Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mfundo 6 Zokuthandizani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino

Mfundo 6 Zokuthandizani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino

Mfundo 6 Zokuthandizani Kuti Zinthu Zizikuyenderani Bwino

MOYO umakhala wabwino kwambiri zinthu zikamatiyendera bwino. Zimenezi zimachitika ngati tikutsatira malamulo a Mulungu ndiponso ngati tikukhala ndi moyo mogwirizana ndi cholinga chake. Baibulo limanena kuti munthu amene ali ndi moyo wabwino ‘akunga mtengo wowoka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.’Salmo 1:3.

Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro ndipo timalakwa, zinthu zingatiyendere bwino pamoyo wathu. Kodi mumafuna kukhala ndi moyo wotero? Ngati ndi choncho, mfundo 6 za m’Baibulo zotsatirazi zingakuthandizeni. Ndipo mutsimikiza kuti mfundo za m’Baibulo ndi nzerudi za Mulungu.—Yakobe 3:17.

1 Khalani ndi Maganizo Oyenera Pankhani ya Ndalama

“Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena . . . adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.” (1 Timoteyo 6:10) Onani kuti vuto si kukhala ndi ndalama, chifukwa tonse timafunika ndalama pamoyo wathu. Koma vuto lagona pa kukonda ndalama. Chikondi chimenechi chimapangitsa munthu kuona ndalama ngati ambuye kapena mulungu wake.

Monga taonera m’nkhani yoyamba ija, anthu amene amafunafuna chuma poganiza kuti chingawathandize kukhala ndi moyo wabwino, akulimbikira mtunda wopanda madzi. Iwo amakhumudwa komanso amadzibweretsera zopweteka zambiri. Mwachitsanzo, pofuna chuma nthawi zambiri anthu amanyalanyaza mabanja awo komanso mabwenzi awo. Ena sagona n’komwe chifukwa cha ntchito, nkhawa kapenanso maganizo. Lemba la Mlaliki 5:12 limati: “Tulo ta munthu wogwira ntchito n’tabwino, ngakhale adya pang’ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikum’gonetsa tulo.”

Ndalama zingatibweretsere zopweteka komanso n’zonyenga zedi. Ndipo Yesu Khristu ananena za “chinyengo champhamvu cha chuma.” (Maliko 4:19) M’mawu ena, tinganene kuti chuma chimaoneka ngati chingatipatse chimwemwe koma si mmene zimakhalira. Chimangopangitsa munthu kukhala ndi mtima wofuna chuma chambiri. Lemba la Mlaliki 5:10 limati: “Wokonda siliva sadzakhuta siliva.”

Mwachidule, tingati munthu wokonda ndalama amadzipweteka yekha ndipo mapeto ake amakhumudwa ngakhale kuchita zachiwembu kumene. (Miyambo 28:20) Kupatsa, kukhululukira ena, makhalidwe abwino, chikondi ndiponso ubwenzi wabwino ndi Mulungu n’zimene zimathandiza munthu kukhala wosangalala komanso ndi moyo wabwino.

2 Khalani ndi Mtima Wopatsa

“Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Ngakhale kuti kupatsa kwa apo ndi apo kungapangitse munthu kusangalala, munthu wamtima wopatsa amakhala wosangalala nthawi zonse. Pali njira zambiri zimene tingasonyezere kuti ndife opatsa. Koma njira yabwino kwambiri yochitira zimenezi ndiponso imene ambiri amaiyamikira ndiyo kudzipereka kuthandiza ena.

Katswiri wa kafukufuku, Stephen G. Post, atafufuza pankhani yoganizira ena, kusangalala ndiponso thanzi ananena kuti, munthu woganizira ndiponso wothandiza anthu ena, amakhala ndi moyo wautali, wabwino ndi wathanzi komanso sakhala ndi nkhawa zambiri.

Ndipo anthu amene amapatsa mowolowa manja sasauka chifukwa chopatsa ena zinthu. Lemba la Miyambo 11:25 limati: “Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.” Mogwirizana ndi mawu amenewa, anthu amene alidi ndi mtima wopatsa, amene amapereka osati ndi cholinga chakuti nawonso adzapatsidwe, amayamikiridwa komanso amakondedwa kwambiri ndi Mulungu.—Aheberi 13:16.

