Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chinyengo cha Otsatsa Malonda

Chinyengo cha Otsatsa Malonda

Chinyengo cha Otsatsa Malonda

YOLEMBEDWA KU POLAND

Tomek wakopeka ndi zimene akuonera pa TV. Iye akumvera mwatcheru uthenga wotsatsa malonda wakuti: “Ngati mwana wanu avala izi, adzakhala katswiri pa masewero othamanga ndipo anzake adzamusirira kwambiri. Mugulireni mwana wanu zovala zimenezi!” Kenako Tomek akuthamangira kwa abambo ake, uku akuimba kanyimbo kotsatsira malondako. Amvekere: “Bambo, mundigulira?”

▪ N’chifukwa chiyani ana amakopeka ndi zinthu zimene akuzitsatsa malonda? Mphunzitsi wina amene anagwidwa mawu m’magazini ina ya ku Poland anati: “Iwo amafuna zinthuzo chifukwa chakuti anthu ena ali nazo. Iwo amafunanso kuti anzawo aziwaona kuti ndi ochita bwino.” (Rewia) Ana akamapempha zinthu amakwiya ngakhale kulira kumene ndipo nthawi zambiri makolo ena amangowagulira zimene akufunazo.

N’chifukwa chiyani uthenga wotsatsa zinthu za ana umakhala wonyenga kwambiri? Katswiri wina wa zamaganizo, dzina lake Jolanta Wąs, ananena kuti uthenga wotsatsa malonda “sunena za mtengo, kulimba kwa chinthucho kapena ubwino wake.” Cholinga cha uthengawo chimangokhala “kukopa omvetsera.” Katswiriyu anapitiriza kuti: “Ana sayamba aganizira uthenga wotsatsa malonda. . . . Iwo sayerekezera zimene akumva mu uthengawo ndi zimene amadziwa kuti ndizo zoona.” Ndipo ngakhale atachita zimenezi, sangadziwe bwinobwino za chinthucho chifukwa ana sadziwa zambiri.

Ndiyeno kodi mungateteze bwanji ana anu ku chinyengo cha otsatsa malonda? Choyamba, magazini taitchula kale ija inanenanso kuti: “Muzikhala ndi nthawi yokambirana ndi ana anu ndipo musasiye kuwafotokozera kuti munthu sakhala wofunika chifukwa chakuti amavala nsapato [kapena zovala] zopangidwa ndi kampani inayake.” Aphunzitseni ana anu kudziwa kuti n’zotheka kukhala osangalala ngakhale alibe zidole zatsopano. Chachiwiri, makolo ayenera kudziwa kuti uthenga wotsatsa malonda ungakope ana awo. Katswiri uja ananena kuti chofunika kwambiri n’chakuti “tisalole kuti otsatsa malonda atisankhire zinthu zimene zingakhale zabwino kwa ana athu.”

Chomaliza, makolo onse angapindule ndi malangizo a m’Baibulo. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Chilichonse cha m’dziko, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso ndi kudzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pamoyo wake, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko.”—1 Yohane 2:15, 16.

Kodi sizoona kuti otsatsa malonda ambiri amakopa “chilakolako cha maso” ndipo amalimbikitsa ana ndi akulu omwe ‘kudzionetsera ndi zimene ali nazo pamoyo wawo’? Mtumwi Yohane anapitiriza kulangiza kuti: “Dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu akhalabe kosatha.”—1 Yohane 2:17.

Makolo amene nthawi zonse amapeza nthawi yokambirana zinthu zaphindu ndi ana awo, angawaphunzitse mfundo za Mulungu ndiponso mfundo zina zothandiza. (Deuteronomo 6:5-7) Ngati tichita zimenezi, ana athu sadzatengeka mosavuta ndi chinyengo cha otsatsa malonda a dzikoli, amene cholinga chawo n’kupangitsa ana kuumiriza makolo awo kuti awagulire zinthuzo.