Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chifukwa Chake Tili ndi moyo

Chifukwa Chake Tili ndi moyo

Chifukwa Chake Tili ndi moyo

BAIBULO limasonyeza kuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu, sachita zinthu popanda cholinga. Mwachitsanzo, taganizirani za mmene analengera kayendedwe ka madzi komwe kamathandiza kuti zinthu zithe kukhala ndi moyo padziko lapansi. Baibulo limafotokoza kayendedwe kameneka mwandakatulo komanso molondola kuti: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.”—Mlaliki 1:7.

Baibulo limayerekezera kudalirika kwa malonjezo a Mulungu ndi kayendedwe ka madzi kameneka. Monga timadziwira, dzuwa limapangitsa kuti madzi a m’nyanja ndi m’mitsinje asanduke nthunzi ndiyeno amadzagwa ngati mvula padziko pano. Yehova atatchula za kayendedwe kamadzi kameneka anati: “Momwemo adzakhala mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.”—Yesaya 55:10, 11.

Madzi abwino amagwanso kuchokera kumwamba kuti zinthu zithe kukhala ndi moyo padziko pano. Mofanana ndi zimenezi, “mawu [a Mulungu] amene atuluka m’kamwa” mwake amatha kukwaniritsa zosowa zathu zauzimu. Zili monga momwe Yesu Khristu ananenera kuti: “Munthu asakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu onse otuluka pakamwa pa Yehova.”—Mateyo 4:4.

Kuphunzira za Mulungu kumatithandiza kuchita zinthu mogwirizana ndi cholinga chake. Komabe, tisanachite zimenezi tiyenera kudziwa cholinga cha Mulungu. Mwachitsanzo, n’chifukwa chiyani Mulungu analenga dziko lapansi lino? Ndipo kodi cholinga chakecho chimatikhudza bwanji? Tiyeni tione mayankho a mafunso amenewa.

Cholinga cha Mulungu Polenga Dziko Lapansi

Popeza Mulungu amatifunira zabwino, anaika mwamuna ndi mkazi oyambirira, Adamu ndi Hava, m’munda wokongola wa Edeni. Ndiyeno anawalangiza kuti abalane. Iye anati: ‘Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.’—Genesis 1:26-28; 2:8, 9, 15.

Kodi mawu amenewa akusonyeza chiyani? N’zoonekeratu kuti Mulungu anafuna kuti dziko lonseli likhale paradaiso woti anthu akhalemo. Mawu ake amati: ‘Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.’Salmo 115:16.

Komabe, kuti anthu adzaone cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi chikukwaniritsidwa, afunika kulemekeza Yehova ndi kumumvera. Kodi Adamu anachita zimenezi? Ayi, anachimwa chifukwa sanamvere Mulungu. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Ana a Adamu, kuphatikizapo ifeyo, anatengera uchimo ndi imfa, monga momwe Baibulo limanenera kuti: “Monga uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.”—Aroma 5:12.

Chifukwa cha zimenezi, anthu onse amafa ndipo n’chifukwa chake dziko lapansi silinakhale paradaiso. Kodi zikutanthauza kuti cholinga cha Mulungu polenga dziko lapansi chinasintha?

Ayi, sichinasinthe. Kumbukirani kuti Mulungu anati: “Mawu anga amene atuluka m’kamwa mwanga, sadzabwerera kwa Ine chabe, koma adzachita chimene ndifuna, ndipo adzakula mmene ndinawatumizira.” Komanso, Mulungu analonjeza kuti: “Ndidzachita zofuna zanga zonse.” (Yesaya 45:18; 46:10; 55:11) Iye amafuna kuti dzikoli likhale paradaiso ndipo mukhale anthu omutumikira mosangalala kosatha, monga mmene anafunira poyamba. Zimenezi n’zimene Mulungu amafuna, kapena kuti cholinga chake.—Salmo 37:29; Yesaya 35:5, 6; 65:21-24; Chivumbulutso 21:3, 4.

Kodi Cholinga cha Mulungu Chidzakwaniritsidwa Bwanji?

Yehova anasonyeza nzeru ndi chikondi chake chachikulu pokonza zoti anthu amasuke ku uchimo ndi zotsatira zake, zomwe ndi kupanda ungwiro ndiponso imfa. Iye anachita zimenezi mwa kukonza zoti pabadwe mwana wopanda tchimo limene anthu onse amatengera kwa munthu woyamba, Adamu. Makonzedwe amenewa amatchedwa dipo, limene linaperekedwa kuti anthu otsatira malamulo a Mulungu akalandire moyo wosatha. (Mateyo 20:28; Aefeso 1:7; 1 Timoteyo 2:5, 6) Kodi dipo limeneli linaperekedwa motani?

Gabrieli, mngelo wa Yehova, anauza namwali Mariya kuti adzabereka mozizwitsa mwana wamwamuna ndipo anam’fotokozera mmene mwanayo adzabadwire ngakhale kuti iye anali ‘asanagonepo ndi mwamuna.’ Mulungu anasamutsa mozizwitsa moyo wa Mwana wake wamwamuna kuchoka kumwamba kupita m’mimba mwa Mariya. Motero, Mariya anatenga pathupi mwa mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu.—Luka 1:26-35.