3 Muzikhululuka ndi Mtima Wonse

“Pitirizani . . . kukhululukirana wina ndi mnzake ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaula za mnzake. Monga Yehova anakukhululukirani ndi mtima wonse, teroni inunso.” (Akolose 3:13) Masiku ano, anthu ambiri safuna kukhululukira anzawo. Iwo amafuna kubwezera osati kuchitira anzawo chifundo. Motero, anthu omwe achitiridwa chipongwe kapena chiwawa nawonso amabwezera chipongwe kapena chiwawa.

Ndipotu mavuto ake si okhawa. Nyuzipepala ina ya ku Montreal, ku Canada, inati: “Kafukufuku yemwe anachitika pa anthu oposa 4,600 azaka zapakati pa 18 ndi 30, anasonyeza kuti anthu ankhanza kwambiri, okonda kukhumudwa ndiponso opanda chifundo” nthawi zambiri anali ndi vuto la mapapo. Ndipo mavuto ena anali aakulu kuposa amene munthu angakhale nawo chifukwa chosuta fodya. Ndithudi, mtima wokhululuka umatithandiza kukhala bwino ndi anthu ena komanso onani kuti umatithandiza kukhala ndi thanzi labwino.—The Gazette.

Kodi mungatani kuti muzikhululukira ena kwambiri? Choyamba, dziunikeni kaye. Kodi nthawi zina simumakhumudwitsa ena? Kodi simusangalala akakukhululukirani? Ndiyeno bwanji nanunso osamakhululukira ena? (Mateyo 18:21-35) Pankhani imeneyi, timafunikanso kukhala odziletsa. Ndipo anthu ena amati tikakwiya ndi bwino kudikira kaye tisanachite chilichonse kuti mtima ukhale pansi. Komanso dziwani kuti kudziletsa n’chamuna. Lemba la Miyambo 16:32 limati: “Wosakwiya msanga aposa wamphamvu.” Mawu akuti “aposa wamphamvu” akusonyeza kuti munthu wotere ndi wopambana.

4 Tsatirani Malamulo a Mulungu

“Malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.” (Salmo 19:8) Kunena mwachidule, malamulo a Mulungu amatithandiza kuti tikhale ndi maonekedwe abwino ndiponso tiziganiza bwino. Amatithandizanso kupewa makhalidwe oipa monga kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, uchidakwa, chiwerewere ndiponso kuwona zinthu zolaula. (2 Akorinto 7:1; Akolose 3:5) Munthu wochita zimenezi angafike pochita zachiwembu, angasauke, angakhale wosakhulupirika, banja lake lingasokonezeke, angamavutike maganizo, angadwale ngakhalenso kufa msanga kumene.

Koma anthu amene amatsatira malamulo a Mulungu amakhala odzilemekeza, amapeza mabwenzi abwino, ndiponso amakhala ndi mtendere wa mumtima. Pa lemba la Yesaya 48:17, 18, Mulungu anati, ine ndine “amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” Ndipo anapitiriza kuti: “Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.” Inde, Mlengi wathu amatifunira zabwino kwambiri. Amafuna ‘kutitsogolera m’njira’ yamoyo wabwino.

5 Khalani ndi Chikondi Chopanda Dyera

“Chikondi chimamanga.” (1 Akorinto 8:1) Kodi moyo ukanakhala wotani popanda chikondi? Bwenzi uli wosasangalatsa komanso wopanda phindu. Mtumwi wachikhristu Paulo anauziridwa ndi Mulungu kulemba kuti: “Ngati . . . ndilibe chikondi [kwa ena], sindili kanthu . . . sindinapindule m’pang’ono pomwe.”—1 Akorinto 13:2, 3.

