Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

▪ “M’zaka za m’ma 1900, anthu pafupifupi 100 miliyoni anafa chifukwa chosuta fodya.”—WORLD HEALTH ORGANIZATION, SWITZERLAND.

▪ “Pa anthu pafupifupi 9000 amene anachitidwa opaleshoni ku [United Kingdom] kuyambira m’chaka cha 1996 mpaka 2003, ambiri mwa anthu amene analandira maselo ofiira a m’magazi, akanatha kumwalira m’chaka chotsatira kapenanso pasanathe masiku 30 atachitidwa opaleshoni poyerekezera ndi amene sanaikidwe magazi.”—NEW SCIENTIST, BRITAIN.

Kodi Khirisimasi ndi Nthawi ya Mtendere?

Magazini ina ya makolo ya ku Sweden inati: “Khirisimasi ndi umodzi mwa miyambo yathu ikuluikulu.” Koma magaziniyi inanenanso kuti ‘nthawiyi imakhala ya mikangano.’ Ndipotu panthawi ya Khirisimasi mabanja “amamenyana kuposa panthawi ina iliyonse pachaka.” Magaziniyi inafunsa makolo oposa 1,100 amene ali ndi ana aang’ono kuti anene zimene zimachitika panthawi ya Khirisimasi. Pafupifupi anthu 88 pa 100 alionse anayankha kuti banja lawo limakangana pankhani yoti “adya chiyani komanso akadyera kuti Khirisimasi.” (Vi Föräldrar) Makolo ambiri amakhumudwa chifukwa agogo amagulira zidzukulu zawo maswiti komanso mphatso zosayenera.

Kupatsa Kumabweretsa Chimwemwe

Nyuzipepala ina ya ku Canada inali ndi mutu wankhani wakuti: “Munthu wa ndalama amakhala wosangalala ngati apatsako ena.” Anthu ambiri amene anafunsidwa pa kafukufuku wina ankaganiza kuti angakhale osangalala ngati atadya okha ndalamazo, koma amene anagwiritsa ntchito ndalama zawo pothandiza anthu ena, mosayang’ana kuti agwiritsa ntchito ndalama zingati, ndi amene anapezeka kuti anali osangalala kwambiri. Nyuzipepalayi inanenanso kuti: “Nthawi zambiri akachita kafukufuku amapeza kuti kulemera si chizindikiro chakuti munthu akusangalala. Ngati munthu ali ndi ndalama zokwanira kupeza zinthu zofunika pamoyo, kulimbana ndi kupeza zambiri sikungamuthandize kukhala wosangalala.”—The Globe and Mail.

Zikupezeka pa Intaneti

Akuluakulu aboma la United States aganiza zofufuza ngati adani awo “angapeze [pa Intaneti] zida za nkhondo zimene zimapezeka ndi anthu oona za chitetezo okha,” inatero magazini ina. “Iwo anadabwa kuona kuti kunali kosavuta kupeza zinthu zimenezi.” Pogwiritsa ntchito malo odziwika bwino ogulitsirapo malonda a pa Intaneti, ofufuzawo amatha kugula “zinthu za ku United States zodzitetezera pankhondo.” Amathanso kugula “zitsulo za ndege zankhondo, zinthu zakale zodzitetezera ku tizilombo tofalitsa matenda ndiponso zinthu zina zoopsa.” Sizikudziwika kuti ogulitsawo amazipeza bwanji zida zimenezi moti ambiri “akuimbidwa milandu,” inatero magaziniyo.—New Scientist.

Zomatira Zakale Kwambiri

Kale, ankamata maluwa okongola ku zipewa za akuluakulu a boma la Roma pogwiritsa ntchito zomatira zamphamvu ngati zamasiku ano. Frank Willer, yemwe anali mkulu wa okonza nyumba zakale kwambiri pa malo akale osungiramo zinthu a ku Rhineland Museum ku Bonn, Germany, anatulukira zimenezi mwangozi. Anagwiritsa ntchito kochekera kakang’ono pochotsa kachitsulo ku chipewa cha m’zaka 100 zoyambirira chomwe chinakhala mu mtsinje wa Rhine kwa zaka pafupifupi 1,500. Iye ananena kuti: “Kutentha kwa chochekeracho kunachititsa kuti masamba omwe anali pachipewacho amatuke, kungotsala zizindikiro za zomatirazo.” Kafukufuku wasonyeza kuti zomatirazi zinapangidwa ndi phula, utomoni, ndi mafuta a nyama.