Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumene Mungapeze Mayankho

Kumene Mungapeze Mayankho

Kumene Mungapeze Mayankho

CHOLINGA chimodzi cha chipembedzo ndi kuphunzitsa anthu kuti adziwe cholinga cha moyo. Komabe, anthu ambiri aona kuti chipembedzo chawo chalephera kukwaniritsa zosowa zawo zauzimu. Denise, amene anakulira m’banja la Chikatolika, amakumbukira kuti: “M’katekisimu wa ku Baltimore muli funso lakuti, ‘Kodi n’chifukwa chiyani Mulungu anatilenga?’ ndipo yankho lake ndi lakuti, ‘Mulungu anatilenga pofuna kuonetsa ubwino wake ndiponso kuti tikasangalale naye kosatha kumwamba.’

Denise anapitiriza kuti: “Limeneli si yankho lomveka la funso lakuti n’chifukwa chiyani ndili ndi moyo. Ngati ndikungoyembekezera kudzapita kumwamba, kodi ndizichita chiyani panopa?” Anthu ambiri amaganiza mofanana ndi Denise. Pakafukufuku wina anapeza kuti anthu awiri pa anthu atatu alionse ankaona kuti matchalitchi ndi masunagoge ambiri sathandiza anthu kudziwa cholinga cha moyo.

Chifukwa cha zimenezi, iwo amakafufuza mayankho kwina monga kwa anthu asayansi, kwa anthu amene amayendera makhalidwe amene iwo amaona kuti ndi abwino, kwa anthu amene amakaniratu makhalidwe abwino komanso kwa anthu amene amakana kuti zinthu zinalengedwa ndi cholinga. Nanga n’chifukwa chiyani anthu amafunabe kudziwa cholinga cha moyo ngakhale kuti ndi ochepa chabe amene amachipeza?

Tinabadwa ndi Mtima Wofuna Zinthu Zauzimu

Dokotala wa zamaganizo, Kevin S. Seybold, ananena kuti “zikuoneka kuti anthu mwachibadwa amafuna kulambira.” Zaka zaposachepadwa asayansi ambiri afika pamfundo yakuti anthu mwachibadwa amafuna kudziwa cholinga chenicheni cha moyo. Anthu ena amakhulupirira kuti chibadwa ndiponso mmene anthu amachitira zinthu, zimasonyeza kuti anabadwa ndi mtima wofuna kukhala paubwenzi ndi wolamulira wamkulu.

Ngakhale kuti akatswiri a zamaphunziro ndiponso anthu ena anzeru amatsutsana pankhani imeneyi, anthu ambiri safunika kuuzidwa ndi asayansi kuti amafunika zinthu zauzimu. Mtima wofuna kuchita zinthu zauzimu ndi umene umachititsa kuti tidzifunsa mafunso ofunika kwambiri akuti: N’chifukwa chiyani tili ndi moyo? Kodi tiyenera kuchita chiyani pamoyo wathu? Ndiponso lakuti, Kodi Mlengi wamphamvu zonse adzatiweruza pa zimene timachita?

Ngati mutayang’ana mofatsa zinthu zolengedwa, mungapeze ena a mayankho a mafunso amenewa. Mwachitsanzo, taganizirani zinthu zodabwitsa kwambiri za m’chilengedwechi, kungoyambira zinthu zing’onozing’ono kwambiri mpaka milalang’amba imene ili kutali kwambiri. Kodi zinthu zimenezi sizimasonyeza kuti pali Mlengi wanzeru? Baibulo limati: “Chilengedwere dziko kumka m’tsogolo, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino lomwe. Makhalidwe a Mulungu amenewa, ngakhalenso mphamvu zake zosatha ndiponso Umulungu wake, zikuonekera m’zinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chodzilungamitsira.”—Aroma 1:20.

Kwaniritsani Zosowa Zanu Zauzimu

Ponena za mmene Mulungu analengera anthu, Baibulo limati: “Waika zamuyaya m’mitima yawo.” (Mlaliki 3:11) Mwachibadwa anthufe timafuna kukhala ndi moyo osati kufa. Ndiponso timafuna kudziwa cholinga chenicheni cha moyo, komanso kupeza mayankho a mafunso athu.

Ndipotu kufuna kupeza mayankho ndiye umunthuwo. Mkonzi wa nyuzipepala ina ataona zimene asayansi apanga ndiponso mmene luso la zopangapanga lapitira patsogolo, anati: “Tidakali ndi mafunso akuti kodi ndife ndani, n’chifukwa chiyani tili ndi moyo ndiponso kodi moyo wathuwu ukulowera kuti?” (The Wall Street Journal) Ndi bwino kupeza mayankho odalirika. Baibulo limanena kumene tingapeze mayankho amenewa. Limati: “Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake.”—Salmo 100:3.

Kodi si nzeru kuyang’ana kwa Mlengi wa zinthu zozizwitsa zimenezi kuti akwaniritse zosowa zathu zauzimu? Yesu Khristu anatilimbikitsa kuchita zimenezi. Iye ankazindikira kuti amene anatipatsa moyo, Mlengi wathu, ndi yekhayo amene angakwaniritse zosowa zathu zauzimu.—Salmo 36:5, 9; Mateyo 5:3, 6.

Ndithudi, kuti tikwaniritse zosowa zathu zauzimu, n’kofunika kwambiri kupeza yankho lodalirika la funso lakuti, N’chifukwa chiyani tili ndi moyo? Pitirizani kuwerenga kuti mumve maganizo otsitsimula a Mlengi wathu pankhani imeneyi.