Chikondi chikutchulidwa pa lembali si chimene anthu okwatirana amasonyezana pankhani yogonana, chimenenso chili ndi nthawi yake. Koma ndi chikondi choposa chimenechi, chomwe ndi chokhalitsa ndipo chimayendera mfundo za Mulungu. * (Mateyo 22:37-39) Munthu amene amakhala ndi chikondi chimenechi samangofuna kuti anthu ena azimukonda koma iyenso amakonda ena. Paulo ananenanso kuti chikondi chimenechi n’choleza mtima ndiponso chokoma mtima. Sichichita nsanje, sichidzitama kapena kunyada. Chimatilimbikitsa kuchitira ena zabwino ndipo sichimakhumudwa msanga koma chimakhululuka. Chikondi chotero chimalimbikitsa ena. Ndiponso chikondi chimenechi chimatithandiza kukhala bwino ndi ena, makamaka a m’banja mwathu.—1 Akorinto 13:4-8.

Makolo amene amakonda ana awo amawapatsa malangizo omveka a m’Baibulo kuti akhale ndi khalidwe labwino. Ana okulira m’mabanja otere amakhala otetezeka ndi ogwirizana m’banja ndipo amaona kuti amakondedwa.—Aefeso 5:33–6:4; Akolose 3:20.

Jack yemwe ndi mnyamata wa ku United States, anakulira m’banja lotsatira malamulo a m’Baibulo. Iye atayamba kukhala yekha analembera makolo ake kalata. Mawu ena a m’kalatayo anali akuti: “Ndakhala ndikuyesetsa kutsatira lamulo [la m’Baibulo] lakuti: ‘Lemekeza atate wako ndi amako, . . . kuti chikukomere.’ (Deuteronomo 5:16) Ndipo zinthu zandiyenderadi bwino chifukwa chotsatira malangizo amenewa. Tsopano ndazindikira kuti zonsezi zachitika chifukwa choti munandisamalira mwachikondi. Ndikukuthokozani kwambiri chifukwa cha ntchito yonse imene munagwira pondilera.” Ngati ndinu kholo, kodi mungamve bwanji mutalandira kalata ngati imeneyi? Ndithudi, mungasangalale kwambiri.

Chikondi cha agape ‘chimakondweranso ndi choonadi,’ chomwe ndi mfundo za m’Baibulo. (1 Akorinto 13:6; Yohane 17:17) Mwachitsanzo: Anthu okwatirana amene ali ndi mavuto a m’banja angaganize zowerengera pamodzi mawu a Yesu opezeka pa Maliko 10:9 akuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi [banja], munthu asachilekanitse.” Tsopano afunika kupenda mitima yawo. Kodi ‘amakondweradi ndi choonadi cha m’Baibulo’? Kodi amaona banja lawo kuti ndi lopatulika monga mmene Mulungu amalionera? Kodi ndi ofunitsitsa kuthetsa mavuto awo mwachikondi? Ngati angachite zimenezi, banja lawo lingayende bwino ndipo angakhale osangalala.

6 Zindikirani Zosowa Zanu Zauzimu

“Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyo 5:3) Anthufe timasiyana ndi nyama chifukwa timazindikira kufunika kwa zinthu zauzimu. N’chifukwa chake timafunsa mafunso ngati akuti, Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? Kodi kunja kuno kuli Mlengi? Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? Kodi m’tsogolomu muli zotani?

Anthu ambiri oona mtima padziko lapansi aona kuti Baibulo limayankha mafunso amenewa. Mwachitsanzo, funso lomalizalo limakhudza cholinga cha Mulungu polenga anthu. Kodi cholinga chake n’chotani? Cholinga chake n’choti dziko lapansi likhale paradaiso momwe anthu okonda Mulungu ndi malamulo ake adzakhale kosatha. Lemba la Salmo 37:29 limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”

