Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndani Angatithandize Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino?

Kodi Ndani Angatithandize Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino?

Kodi Ndani Angatithandize Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino?

KODI ndani angatithandize kuti zinthu zizitiyenderadi bwino pamoyo wathu wonse osati pankhani zochepa chabe? Monga tafotokozera m’nkhani yapitayi, kuti zinthu zizitiyendera bwino timafunika kutsatira mfundo zabwino ndiponso kukhala ndi cholinga chabwino pamoyo. Zinthu zimenezi sizidalira kutchuka, kulemera kapena mphamvu.

Kodi tingapeze kuti mfundo zabwino komanso mayankho a mafunso okhudza cholinga cha moyo? Kodi ndi mwa kutsatira maganizo athu? Kunena zoona, popeza ndife opanda ungwiro, nthawi zambiri timafuna zinthu zolakwika zimene zimatipangitsa kusankha zinthu molakwika. (Genesis 8:21) N’chifukwa chake anthu ambiri amakonda kuchita zinthu zopanda pake zimene Baibulo limazitchula kuti “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pamoyo wake.” (1 Yohane 2:16) Koma zimenezi si zimene zingachititse moyo kukhala wabwino. Zimenezi zimangochititsa anthu kuganiza kuti zinthu zikuwayendera bwino koma mapeto ake amakhumudwa ndipo sasangalala. N’chifukwa chake anthu ambiri amapempha Mlengi kuti awathandize kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri pamoyo. *

Mulungu Ndi Amene Angatithandize

N’chifukwa chiyani ndi bwino kupempha Mlengi kuti atithandize pankhani imeneyi? Iye amadziwa chifukwa chake anatilenga, choncho amadziwanso zimene tiyenera kuchita pa moyo wathu. Iye amadziwanso mmene anapangira matupi ndi maganizo athu. Motero Mulungu amadziwa mfundo zabwino kwambiri zimene anthufe tiyenera kutsatira. Ndiponso, Mulungu ndiye chikondi ndipo amafuna kuti tikhale osangalala komanso kuti zinthu zizitiyendera bwino. (1 Yohane 4:8) Kodi malangizo amene Iye amatipatsa chifukwa chotikonda tingawapeze kuti? Tingawapeze m’Baibulo limene Mulungu anatilembera pogwiritsa ntchito amuna okwanira 40. * (2 Timoteyo 3:16, 17) Komabe, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malangizo a m’buku limeneli?

Yesu Khristu, yemwe ndi woimira wamkulu wa Mulungu, anati: “Nzeru imatsimikizirika kukhala yolungama mwa ntchito zake,” kapena kuti zotsatira zake. (Mateyo 11:19; Yohane 7:29) Nzeru zochokera kwa Mulungu zimatithandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino komanso tizisangalala nthawi zonse ‘m’mayendedwe onse abwino.’ Koma anthu amene amatsatira nzeru za anthu osati za Mulungu, zinthu siziwayendera bwino ndipo sasangalala.—Miyambo 2:8, 9; Yeremiya 8:9.

Taganizirani za gulu la achinyamata la m’ma 1960 lomwe silinkafuna kutsatira chikhalidwe chawo. Achinyamata amenewa sankatsatira malangizo a anthu achikulire ndipo ankalimbikitsa ena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kukhala moyo wosaganizira za m’tsogolo ndiponso ufulu pankhani ya kugonana. Koma kodi chinali cha nzeru kukhala moyo wotere? Kodi khalidwe limeneli linathandiza anthu kukhala ndi cholinga chabwino pamoyo ndiponso kukhala ndi mfundo zabwino zothandiza anthu kukhala ndi mtendere wa mumtima komanso osangalala nthawi zonse? Mbiri ikusonyeza kuti moyo umenewu sunathandize anthu kukhala abwino koma unapangitsa kuti makhalidwe abwino ayambe kulowa pansi.—2 Timoteyo 3:1-5.

Mosiyana ndi nzeru za anthu, malangizo a m’Baibulo amathandiza nthawi zonse. (Yesaya 40:8) Mukamawerenga nkhani yotsatira muona chifukwa chake tikutero. Nkhani imeneyi ikufotokoza mfundo 6 za m’Baibulo zimene zathandiza anthu ambiri, ochokera m’mitundu yonse, kuti zinthu ziziwayendera bwino komanso azisangalala, kaya ndi olemera kapena osauka.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Onani magazini yapadera ya Galamukani! ya November 2007, imene inafotokoza nkhani yakuti “Kodi Tiyenera Kukhulupirira Baibulo?” Nkhani za m’magazini imeneyi zinafotokoza umboni wa ofukula zinthu zakale, akatswiri a mbiri yakale, asayansi ndiponso umboni wina wosonyeza kuti Baibulo ndi louziridwadi ndi Mulungu.

[Bokosi patsamba 5]

 ZIMENE ZIMACHITITSA ENA KUONA KUTI MOYO WABWINO NDI WOPANDA PHINDU

Anthu ambiri amakhulupilira kuti kulibe Mulungu ndiponso kuti zinthu zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina. Maganizo amenewa akanakhala kuti ndi oona ndiye kuti tikanati zinthu zinangokhalako mwangozi ndipo zikanakhala zopanda phindu kufunafuna cholinga cha moyo komanso mfundo zoti tizitsatira.

Ena amakhulupilira kuti tinalengedwa ndi Mulungu komano Iye anangotisiya. Ngati zili choncho ndiye kuti anthufe ndi amasiye ndipo moyo wathu ulibe cholinga komanso mfundo zenizeni zoti tizitsatira. Taganizirani izi: Mulungu analenga nyama iliyonse ndi nzeru zachibadwa kuti izitha kuchita zinthu zosiyanasiyana m’chilengedwe. Ndipo zimenezi zachititsa kuti nzeru zapamwamba za Mulungu zionekere m’chilengedwe. Kodi Mlengi yemweyu angatilenge n’kutisiya opanda kutitsogolera? Ayi sangatero.—Aroma 1:19, 20.

Chifukwa choti anthu amene amakhulupirira kuti kulibe Mulungu amaona kuti kufunafuna cholinga pamoyo komanso mfundo zabwino n’kopanda phindu, amaganiza kuti munthu amakhala ndi moyo wabwino ngati ali ndi chuma kapena ntchito yabwino.

[Chithunzi patsamba 5]

Nzeru ya m’Baibulo imatsimikizirika kukhala yothandiza chifukwa cha zotsatira zake zabwino