Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anachira ndi “Buku Lakale Kwambiri”

Anachira ndi “Buku Lakale Kwambiri”

Anachira ndi “Buku Lakale Kwambiri”

▪ Munthu wina wa Mboni za Yehova ku Brazil, South America, ankalalikira kunyumba ndi nyumba ndipo anapeza mayi wina amene anamuuza kuti apongozi ake anachira ndi buku linalake. Mboni ija inafunsa mwachidwi kuti buku lake liti. Mayiyo anati: “Ndi buku lakale kwambiri” ndipo anakatenga buku la mwana wake lakutha la Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.

Mayiyo anafotokoza kuti apongozi ake ankadwala matenda a maganizo ndipo ankawopa kwambiri kufa komanso ankawopa kukhala m’mdima moti sankachoka kuchipinda. Mwana wa mayiyo anapeza buku la Nkhani za Baibulo, ndipo anayamba kuwawerengera agogo akewo. Agogowo analimbikitsidwa kwambiri ndi zimene mdzukulu wawoyo ankawawerengera moti vuto lawolo linatha.

Mboniyo inati: “Nditawauza mayiwo kuti bukuli anafalitsa ndi a Mboni za Yehova ndiponso kuti ndikhoza kuwapezera lawo, anandiuza kuti ndikawabweretsere mabuku awiri, lawo ndi la apongozi awowo. Nditawapititsira mabukuwo, anandipemphanso ngati ndingawabweretsere ena. Patapita nthawi ndinawapatsa mabuku 16 ndipo anakapatsa anzawo.”

Mukhoza kuitanitsa Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, lomwe lili ndi nkhani za anthu ndiponso za m’Baibulo zokwana 116. Zaka 30 zapitazo kuchokera pamene bukuli linafalitsidwa, asindikiza mabuku amenewa oposa 72 miliyoni. Kuti mupeze bukuli lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire buku limene lasonyezedwa panoli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwa ulere.