Ndithudi, Mlengi wathu amatifunira zinthu zabwino kwambiri osati kungokhala ndi moyo wabwino kwanthawi yochepa, mwina zaka 70 kapena 80 zokha. Iye amafuna kuti tikhale ndi moyo wabwino kosatha. Choncho, ino ndiyo nthawi yofunika kuti inuyo muphunzire za Mlengi wanu. Yesu anati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.” (Yohane 17:3) Mukamaphunzira zimenezi ndi kuzigwiritsa ntchito pamoyo wanu mudzaona nokha kuti “madalitso a Yehova alemeretsa, sawonjezerapo chisoni.”—Miyambo 10:22.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 22 M’Malemba Achigiriki Achikhristu, kapena kuti “Chipangano Chatsopano,” pafupifupi malo onse pamene pamapezeka mawu akuti “chikondi,” amachokera ku mawu Achigiriki akuti agape. Chikondi cha agape ndi chikondi chimene munthu amasonyeza potsatira mfundo za makhalidwe abwino, kaya munthuyo akufuna kapena sakufuna, podziwa kuti ndi udindo wake kuchitira ena zabwino. Ndipo chikondi cha agape si chachinyengo koma n’chenicheni ndipo chimachokera mumtima.—1 Petulo 1:22.

[Bokosi patsamba 7]

MFUNDO ZINA ZOKUTHANDIZANI KUTI ZINTHU ZIZIKUYENDERANI BWINO

Opani Mulungu. “Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.”—Miyambo 9:10.

Sankhani bwino anzanu. “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzaphwetekedwa.”—Miyambo 13:20.

Pewani kumwa ndi kudya kwambiri. “Wakumwaimwa ndi wosusukayo adzasauka.”—Miyambo 23:21.

Musamabwezere. “Musabwezere choipa pa choipa.”—Aroma 12:17.

Muzilimbikira ntchito. “Ngati wina safuna kugwira ntchito, asadyenso.”—2 Atesalonika 3:10.

Muzichitira ena zimene mumafuna kuti azikuchitirani. “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zimenezo.”—Mateyo 7:12.

Muzisamala polankhula. “Amene akufuna kusangalala ndi moyo ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake kulankhula zoipa.”—1 Petulo 3:10.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]

CHIKONDI NDI MANKHWALA

Dokotala wina yemwenso walembapo mabuku pankhani za matenda dzina lake Dean Ornish, analemba kuti: “Munthu amene akusowa chikondi ndi ubwenzi wa pamtima amadwala mosavuta, amakhala wachisoni ndipo amavutika, pamene munthu amene sakusowa chikondi amachira msanga, amakhala wosangalala komanso sachedwa kupeza bwino. Pakanakhala mankhwala amphamvu ngati imeneyi, ndiye kuti madokotala onse angamapereke kwa wodwala aliyense mankhwala amenewo. Ndipo kungakhale kulakwa kusapatsa odwala mankhwala woterowo.”

[Bokosi/Zithunzi patsamba 9]

TSOPANO ZIKUMUYENDERA BWINO

Milanko, yemwe amakhala ku dziko lina la ku Balkans, analowa usilikali panthawi imene kwawo kunkachitika nkhondo. Chifukwa chakuti ankachita zinthu molimba mtima, anapatsidwa dzina lakuti Rambo, potengera dzina la katswiri wa mafilimu achiwawa. M’kupita kwanthawi, Milanko anakhumudwa kwambiri ndi ntchito yake yausilikali poona katangale ndi chinyengo chimene chinkachitika pantchito yakeyo. Iye analemba kuti: “Zimenezi zinachititsa kuti ndiyambe makhalidwe oipa monga kumwa mowa, mankhwala osokoneza bongo, kusuta, njuga ndi chiwerewere. Moyo wanga unaipiratu moti sindinkadziwa kuti ndingasinthe bwanji.”

Moyo wake uli choncho, Milanko anayamba kuwerenga Baibulo. Nthawi ina atapita kukacheza kwa wachibale wake, anaona magazini ya Nsanja ya Olonda, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Iye anasangalala ndi zimene anawerenga m’magaziniyo ndipo kenako anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni. Mfundo za m’Baibulo zinam’thandiza kukhala wosangalala komanso kukhala ndi moyo wabwino. Iye anati: “Zinandilimbikitsa kusiya makhalidwe anga onse oipa ndi kukhala munthu watsopano, ndipo ndinabatizidwa kukhala wa Mboni za Yehova. Anthu amene ankandidziwa kuti ndine Rambo, tsopano amanditchula dzina langa lakale lakuti Bunny chifukwa tsopano ndine wofatsa ndiponso wakhalidwe.”