Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Dzikoli Lili ndi Zamoyo Zochuluka

Dzikoli Lili ndi Zamoyo Zochuluka

Dzikoli Lili ndi Zamoyo Zochuluka

DZIKOLI lili ndi zamoyo zankhaninkhani mwina zoposa mamiliyoni ambirimbiri. Zambiri zimakhala m’dothi, mumpweya ndi m’madzi ndipo ndi zoti sitingazione ndi maso paokha. Mwachitsanzo, ofufuza ena anapeza kuti dothi lokwana sipuni imodzi yokha limatha kukhala ndi tizilombo tamitundu 10,000, kuphatikizaponso mitundu ina yosiyanasiyana ya tizilombo tosaoneka ndi maso. Ndipo pali mitundu ina ya tizilombo timene timakhala pamtunda wa makilomita atatu kupita pansi panthaka.

M’mlengalenga mulinso zamoyo zochuluka, kuphatikiza pa mbalame, mileme ndi tizilombo tina touluka. Ndipo m’nyengo ina pachaka, m’mlengalenga mumadzaza mungu ndi timbewu tosiyanasiyana. Ndipo m’madera ena, m’mlengalenga mumadzaza tizilombo tochuluka tosaoneka ndi maso. Magazini ina inati: “Mumpweya muli tizilombo tochuluka kwambiri mofanana ndi timene tili m’nthaka.”—Scientific American.

Sitikudziwa kuti m’nyanja muli zamoyo zochuluka motani, chifukwa kufufuza zam’nyanja kumafuna ndalama zambiri. N’kutheka kuti ngakhale m’malo a pansi pa nyanja, omwe anthu amapitamo mosavuta pofufuza zinthu, muli zamoyo zokwana mamiliyoni ambirimbiri zimene sizinadziwikebe.

Komabe zimene tikudziwa ndi zakuti, dzikoli lili ndi zamoyo zankhaninkhani moti pakanapanda zamoyo zimenezi sibwenzi mpweya, madzi ndiponso nthaka zili bwinobwino. Mwachitsanzo, zigoba za tizilombo takufa ndiponso timapiri ta pansi panyanja topangidwa ndi zamoyo zing’onozing’ono zimathandiza kwambiri kuti madzi azikhala oyera. Bungwe lina linati zinthu zimenezi zimayeretsa madzi m’nyanja “monga mmene mankhwala enaake amatsukira m’mimba.” M’nyanja muli zomera zosiyanasiyana. Zina ndi zazing’ono kwambiri ndipo zimayandama pamwamba pa madzi. Zomera zimenezi zimathandiza kuti mpweya wabwino umene timapuma ndiponso mpweya umene timatulutsa ukhale pa mlingo woyenerera m’madzi ndi mumlengalenga. Komanso m’dothi muli tizilombo ting’onoting’ono timene timawoletsa zinthu kuti zisanduke manyowa omwe zomera zimagwiritsa ntchito. Kunena zoona dzikoli lili ndi zamoyo zambiri.—U.S. National Oceanic and Atmospheric Administration.

Komatu padziko pano sipangakhale zamoyo pakanapanda zinthu zina zogometsa zokhudza dzikoli zimene akatswiri a sayansi azitulukira posachedwapa. Zina mwa zinthu zimenezi ndi izi:

1. Dziko lili pamalo abwino kwambiri mu mlalang’amba wa Milky Way ndiponso latalikirana bwino ndi dzuwa komanso mapulaneti ena. Chinanso limadutsa m’njira yabwino pozungulira dzuwa, linapendekeka bwino, limazungulira moyenerera komanso lili ndi mwezi

2. Dziko limatetezedwa ndi mlengalenga komanso nyesi yake

3. Dziko lili ndi madzi ochuluka

4. Kayendedwe ka madzi, mpweya ndi zinthu zina kamathandiza kubwezeretsa zinthu zofunika komanso kuchotsa zinthu zoipa

Zinthu zonsezi tazifotokoza m’nkhani zotsatirazi, ndiye mukamawerenga dzifunseni kuti: ‘Kodi dzikoli linangokhalako mwangozi kapena pali winawake wanzeru amene analilenga? Ngati pali winawake amene analilenga, kodi analilenga ndi cholinga chotani?’ Nkhani yomaliza ndi imene iyankhe funso limeneli.

[Bokosi patsamba 3]

“IFEYO SITINGAVOMEREZE ZOTI KULI MLENGI”

Ngakhale kuti zachilengedwe zimasonyeza kuti n’zopangidwa mwaluso kwambiri, asayansi ambiri amatsutsa zoti kuli Mlengi. Wasayansi wina, dzina lake Richard C. Lewontin, yemwe amakhulupirira kuti zinthu sizinachite kulengedwa, ananena kuti si mfundo zimene asayansi atulukira zimene zimachititsa kuti anthu ena azitsutsa “zoti zinthu zinachita kulengedwa.” M’malo mwake, iye anati, anthuwa amatero chifukwa choti “anasankha kale kuti aziyendera mfundo yoti kulibe Mlengi,” ndipo amayesetsa kupeza umboni wotsimikizira mfundo yawoyi. Poyankhula moimira maganizo asayansi anzake, iye anatinso, “mfundo yoti zinthu sizinachite kulengedwa ndi yosatsutsika chifukwa choti ifeyo sitingavomereze zoti kuli Mlengi.”

Kodi n’chinthu chanzeru kukakamira maganizo amenewa ngakhale kuti pali umboni wosatsutsika wakuti kuli Mlengi? Kodi inuyo mukuganiza bwanji pankhaniyi?—Aroma 1:20.