Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dziko Lili pa Malo Abwino Kwambiri Mumlengalenga

Dziko Lili pa Malo Abwino Kwambiri Mumlengalenga

Dziko Lili pa Malo Abwino Kwambiri Mumlengalenga

DZIKOLI pamodzi ndi mayiko ena zimayenda mozungulira dzuwa. Zonsezi zili mkati mwa mlalang’amba. Chifukwa cha kupita patsogolo kwa sayansi ya zakuthambo ndi sayansi ya kapangidwe ka zinthu, akatswiri a sayansi adziwa zinthu zozama kwambiri zokhudza kadera kakang’ono kamene pali dziko lathuli mumlengalenga.

Choyamba n’chakuti dzikoli pamodzi ndi mayiko ena ozungulira dzuwa zili m’chigawo chabwino kwambiri mumlalang’amba (wotchedwa Milky Way), choyenerera zinthu zamoyo. Kuchokera pakati pa mlalang’ambawu kufika m’chigawo chimenechi pali mtunda wautali ndithu. Moti kuwala kochokera pakati pa mlalang’ambawu kungathe zaka pafupifupi 28,000 kuti kufike m’chigawochi. M’chigawochi muli zinthu zonse zothandiza kuti zamoyo zikhalepo ndipo zinthuzi zili pamlingo woyenerera. Zinthu zimenezi n’zosowa kwambiri mukamatalikirana ndi chigawo chimenechi kulowera kunja kwa mlalang’ambawu. Komanso mukamalowera cha mkati mwa mlalang’ambawu mumafika m’chigawo chinachake chimene muli cheza choopsa kwambiri ndi zinthu zinanso zoopsa. Magazini ina inati: “Dziko lathuli lili pa malo abwino kwambiri kuposa malo ena alionse mumlengalenga.”—Scientific American.

Limayenda “Mumsewu” Wabwino Kwambiri

Njira imene dziko limayenda pozungulira dzuwa ndi yabwino kwambiri. Malo amene dziko limadutsa ali pamtunda wa makilomita pafupifupi 150 miliyoni kuchokera ku dzuwa. Mtunda umenewu ndi woyenera kuti zamoyo zikhalepo chifukwa si malo ozizira kwambiri kapena otentha kwambiri. Dziko limatenga chaka kuti lizungulire dzuwa ndipo likamazungulira silitalikira kwambiri kapena kuyandikira kwambiri dzuwalo.

Dzuwa nalonso lili ndi mphamvu imene imathandizanso kuti dziko likhale labwino. Silisunthasuntha, ndi lalikulu bwino komanso limatulutsa mphamvu zake pamlingo woyenera. Chifukwa cha zimenezi, anthu ena amati dzuwa “si nyenyezi wamba.”

Mwezi Umalithandiza

Mwezi uli pafupi kwambiri ndi dzikoli ndipo umalithandiza kwambiri. Mwezi ndi wocheperapo poyerekezera ndi dziko moti ungalowe kanayi m’dzikoli. Komabe pali mayiko ena omwe ali ndi miyezi yaing’ono kwambiri poyerekezera ndi kukula kwa mayikowo. Izitu sikuti zinangochitika mwangozi.

Choyamba, mwezi umachititsa kuti madzi a m’nyanja zikuluzikulu azisinthasintha kayendedwe kawo, motero zinthu zachilengedwe zimakhala bwinobwino m’dzikoli. Mwezi umathandizanso kuti dziko lizitha kumazungulira bwinobwino ngati nguli. Pakanapanda mwezi dzikoli bwenzi likumayenda mwapendapenda pozungulira dzuwa, moti zikanasokoneza kwambiri nyengo, kayendedwe ka madzi m’nyanja komanso zinthu zina zambiri.

