Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Tsopano mabuku, magazini ndi zinthu zina za Mboni za Yehova zikupezeka pa Intaneti pa adiresi yawo (www.pr418.com) m’zinenero 314. Chaka chatha, anthu oposa 22 miliyoni anagwiritsa ntchito adiresi imeneyi. Zimenezi zikutanthauza kuti tsiku lililonse anthu amene ankagwiritsa ntchito adiresi imeneyi analipo pafupifupi oposa 60,000.

“Masiku ano, vuto lalikulu padziko lonse ndi kupeza madzi abwino komanso okwanira anthu onse. . . . Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti nthawi zambiri kumene kumasowa madzi kumakhala kuti kuli nkhondo.”—BAN KI-MOON, UN SECRETARY-GENERAL.

Munthu Wosangalala Amakhala Wathanzi

Kuyambira kale, anthu akhala akuona kuti munthu wosangalala ndiponso amene sakonda kudandaula, nthawi zambiri amakhalanso wathanzi. Koma sizikhala choncho kwa anthu opanda chikondi, okonda kuda nkhawa komanso osachedwa kutaya mtima. Pakafukufuku wina amene wachitika posachedwapa, ofufuza apeza kuti anthu amene amasangalala sadwaladwala chifukwa timadzi tinatake tam’thupi timene timachititsa munthu kudwala timakhala tochepa. Anthu amenewa amakhalanso ndi “zinthu zimene zimateteza thupi lawo kuti lisamatupe.” Katswiri wina wa sayansi, Andrew Steptoe wa ku University College, ku London ananena kuti “munthu amakhala wosangalala osati chifukwa cha chibadwa chake koma kucheza bwino ndi anthu komanso kudziwa kuti akuchita zopindulitsa pamoyo wake.”

Kuona Mwezi ndi Zipangizo Zapamwamba

Kuyambira kale, Asilamu amayang’ana kumwamba kuti aone ngati mwezi watuluka. Mwezi ukaoneka amakhala mapeto a Ramadan ndipo amasiya kusala kudya. M’madera ena, ankaona mwezi popanda kugwiritsa ntchito chipangizo chilichonse ndiyeno mtsogoleri wachipembedzo amakauza okhulupirira anzake zimenezi. Koma m’zaka zingapo zapitazo, atsogoleri ena avomereza kuti aziona ngati mwezi watuluka pogwiritsa ntchito zipangizo zapamwamba. Tsopano akatswiri a sayansi ya zakuthambo a ku Iran ndi atsogoleri achipembedzo amene amaona ngati mwezi watuluka, akugwiritsa ntchito zipangizo zapamwamba kuonera mwezi. Zipangizo zake ndi zinthu monga makina oonera zinthu zakutali, zoonera zinthu usiku komanso ndege zimene zili ndi zoonera zinthu zakuthambo. Mwezi ukaoneka mofulumira ndiye kuti nyengo yosala kudya imatha msanga.

Kodi Ana Amazindikira Khalidwe la Munthu?

Ofufuza pa Yale University, ku America, ananena kuti ngakhale ana a miyezi 6 yokha amatha “kuzindikira khalidwe la munthu ngakhale asanayambe kulankhula.” Ana a miyezi 6 mpaka 10 anaona chidole cha maso aakulu chikukwera phiri ndipo zidole zina zinkathandiza chidolecho kuti chikwere, pamene zidole zina zimachikokera pansi. Nyuzipepala ina inanena kuti ndiyeno anawo “anapatsidwa zidolezo kuti asankhe chidole chimene akufuna kusewera nacho. . . . Pafupifupi mwana aliyense anasankha chidole chomwe chimathandiza chidole china chija kukwera phiri. Zimenezi zikusonyeza kuti anawo ankatha kusiyanitsa pakati pa chidole chabwino ndi choipa.” Nyuzipepalayo inanenanso kuti, penapake tingati “ngakhale ana angathe kusiyanitsa munthu woipa ndi wabwino, ndipo amadziwa munthu woyenera kusewera naye.”—Houston Chronicle.

‘Anthu Akukonda Kwambiri Madzi a M’mabotolo’

Magazini ina inati: “Anthu a ku America akukonda kwambiri madzi a m’mabotolo ndipo pachaka iwo amagula mabotolo amadzi pafupifupi 30 biliyoni.” Koma anthu ambiri amene amagula madzi a m’mabotolo samadziwa kuti ambiri amakhala otunga pampope. Magaziniyi inapitiriza kuti: “Ngati anthu ena amamwa madzi a m’mabotolowo kusiya apampope pofuna kupewa matenda ndiye kuti akudzinamiza.” M’mayiko ambiri, madzi apampope amawayeza bwino kwambiri motsatira malamulo a zaukhondo adzikolo. Komanso tingati madzi apampope ndi “aulere” powayerekezera ndi a m’mabotolo omwe ndi “odula kwambiri.”—U.S.News & World Report.