Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Chithunzichi Chalakwika Pati?
Tchulani zinthu zitatu pa chithunzichi zomwe sizikugwirizana ndi nkhani ya m’Baibulo ya pa Genesis 7:1-9, 13-16, 23; 8:15-19.
1. ․․․․․
2. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Yerekezerani Levitiko 11:3 ndi Deuteronomo 14:4.
3. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Yerekezerani ndi Deuteronomo 14:7-19.
KAMBIRANANI:
Kodi Nowa anathandizidwa bwanji ndi ana ake komanso azipongozi ake? Kodi mungatsanzire bwanji ana a Nowa?
Kuchokera M’magazini Ino
Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.
TSAMBA 6 Kodi munthu wokonda ndalama sangakhale ndi chiyani? Mlaliki 5:․․․
TSAMBA 9 Kodi ndi anthu otani amene angakhale osangalala? Mateyo 5:․․․
TSAMBA 18 Kodi munthu sayenera kuchita chiyani popemphera? Mateyo 6:․․․
TSAMBA 28 Kodi tizitani tikakhala ndi nkhawa? 1 Petulo 5:․․․
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?
Onani zokuthandizani kupeza yankho. Onaninso malembawo. Kenako lembani mayina olondola pa mizereyi.
4. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ngakhale kuti bambo anga anali ndi khalidwe loipa, ine ndinali mfumu imene ‘inaumirira Yehova.’
Werengani 2 Mafumu 18:1-6.
5. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ndinagwiritsa ntchito molakwika mphamvu zanga mwa kupha anthu ambiri osachimwa.
Werengani 2 Mafumu 21:16.
6. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ndinatengera khalidwe loipa la bambo anga ndipo ndinaphedwa ndi anyamata anga.
Werengani 2 Mafumu 21:19-23.
▪ Mayankho ali pa tsamba 22
MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31
1. Chingalawa sichinali chosongoka kumbuyo ndi kutsogolo.
2. Nowa analowetsa m’chingalawa nyama 7 “zoyera,” monga nkhosa.
3 Nowa analowetsa m’chingalawa nyama ziwiri zokha pamtundu uliwonse wa nyama ‘zodetsedwa.’
4 Hezekiya.—Mateyo 1:9.
5. Manase.—Mateyo 1:10.
6. Amoni.—Mateyo 1:10.