Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Zinachitikira Kuti?

1. Kodi Yesu ananyamukira kuti popita kumwamba?

ZOKUTHANDIZANI: Werengani Machitidwe 1:6-12.

Lembani mzere wozungulira yankho lanu pamapupo.

Phiri la Karimeli

Phiri la Gerizimu

Phiri la Maolivi

Hebroni

▪ Yesu atatsala pang’ono kupita kumwamba, ophunzira ake anamufunsa chiyani?

․․․․․

▪ Kodi Yesu anati ophunzira ake adzatani?

․․․․․

KAMBIRANANI:

Kodi mawu a angelo a pa Machitidwe 1:11 akwaniritsidwa bwanji? Kodi mungatani kuti muzichita nawo ntchito imene Yesu anauza otsatira ake, monga momwe zalembedwera pa Machitidwe 1:8?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

TSAMBA 4 Kodi Baibulo limanena chiyani za Eliya? Yakobe 5:․․․

TSAMBA 7 Kodi munthu amakhala ndi moyo ndi chiyani? Mateyo 4:․․․

TSAMBA 19 Kodi ndani amapambana mbale kuumirira? Miyambo 18:․․․

TSAMBA 20 Kodi pali nthawi yochita chiyani? Mlaliki 3:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?

Onani zokuthandizani kupeza yankho. Onaninso malembawo. Kenaka lembani mayina olondola pa mizereyi.

2. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Panthawi ya ulamuliro wanga, Hilikiya “anapeza buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.”

Werengani 2 Mbiri 34:1, 14.

3. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinali chiwanga kapena kuti kazembe woyamba wa Ayuda amene anabwerera ku Isiraeli kuchoka ku Babulo.

Werengani Hagai 1:14.

4. ․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ntchito yanga inali yopala matabwa.

Werengani Mateyo 1:16; 13:55.

▪ Mayankho ali pa tsamba 14

MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31

1. Phiri la Maolivi.

▪ Anamufunsa Yesu nthawi imene adzabwezeretse Ufumu.

▪ Yesu anati ophunzira ake adzalalikira za iye mpaka kumalekezero a dziko lapansi.

2. Yosiya.​—Mateyo 1:⁠10.

3. Zerubabele.​—Mateyo 1:⁠12.

4. Yosefe.​—Mateyo 1:⁠16.

[Mawu a Chithunzi patsamba 31]

Center circle: Oxford Scientific/​photolibrary