Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhono Zokongola Kwambiri za Paua

Nkhono Zokongola Kwambiri za Paua

Nkhono Zokongola Kwambiri za Paua

YOLEMBEDWA KU NEW ZEALAND

M’nyanja mumakhala nkhono zikuluzikulu zomwe zimayenda pang’onopang’ono m’matanthwe ndipo zimadya zomera za m’mphepete mwa nyanjazi. Ziganamba zake, zomwe zimakhala zokongola kwambiri ndiponso zochititsa chidwi, zimakutidwa ndi laimu komanso tizilombo tina ta m’nyanja.

MTUNDU wa nkhono zimenezi umatchedwa paua ndipo umapezeka ku New Zealand. Nkhono za mtundu umenewu ndiponso za mitundu ina zimakhala m’matanthwe a m’mphepete mwa nyanja. Ndipo anthu amakonda nkhono za paua chifukwa cha kukongola kwa chiganamba chake, chimene amachigwiritsa ntchito popanga zinthu zokongola kwambiri monga ngale. Ndiponso anthu ena amanena kuti nyama yake ndi yokoma kwambiri.

Nkhono ya paua ndi imodzi mwa nkhono za mitundu yoposa 100 imene imapezeka padziko lapansi m’mayiko monga South Africa, California, U.S.A., Japan, Australia ndiponso pachilumba cha Guernsey ku English Channel. Koma nkhono ya paua yomwe chiganamba chake ndi chokongola kwambiri imapezeka kum’mwera kwa nyanja ya mchere ya South Pacific kokha, komwe madzi ake ndi ozizira.

Nkhonoyi Ndi Yochititsa Chidwi

Chiganamba cha nkhono imeneyi chili ndi mapuloteni ndiponso makemikolo enaake amene amachititsa kuti chizioneka chokongola kwambiri chikakhala pa dzuwa monga mmene ziganamba za nkhono zina za mtunduwu zimachitira. N’chifukwa chake nkhono ya paua imatchedwa nkhono yokongola kwambiri. Madzi akazizira kwambiri, nkhono zimenezi zimakabisala kapena kuti kugona. Panthawi imeneyi ziganamba za nkhonozi zimatenga nthawi yaitali kuti zikhwime. Katswiri wina wofufuza za nkhono za paua ananena kuti chiganamba chake chimaoneka ndi mitundu yosiyanasiyana chifukwa cha madzi komanso zakudya zomwe nkhonozi zimadya.

Nkhono zimenezi zimasankha kwambiri zakudya ndipo sizikonda kuyandikana ndi zamoyo zina, makamaka zimene zimadya zomera zomwe nkhonozi zimakonda. Ndipo nsomba inayake yotchedwa starfish ndi mdani wamkulu wa nkhono zimenezi. Nsomba zochepa chabe za mtundu umenewu zingathe kuseseratu nkhono zambirimbiri. Nsombazi zili ndi zinthu zinazake zooneka ngati miyendo zimene zimatha kutseka mopumira mwa nkhonozi ndipo zimabanika n’kugwa kuchokera ku matanthwe amene zimamata. Kenako nsombazi zimadya nkhonozi.

Nkhono za Paua Amazigwiritsa Ntchito M’njira Zambiri

Ngakhale kuti nkhono yeniyeniyo imaoneka yosakopa, mtundu wina wa anthu a ku New Zealand wotchedwa Amaori wakhala ukudya nyama yake kwa zaka zambiri. Mbali ya thupi la nkhono imene anthu amadya ndi mnofu wake umene imagwiritsa ntchito poyenda m’malo a miyala. Amaori amagwiritsanso ntchito chiganamba cha nkhonoyi ngati nyambo yophera nsomba ndiponso popanga zinthu zina zokongoletsera m’nyumba. Iwo amagwiritsanso ntchito ziganambazi popanga maso a ziboliboli.

Nkhono za mtundu umenewu ndi zotchuka kwambiri masiku ano. Ndipo alendo amene amakacheza ku New Zealand, salephera kugula mikanda yopangidwa ndi ziganamba za nkhonozi.

Masiku ano anthu ambiri osambira amagwira nkhono zochuluka, ngakhale popanda kugwiritsa ntchito zipangizo zopumira akapita pansi panyanja. Ndipo malonda ankhonozi abweretsa ndalama zambiri m’dzikoli. Pofuna kuteteza nkhono zimenezi, boma la New Zealand lakhazikitsa lamulo loletsa anthu kugwira nkhono zambiri. Nyama yambiri ya nkhonozi imaikidwa m’zitini n’kuitumiza ku Asia ndipo ina amaiziziritsa n’kuitumiza ku Singapore ndi ku Hong Kong kumene anthu amaikonda kwambiri. Nthawi zambiri nyamayi amangoiduladula n’kuidya yosaphika. Ngakhale kuti nkhonozi zimapezeka zambiri, anthu ambiri a ku New Zealand sanalaweko nyama yake chifukwa yambiri amaigulitsa kunja.

