Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nyengo Imene Dzuwa Silituluka

Nyengo Imene Dzuwa Silituluka

Nyengo Imene Dzuwa Silituluka

YOLEMBEDWA KU FINLAND

BAIBULO limanena kuti: “Dzuwa lituluka, nililowa, nilifulumira [kubwerera] komwe linatulukako.” (Mlaliki 1:5) Komabe, ku madera ambiri a kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi, ku Arctic Circle, dzuwa silituluka kuyambira pakati pa mwezi wa November mpaka kumapeto kwa mwezi wa January. M’nyengo yachisanu, kumadera amenewa kumakhala mdima.

Nthawi zina zimenezi zimachitikanso ku madera a kum’mwera kwa Arctic Circle. Mwachitsanzo, madera omwe ali pamtunda wa makilomita 800 kum’mwera kwa Arctic Circle, kunja kumakhala dzuwa kwa maola 6 okha m’nyengo yachisanu. Madera amenewa ndi mizinda ya St. Petersburg, ku Russia; Helsinki, ku Finland; Stockholm, ku Sweden; ndi Oslo, ku Norway.

Munthu wina dzina lake Ari, amene wakulira m’mzinda wa Kiruna kumpoto kwa Sweden, anati: “Si zoona kuti m’nyengo yachisanu ku Arctic kumakhala mdima wandiweyani.” Nthawi zambiri masana kumakhala “chisisira.” Paula, yemwe amajambula zithunzi ndipo amakhala kumpoto kwa Finland, anati: “Kudera lino kukakhala chipale chofewa, kunja kumaoneka mbuu.”

Nyengo yachisanu imene kumakhala mdima kwambiri imadwalitsa anthu ena. Wolemba nyimbo wina wotchuka wa ku Finland, dzina lake Jean Sibelius, analemba kuti: “Ndimadwala kwambiri nyengo ikamasintha.” Iye anawonjezera kuti: “Nthawi zonse mu nyengo yachisanu, imene tsiku limakhala lalifupi, ndimavutika maganizo.” Si Sibelius yekha amene amavutika ndi matenda amenewa m’nyengo yachisanu. Ngakhale katswiri wina wachigiriki, Hippocrates (amene anakhalako kuyambira cha m’ma 460 mpaka cha m’ma 377 B.C.E.), ankakhulupiriranso kuti nyengoyi imapangitsa anthu kudwala matenda a maganizo.

Komabe, kuyambira cha m’ma 1980 m’pamene anthu anazindikira kuti matendawa amabweradi chifukwa cha nyengoyi. Ochita kafukufuku apeza kuti pa anthu a m’madera amenewa ndi anthu ochepa chabe amene amadwala ndi kusintha kwa nyengo. Matenda ena a mtundu umenewu, koma osaopsa kwambiri, ndi amene ali ofala. Ndipo matenda amenewa ndi amene anthu ambiri amadwala.

Andrei, wa ku St. Petersburg, m’dziko la Russia, ananena kuti, “Ndimafuna kumangogona nthawi zonse.” Annika, amene amakhala ku Finland, amakhumudwa nyengo yachisanu ikayandikira. Iye anati: “Nthawi zina mdima umandidwalitsa kwambiri chifukwa timasowa kothawira.”

Akatswiri amafotokoza njira zambiri zimene zingathandize munthu kupirira matenda a maganizo. Mwachitsanzo, ena amanena kuti wodwalayo azikonda kukhala panja masana. Iwo amanenanso kuti anthu amene amagwira ntchito zapanja m’nyengo yachisanu sadwaladwala matenda amenewa.

Jarmo amene wakhalapo kumpoto komanso kum’mwera kwa Finland mu nyengo yachisanu, ananena kuti, “Kukakhala mdima wandiweyani, timayatsa makandulo ndiponso nyali zambiri.” Anthu ena odwala matenda amenewa, amachira akawaika pamalo owala kwambiri. Ndipo ena amayamba achoka kaye m’malo amenewa n’kupita kumayiko a kum’mwera kwambiri kwa dzikoli. Komabe, ena amachenjeza kuti anthu akachoka ku malo a dzuwa amenewa n’kubwerera kwawo kumene kumakhala mdima m’nyengo yachisanu, amatha kudwala kwambiri.

Kudya zakudya zoyenera n’kofunikanso. Dzuwa limathandiza kuti m’thupi mukhale vitamini D, ndipo ngati kunja kulibe dzuwa vitamini imeneyi imachepa m’thupi. Choncho, anthu ena amanena kuti m’nyengo yachisanu ndi bwino kumadya chakudya chimene chili ndi mavitamini amenewa, monga nsomba, chiwindi ndiponso mkaka.

Chimene chimachititsa nyengoyi kukhala ya mdima n’chimenenso chimachititsa kuti kunja kukhale dzuwa. Dziko likamazungulira madera ozizira amayamba kuyang’ana kumene kuli dzuwa. Ndipo pang’onopang’ono dzuwa limayamba kuoneka kwambiri masana. Ndiyeno imafika nyengo yotentha, imene anthu amasangalala ndi dzuwa mpaka pakati pa usiku.

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Nthawi zambiri masana kumakhala “chisisira”

[Chithunzi patsamba 26]

Masana m’nyengo yachisanu ku Arctic

[Mawu a Chithunzi]

Dr. Hinrich Bäsemann/​Naturfoto-Online

[Chithunzi patsamba 26]

Anthu ambiri amadwala chifukwa cha kusowa kwa dzuwa