mukutero. Koma inu simunagone. Ndipo munachita kukhala pafupi ndi chitsekocho itakwana nthawi imene mwana wanu anafunikira kufika. Chitsekocho chatseguka tsopano, ndipo mukuyang’anizana. Kodi munganene chiyani? Kodi mungachite chiyani?

Mungasankhe kuchita zinthu zingapo. Mwina mungakhululuke, poganiza kuti, ‘Mwana ndi mwana, amalakwitsa.’ Kapena mungaume mtima n’kumuuza kuti, “Basi, suzichokanso panyumba.” Koma m’malo mofulumira kukwiya, mvetserani kaye, mwina pali chifukwa chomveka chimene wachedwera. Kenako mungagwiritse ntchito zimene walakwazo ngati mpata womuphunzitsira mfundo yofunika kwambiri. Mungachite bwanji zimenezi?

Zimene mungachite: Muuzeni mwana wanuyo kuti mukambirana nkhaniyo kukacha. Kenako kukacha, khalani naye pansi panthawi yabwino n’kumuuza zimene muchite. Makolo ena achita zotsatirazi. Ngati mwana wawo sanasunge nthawi yofikira panyumba, ulendo wotsatira umene akuchoka amamuuza kuti afike panyumba mofulumira ndi mphindi 30, nthawi yake yeniyeni yofikira panyumba isanakwane. Koma ngati mwanayo amasunga nthawi yofikira panyumba ndipo wasonyeza kuti ndi wodalirika, mungaganizire zomuwonjezera ufulu, ndipo mwinanso kumuwonjezera nthawi yofikira panyumba. M’pofunika kwambiri kuti mwana wanu azidziwa bwino nthawi imene ayenera kufikira panyumba ndi zimene mudzachite ngati walephera kusunga nthawiyo. Ndipo akalakwa, musalephere kupereka chilango.

Chenjezo: Baibulo limati: “Kulolera kwanu kudziwike.” (Afilipi 4:5) Musanamuikire nthawi yofikira panyumba, kambiranani za nkhaniyo. Muloleni anene nthawi imene angakonde ndi zifukwa zake. Ganizirani bwino zimene wanenazo. Ngati mwana wanu wasonyeza kuti ndi wodalirika, mungamuganizire pa zimene akufunazo ngati zili zomveka.

Kusunga nthawi ndi kofunika kwambiri pamoyo. Choncho, cholinga choikira nthawi yofikira panyumba si chakuti mwana wanu angopewa mavuto. Koma kuti mum’phunzitse kuchita zinthu zimene zidzamuthandiza akadzachoka panyumba panu.—Miyambo 22:6.

[Chithunzi patsamba 27]

Mofanana ndi laisensi ya galimoto, nthawi yanu yofikira panyumba ndi umboni wakuti mukukula