Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu a ku Okinawa Amakhala ndi Moyo Zaka Zambiri Kodi Chinsinsi Chawo N’chiyani?

Anthu a ku Okinawa Amakhala ndi Moyo Zaka Zambiri Kodi Chinsinsi Chawo N’chiyani?

Anthu a ku Okinawa Amakhala ndi Moyo Zaka Zambiri Kodi Chinsinsi Chawo N’chiyani?

YOLEMBEDWA KU JAPAN

▪ M’chaka cha 2006 pa zilumba za Okinawa, m’dziko la Japan, panali anthu okwana 1.3 miliyoni ndipo anthu pafupifupi 740 anali azaka zoposa 100. Pa anthu amene anali ndi zaka zoposa 100 amenewa, pafupifupi anthu 666 anali akazi. Malinga ndi kafukufuku amene anachita kumeneko motsogoleredwa ndi Dr. Makoto Suzuki, ndiye kuti pa anthu 100,000 alionse, pafupifupi 50 anali azaka zoposa 100. Koma m’mayiko ambiri otukuka, pa anthu 100,000 alionse, anthu 10 kapena 20 ndi amene ali ndi zaka zoposa 100.

Pakafukufuku ameneyu, amene ena amati ndi “kafukufuku wakale kwambiri padziko lonse wokhudza anthu azaka zoposa 100 yemwe akuchitikabe mpaka pano,” anapeza kuti “anthu ambiri azaka zoposa 100 [anali] athanzi labwino.” Pofuna kupeza chifukwa chake anthuwa anali athanzi labwino, Suzuki ndi gulu lake anafufuza anthu oposa 900 azaka zoposa 100 kuti adziwe zimene amachita pamoyo wawo ndiponso chibadwa chawo. Iwo anafufuzanso anthu ena a ku Okinawa azaka 70 kapena kuposerapo. Ofufuzawa anapeza kuti anthu amenewa anali ochepa matupi koma amphamvu ndi athanzi. Mitsempha yawo inali yosatsekeka ndi mafuta, komanso ambiri mwa anthu amenewa analibe matenda a khansa kapena a mtima. Ndipo pa anthu azaka zoposa 95, panali anthu ochepa odwala matenda a maganizo poyerekeza ndi anthu azaka zomwezi a m’mayiko ena otukuka. Kodi chinsinsi cha anthu amenewa n’chiyani?

Chifukwa chachikulu ndi chibadwa chawo. Komanso pali zifukwa zina monga kusasuta fodya, kusamwa kwambiri mowa, ndiponso kudya bwino. Anthu a ku Okinawa amadya zakudya zokhala ndi shuga wochepa, amakonda kwambiri masamba, zipatso ndiponso mafuta osanenepetsa kwambiri. Anthu amenewa alinso ndi chizolowezi chokudya pang’ono. Munthu wina amene akuchita nawo kafukufukuyu, dzina lake Dr. Bradley Willcox anati: “Muzisiya kudya mukangoyamba kumva kuti mwakhuta, chifukwa pamatenga mphindi 20 kuti mimba idziwitse ubongo kuti yakhuta.”

Anthu a ku Okinawa amachita zinthu zambiri zolimbitsa thupi monga kulima, kuyendayenda, kapena kuvina magule. Pa za khalidwe, atafufuza anapeza kuti anthu azaka zoposa 100 amenewa anali osangalala komanso omva maganizo a anzawo. Anapezanso kuti amadziwa mmene angathetsere nkhawa ndipo azimayi ochuluka anali “ochezeka kwambiri.”

Willcox ananenanso kuti “palibe mankhwala” othandiza munthu kuti akhale ndi moyo kwa zaka zambiri. Malinga ndi zimene anapeza pakafukufuku wawoyo, anthu amenewa amakhala ndi moyo kwa zaka zambiri chifukwa cha chibadwa chawo, zakudya, masewero olimbitsa thupi, makhalidwe abwino ndiponso “njira zabwino zothetsera nkhawa.”