Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Anthu Ambiri Amakonda Pizza

Anthu Ambiri Amakonda Pizza

Anthu Ambiri Amakonda Pizza

YOLEMBEDWA KU ITALY

MFUMU Ferdinand Woyamba (anabadwa mu 1751 ndipo anamwalira mu 1825) anayenda mozemba atavala ngati munthu wamba n’kupita kudera la anthu osauka la mumzinda wa Naples, ku Italy. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Akuti ankafuna kukadya nawo chakudya chimene mkazi wake analetsa kuti chisamapezeke ku nyumba yachifumu. Chakudya chake chinali pizza.

Mfumuyi ikanakhala kuti ilipobe masiku ano si bwenzi ikuvutikanso chonchi kuti ipeze pizza. Panopo ku Italy kuli malo pafupifupi 30,000 ophikira pizza ndipo amaphika pizza wambiri moti munthu aliyense wa kumeneku angapeze pizza pafupifupi 45 pachaka.

Chinali Chakudya cha Anthu Osauka

Zikuoneka kuti pizza anachokera ku Naples cha mu 1720. Panthawi imeneyi, anthu osauka ndi amene ankadya pizza ndipo chinali chakudya chosavuta kuphika chomwe chinkagulitsidwa m’malesitilanti komanso malo ena. Anthu ambiri ogulitsa pizza ankayendayenda m’misewu uku akuitanira malonda awo. Kuti pizza akhalebe wotentha ankamuika m’mabeseni achitsulo otchedwa scudo amene anthu ogulitsawa ankasenza.

Kenako mfumu Ferdinand Woyamba anadziwitsa anthu a kunyumba yachifumu kuti amakonda kwambiri pizza. Pasanapite nthawi anthu ambiri anayamba kukonda pizza. Ndipo ngakhale anthu olemera, otchuka ngakhalenso a m’banja lachifumu anayamba kupita kumalo ophikira pizza. Mdzukulu wa mfumu Ferdinand yemwe ankatchedwa kuti mfumu Ferdinand Wachiwiri anachita kumangitsa uvuni wophikira pizza ku nyumba yachifumu ya ku Capodimonte mu 1832. Motero alendo ake olemekezeka akabwera ankasangalala.

Kodi Pizza ndi Chakudya Chopatsa Thanzi?

Masiku ano achinyamata ambiri amakonda pizza koma m’pofunika kusamala. Kuti pizza akhale wopatsa thanzi ayenera kukhala ndi zakudya zopatsa mphamvu, zomanga ndi kukulitsa thupi, mafuta, mavitamini komanso zinthu zina zofunika m’thupi. M’pofunikanso kuikamo mafuta a maolivi amene amathandiza kuti m’thupi muzikhala mapuloteni otchedwa HDL amene akatswiri amati “ndi abwino chifukwa chakuti amayeretsa mitsempha.”

Komanso pizza akaphikidwa bwino, thupi limam’gaya mosavuta. Chifukwa chimodzi n’chakuti pokanda ufa wophikira pizza madzi ambiri amalowerera mu ufawo. Komanso pizza amakhutitsa msanga chifukwa cha ufa umene amapangirawo moti ngakhale anthu amene amam’konda kwambiri amalephera kudya wambiri.

Mukamadya pizza muzikumbukira kuti poyamba chinali chakudya cha anthu osauka. Komanso muziyamikira kuti mfumu Ferdinand Woyamba sanabise zoti amakonda kwambiri pizza.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]

Pizza amapsa bwino mu uvuni wa nkhuni. Utsi wa muuvuni umachititsa kuti akhale wonunkhira bwino ndipo kaphulusa kotentha kamene kamakhala pansi pa uvuniwo, kamathandizanso kuti akhale wokoma kwambiri.

▪ Mu 1990, anapanga pizza wamkulu kwambiri padziko lonse. Anali wozungulira ndipo atayeza pakati anapeza kuti anakwana mamita 37 ndipo ankalemera makilogalamu oposa 12,000.

▪ Kuyambira kale, anthu akamapanga pizza amaponya m’mwamba chimbamu chake n’kumachizunguza. Sikuti amachita zimenezi pofuna kungosangalatsa anthu koma amafuna kuti chiphwaphwatike ngati chitumbuwa n’kupanga pizza.

[Chithunzi chachikulu patsamba 26]