Popeza kuti mayiko ambiri akugula nkhono zimenezi, anthu ayamba ulimi wamakono wa nkhono. Ulimi umenewu ukuyendanso bwino kwambiri ku Australia, Japan, ndi ku United States. Njira yatsopano imeneyi yapangitsa kuti nkhono za paua azitha kuzisunga m’mathanki mmene madzi ake amatha kuwasintha kuti akhale ofunda kapena ozizira.

Nkhono zoweta zimenezi zimadya kwambiri mofanana ndi nkhono za m’nyanja. M’mlungu umodzi wokha zimatha kudya chakudya cholemera theka la thupi lawo. N’zodabwitsanso kuti nkhono za mtundu wa paua zimatha kutembenukanso mwamsanga akazigadamiza. Ulimi wa nkhono ndi wosavuta. Katswiri wina wa ulimi umenewu ananena kuti “nkhono za mtundu wa paua ndi zosavuta kuweta chifukwa ndi zofatsa.”

Ngale za Paua

Ngakhale kuti nkhono za paua amazigwiritsa ntchito popanga mikanda ndiponso amadya nyama yake, nkhonozi zimakhalanso ndi ngale zokongola kwambiri. Ngale zachilengedwe sizipezeka kawirikawiri m’nkhono zimene zili m’nyanja. Koma zimatha kupangidwa pogwiritsa ntchito njira imene katswiri wina wa sayansi wa ku France, dzina lake Louis Boutan, anayambitsa m’zaka za m’ma 1890. Pogwiritsa ntchito njira imeneyi amatha kupanga ngale yokhala ndi mitundu yofanana ndi chiganamba cha nkhono. Kodi zimenezi zimatheka bwanji?

Amatsegula malo awiri m’mbali mwa chiganamba cha nkhonozi ndikuikamo kamwala kapena kachitsulo ndipo amachitanso zimenezi pamsana pake. M’kupita kwa nthawi nkhonoyi imatulutsa timadzi timene timakuta timiyalati. Pakatha miyezi pafupifupi 18, nkhonoyi imakhala itatulutsa timadziti mobwerezabwereza ndipo kangale kakang’ono kamapangika. (Onani bokosi lili m’munsili.) Koma zimatenga pafupifupi zaka 6 kuti ngale yaikulu ipangike. Pa nkhono 50 za mtundu wa paua ndi pafupifupi imodzi yokha imene imatha kupanga ngale yapamwamba kwambiri. Ngale imeneyi imakhala yosalala ndiponso yonyezimira kwambiri.

Akatswiri ofufuza sanapezebe njira yopangira ngale zobulungira pogwiritsa ntchito nkhono. Zimenezi zili choncho chifukwa chakuti nkhono za paua zili ndi mnofu winawake m’mimba mwake umene umathandiza nkhonozi kulavula chinthu chilichonse chobulungira ngati mkanda. Mwina m’tsogolomu munthu wina adzatulukira njira yopangira ngale yobulungira bwino pogwiritsa ntchito nkhono zimenezi.

Komabe, pakali pano tingathe kusangalala ndi zinthu zochuluka kuchokera ku nkhonoyi monga mikanda yokongola, ziganamba zake zokongola kwambiri komanso nyama yake youtsa mudyo. Ndithudi tiyenera kuthokoza kwambiri Mulungu chifukwa chotipatsa mphatso yabwino kwambiri imeneyi.—Yakobe 1:17.

[Bokosi/Chithunzi pamasamba 24, 25]

ZIGANAMBA ZAKE N’ZOLIMBA KWAMBIRI

Ziganamba za nkhono za paua zimapangidwa ndi mchere wooneka ngati laimu. Mchere umenewu ndi umenenso amagwiritsa ntchito popanga choko. Komabe, chiganamba cha nkhono zimenezi n’cholimba kwambiri kuposa choko.

Nkhonozi zimapeza mcherewu kuchokera m’madzi a m’nyanja ndipo umakuta mkati mwa chiganambacho. Zimenezi zimachititsa kuti chiganambacho chikhale cholimba komanso chokongola kwambiri.

Asayansi alephera kutengera mmene chiganamba cha nkhonozi chimapangidwira. Chiganambachi chili ndi njira zosachepera zisanu zothandiza kuti chisasweke ndipo chimatha kudzikonza chokha chikathetheka. Ndithudi, nkhono za paua zinalengedwa modabwitsa kwambiri.

[Mawu a Chithunzi]

© Humann/​gt photo

[Mawu a Chithunzi patsamba 23]

Top left: © K.L. Gowlett-Holmes; top right: Marcus Byrne/​Photographers Direct

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Silverdale Marine Hatchery, New Zealand