Linapendekeka Bwino Komanso Limazungulira Bwino

Dzikoli linapendekeka bwino ndipo izi zimachititsa kuti nyengo izisinthasintha pachaka. Zimenezi zimachititsanso kuti lisamatenthe kwambiri kapena kuzizira kwambiri komanso kuti madera osiyanasiyana azikhala ndi nyengo zosiyanasiyananso. Buku lina linati: “Zikuoneka kuti dzikoli linapendekeka m’njira yoyenerera kwambiri kuti padziko pano pakhale zamoyo.”—Rare Earth—Why Complex Life Is Uncommon in the Universe.

Dzikoli likamazungulira ngati nguli, limazungulira pa liwiro loyenerera kuti usana ndi usiku usamatalike kapena kufupika kwambiri. Likanakhala kuti limazungulira pang’onopang’ono, bwenzi mbali imene yayang’ana kudzuwa ikutentha kwambiri pomwe mbali inayo bwenzi ikuzizira modetsa nkhawa. Ndipo likanakhala kuti limafulumira kwambiri bwenzi kukuchitika chimphepo chadzaoneni komanso zinthu zina zoopsa kwambiri.

Pamenepa tingathe kuona kuti zinthu zonse zokhudza dzikoli, kungoyambira malo amene lilipo mumlengalenga, mmene limazungulilira komanso mwezi wake, zimapereka umboni wakuti pali Mlengi wanzeru woganiza mozama amene analipanga mwaluso. * Paul Davies, yemwe ndi katswiri wa sayansi ya kapangidwe ka zinthu komanso amakhulupirira zoti zinthu zinangokhalapo zokha, anati: “Ngakhale asayansi amene amati kulibe Mulungu amagoma akaganizira za ukulu, kudabwitsa, kugwirizana, kukongola, ndiponso luso lapamwamba limene limaoneka m’chilengedwe chonse.”

Kodi zinthu zochititsa chidwi zonsezi zinangokhalapodi mwangozi kapena zinachita kupangidwa mwanzeru? Ganizirani funso limeneli pamene mukuwerenga nkhani yotsatirayi, imene ikufotokoza zinthu ziwiri zimene zimateteza zamoyo padziko pano kuti zisawonongedwe ndi zinthu zoopsa za mumlengalenga.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Chilengedwe chonsechi kuti chikhalepo m’pofunika mphamvu za mitundu inayi zimene zimagwira ntchito pa zinthu zonse za m’chilengedwe. Zina mwa mphamvu zimenezi zimakoka zinthu, zina zimakankha, ndipo zina zimatulutsa mphamvu yangati yamagetsi. Mphamvu zonsezi zimagwira ntchito mogwirizana, iliyonse pamlingo woyenera.—Onani mutu 2 wa buku lakuti Is There a Creator Who Cares About You?, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Bokosi patsamba 5]

KODI MULI PA LIWIRO LOPOSA LA CHIPOLOPOLO?

Mukamamaliza kuwerenga kabokosi aka, mukhala mutayenda ulendo wautali zedi koma wopanda mabampu. Taganizirani izi:

Dziko ndi lobulungira ndipo ulendo wozungulira dzikoli ndi wautali makilomita 40,000. Koma likamazungulira ngati nguli, limatenga maola 24 kuti limalize kutembenuka. Motero munthu amene ali m’dera lapakati penipeni pa dzikoli amakhala pa liwiro la makilomita 1,600 pa ola limodzi. (Koma munthu amene ali m’dera la kumpoto kwenikweni kapena kum’mwera kwenikweni kwa dzikoli amangozungulira pamalo amodzimodzi.)

Komanso dziko palokha limayenda mozungulira dzuwa pa liwiro la makilomita 30 pa sekondi iliyonse. Nalonso dzuwa limodzi ndi mayiko ena onse olizungulira amayenda mozungulira m’mlalangamba pa liwiro la makilomita 249 pa sekondi. Ili ndi liwiro lalikulu kwambiri poyerekezera ndi chipolopolo chomwe chimayenda pafupifupi kilomita imodzi yokha pa sekondi.

[Mawu a Chithunzi patsamba 4]

Milky Way: NASA/JPL/Caltech

[Mawu a Chithunzi patsamba 5]

Earth: Based on NASA/Visible Earth imagery