Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Madzi Opatsa Moyo

Madzi Opatsa Moyo

Madzi Opatsa Moyo

Nthawi ina, Yesu ali paulendo, anadutsa m’dera la Samariya lomwe linali kumpoto kwa Yerusalemu. Iye anali atatopa komanso anali ndi ludzu. Kenako, anakhala pa chitsime n’kupempha mayi wina wachisamariya kuti amupatse madzi. Mayiyu anadabwa kwambiri kuti Myuda akumupempha madzi chifukwa panthawiyo, Ayuda ndi Asamariya sankagwirizana.

Mayiyu anafunsa Yesu modabwa, kuti: “Popeza inu ndinu Myuda, mukupempha bwanji madzi akumwa kwa ine, mayi Wachisamariya?”

Yesu anayankha kuti: “Mukanadziwa mphatso yaulere ya Mulungu ndi amene akukuuzani kuti, ‘Mundipatseko madzi akumwa,’ mukanam’pempha iyeyo, ndipo akanakupatsani madzi amoyo.”

Yesu anapitiriza kuuza mayiyo kuti: “Aliyense wakumwa madzi awa adzamvanso ludzu. Koma amene adzamwa madzi amene ine ndidzam’patse sadzamvanso ludzu mpang’ono pomwe, ndipo madzi amene ndidzam’patse, adzasanduka kasupe wa madzi otumphuka mwa iye opatsa moyo wosatha.”—Yohane 4:1-15.

Kodi pamenepa Yesu ankanena madzi otani?

BAIBULO limanena kuti Mlengi wathu, Yehova Mulungu, ndi “kasupe wa madzi amoyo.” (Yeremiya 2:13) Moyo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu. Ndipo kuti tipitirize kukhala ndi moyo, tiyenera kumwa madzi amene iye amapereka, enieni ndi auzimu omwe.

Masiku ano, kuposa kale lonse, anthu akufunafuna mayankho a mafunso ofunikira kwambiri. Motero, tinganene kuti anthu padziko lonse ali ndi ludzu lauzimu. Anthu akufunafuna mayankho amafunso monga akuti: Kodi akufa ali kuti? Kodi n’zotheka kudzawaonanso? N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika? Kodi nkhondo, ziwawa, njala ndiponso matenda zidzatha? Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti mayankho a mafunso amenewa amapezeka ‘m’madzi’ otsitsimula, omwe ndi Mawu a Mulungu, Baibulo.

Pamene Yesu ankalankhula ndi mayi wachisamariya pachitsime, ankanena za madzi opatsa moyo, omwe ndi choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu. Mboni za Yehova zikukulimbikitsani kuti mulawe madzi a choonadi amenewa. Zimenezi ndi zimenenso buku lomalizira la m’Baibulo likukulimbikitsani kuchita. Bukuli limati: “Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.”—Chivumbulutso 22:17.

Kuti mudziwe zambiri za m’mene Ufumu wa Mulungu udzathandizire anthu, kaonaneni ndi Mboni za Yehova ku Nyumba ya Ufumu yakufupi ndi kumene mumakhala. Mungawalemberenso kalata pogwiritsa ntchito adiresi yoyenera pa maadiresi omwe ali patsamba 5 la magazini ino. Mungafufuzenso pa adiresi yathu pa Intaneti iyi: www.pr418.com.

[Bokosi pamasamba 8, 9]

KODI ZIPEMBEDZO ZATHETSA LUDZU LA CHOONADI?

Munthu sangapeze madzi otsitsimula a choonadi mwa kumangopita kutchalitchi kapena kumangonena kuti ndi wopemphera. Zoona zake n’zakuti, zipembedzo zambiri masiku ano zaonjezera mavuto a anthu m’malo mowathetsa. Mwachitsanzo, panthawi ya nkhondo, Akatolika amapha Akatolika anzawo, Apolotesitanti nawonso amapha Apolotesitanti anzawo ndipotu onsewa amakhala atapemphera kwa Mulungu kuti awathandize pa nkhondozo.

Komanso pali malipoti ambiri osonyeza kuti atsogoleri a mipingo amaba ndalama zatchalitchi ndiponso amachita zachiwerewere ndi ana. Kunena zoona, madzi amene zipembedzo zambiri zimapatsa anthu awo ndi oipa. (Chivumbulutso 17:4-6; 18:1-5) Zimenezi zikufanana ndi zimene Baibulo limanena pa Tito 1:16, kuti: “Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu, koma amam’kana ndi ntchito zawo.” Nthawi ino pamene padziko lonse pali chilala chauzimu, zipembedzo zambiri zalephera kupatsa anthu awo madzi a choonadi.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

Buku la mitu 19, lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lomwe lili ndi masamba 224, lili ndi mayankho a m’Baibulo a mafunso ofunika kwambiri monga akuti:

“Kodi Mulungu ali nalo cholinga chotani dziko lapansili?”

“Kodi akufa ali kuti?”

“Kodi tili ‘m’masiku otsiriza?’”

“N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthu azivutika?”

[Chithunzi patsamba 9]

Mungapeze ‘madzi achoonadi’ ku Nyumba ya Ufumu ya m’dera lanu