Yesu anabadwa patatha miyezi 9 monga munthu wangwiro, mofanana ndi munthu woyamba, Adamu. Patapita nthawi, anapereka nsembe moyo wake wangwiro. Mwakuchita zimenezi, Yesu anakhala ‘Adamu wachiwiri’ ndipo anapangitsa kuti anthu onse okhulupirika kwa Mulungu awomboledwe ku uchimo ndi imfa.—1 Akorinto 15:45, 47.

Ndithudi, Mulungu anachita zimenezi chifukwa chotikonda, ndipo zizitilimbikitsa kumukondanso. Zili ngati mmene Baibulo limanenera kuti, “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Komano funso n’lakuti, kodi tingachite chiyani chifukwa cha chikondi chimene Mulungu watisonyeza? Tiyenera kuyamikira mphatso imeneyi. Onani mmene ena achitira zimenezi.

Khalani ndi Cholinga Pamoyo

Denise, amene tamutchula m’nkhani yapita ija, anapeza kuti kulemekeza Mulungu mwa kumvera malamulo ndi malangizo ake kunamuthandiza kukhala ndi cholinga pamoyo wake. Iye anati: “Kuwonjezera pa mfundo yakuti Mulungu adzakwaniritsa cholinga chimene anali nacho polenga anthu, ndaphunziranso m’Baibulo kuti Mulungu ali ndi ntchito imene anthu omutumikira afunika kugwira. Sindikuganiza kuti pali moyo wina wosangalatsa kuposa kutamanda Mulungu mwa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi cholinga chake.”

Ifenso tingachite zimenezi mwa kuphunzira zimene Mulungu amafuna ndiyeno n’kumazichita. N’zoona kuti panopa sitinapindule mokwanira ndi nsembe ya dipo, imene idzapangitse kuti tisangalale ndi moyo wangwiro m’dziko latsopano limene mudzakhale chilungamo. Komabe, panopo tifunika kukwaniritsa zimene mwachibadwa mtima wathu umafuna kudziwa pankhani zauzimu.

Dave, amene tamutchula m’nkhani yoyamba ija, ndi mmodzi mwa anthu amene anathetsa njala yawo yauzimu. Iye anapeza mayankho a mafunso okhudza cholinga cha moyo. Iye anati: “Ndikakumbukira mmene moyo wanga unalili ndisanadziwe cholinga cha Mulungu, ndimaona kuti unali wosapindulitsa. Panthawiyo sindinkadziwa kuti moyo wanga unali wosasangalatsa chifukwa chosakwaniritsa zosowa zanga zauzimu. Koma panopo ndikusangalala chifukwa ndikudziwa chifukwa chake ndili ndi moyo komanso ndikudziwa zimene ndiyenera kumachita.”

Inde, mosiyana ndi zimene anthu opanda ungwiro amaganiza, maganizo a Mulungu pankhani ya cholinga cha moyo, monga alembedwera m’Baibulo, ndi osangalatsa kwambiri. Tili ndi moyo chifukwa Yehova anali nafe cholinga potilenga. Iye anafuna kuti tizitamanda dzina lake, tikhale naye paubwenzi, ndipo motero tikwaniritse zosowa zathu zauzimu. Panopo komanso mpaka muyaya, tingasangalale ndi kukwaniritsidwa kwa mawu ouziridwa akuti: “Odala anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—Salmo 144:15.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 8]

CHINAYAMBITSA MAVUTO

Ena amati mavuto ndi chimodzi mwa zinthu zikuluzikulu zimene zimapangitsa kuti tizilephera kudziwa chifukwa chake tili ndi moyo. Viktor Frankl anati: “Ngati moyo uli ndi cholinga, ndiye kuti palinso chimene chimapangitsa kuti tizivutika. N’zovuta kuthetsa mavuto pamoyo wathu monga mmene zimavutira kuthetsa masoka ndi imfa.”

Baibulo limafotokoza chifukwa chake anthu amavutika komanso amafa. Mulungu si amene amachititsa kuti tizivutika. Timavutika chifukwa banja loyambirira linasankha kuchita zinthu mosadalira Mlengi wawo. Ana awo onse anatengera khalidwe loipa limeneli ndipo n’limene limachititsa kuti tizivutika.

Ngakhale kuti kudziwa chifukwa chake tili ndi moyo sikungathetse mavuto onse, kumatithandiza kuti tipirire. Komanso, kungatithandize kuyembekezera nthawi imene Mulungu adzachotse mavuto ndi imfa.

[Chithunzi patsamba 7]

Baibulo limayerekezera kudalirika kwa malonjezo a Mulungu ndi kayendedwe kodabwitsa ka madzi

[Chithunzi]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mvula Nthunzi Nthunzi

↓ ↑

↓ ↑

Nyanja, mitsinje

→ → Nyanja ya mchere

[Chithunzi patsamba 8]

Kodi tikudziwa kuti nthawi ina dzikoli lidzakhala paradaiso mmene mudzakhale anthu osangalala ndi athanzi?

[Chithunzi patsamba 9]

‘Sindikuganiza kuti pali moyo wina wosangalatsa kuposa kutamanda Mulungu.’—Denise