Mmero Wodutsira Mkaka
Panagona Luso!
Mmero Wodutsira Mkaka
▪ Ngati munaonapo nkhosa, mbuzi kapena ng’ombe ikubereka, muyenera kuti munadabwa kuona kuti kamwanako sikachedwa kuimirira ndi kupeza bere kuti kayamwe. Nyama zonse zosaikira mazira zimayamwitsa ana awo mkaka. Koma ana a nyama zoterezi zimene zimabzikula, monga nkhosa, mbuzi ndi ng’ombe, ndi odabwitsa m’njira inanso.
Taganizirani izi: Ng’ombe zili ndi chifu cha zigawo zinayi, zomwe zimagwira ntchito zosiyanasiyana zogaya udzu ndi mbewu zina. Komatu tiana ta ng’ombe timayamwa mkaka basi, umene sufunika kudutsa m’zigawo zonsezo kuti ugayike. Choncho pamene kamwana kakuyamwa, mmero wapadera umatseguka kuti mkakawo udutse ndi kukalowa m’chigawo chomaliza cha chifu.
Ngati mkaka ungalowe m’chigawo choyamba, chodziwikanso kuti nyado, kamwanako kangavutike kwambiri. Zili choncho chifukwa mu nyado ndi mmene zakudya zolimba kwambiri zimagayidwa pogwiritsa ntchito mabakiteriya amene amathandiza kuti chakudya chisase. Mkaka ukamasasa, umatulutsa mpweya umene tiana sitingathe kuutulutsa. Koma tiana ta nyama zobzikula tikamayamwa mkaka kubere kapena m’chibekete, mmero wolowera ku nyado umatsekeka wokha.
Koma chodabwitsa n’chakuti kamwana kakamamwa madzi, pamachitika zosiyana ndi zimene tafotokozazi. Kamwanako kamafunika madzi ambiri m’nyado kuti mabakiteriya ndi tizilombo tina tichulukane mmenemo pokonzekera nthawi imene kadzayambe kudya udzu ndi mbewu zina. Ngakhale kuti mkaka umapita kuchigawo chomaliza cha chifu, madzi amalowa m’nyado. Mmero wa mwana wa ng’ombe wodabwitsawu ndi wodutsira mkaka basi.
Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi zinangochitika kuti nyamazi zikhale ndi mmero wodutsira mkakawu? Kapena kodi pali Mlengi wanzeru amene anazipanga?
[Chithunzi patsamba 13]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Mkaka umapitirira zigawo zitatu zoyambirira za chifu cha mwana wa ng’ombe
[Chithunzi]
Mmero wodutsira mkaka
1 Nyado
2 Kafucheche
3 Chidyaabusa
4 Chigawo chomaliza cha chifu