Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndimuiwale?

Kodi Ndingatani Kuti Ndimuiwale?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Ndimuiwale?

“Tinakhala pachibwenzi kwa miyezi 6 ndipo tinali titadziwana kwa zaka 5. Koma atayamba kuganiza zothetsa chibwenzicho, zinam’vuta kwambiri kuti andiuze. Motero anangosiya kundilankhulitsa. Ndinathedwa nzeru kwambiri ndi zimenezi. Zinandisokonezeratu maganizo. Ndinkangodzifunsa kuti, ‘Kodi ndinam’lakwira chiyani?’”—Anatero Rachel. *

CHIBWENZI chikatha mungakhumudwe kwambiri. Taganizirani zimene zinachitikira Jeff ndi Susan. Iwowa anali pachibwenzi kwa zaka ziwiri. Panthawiyi iwowa ankakondana kwambiri. Patsiku Susan ankalandira mauthenga a pafoni ambirimbiri achikondi ochokera kwa Jeff. Nthawi zambiri ankamupatsanso timphatso tosiyanasiyana tosonyeza chikondi. Susan anati: “Jeff ankamvetsera mwachidwi ndikamamuuza zinthu ndipo ankandimvetsa kwambiri. Osanama ayi, ndikakhala ndi Jeff ndinkadziwa kuti ndine ndekha basi.”

Posakhalitsa, Jeff ndi Susan anayamba kukambirana zomanga banja komanso za komwe angakakhale akadzakwatirana. Jeff anafika pofunsa za saizi ya mphete yoti Susan adzavale paukwati wawo. Kenaka, Jeff anangothetsa chibwenzicho mwadzidzidzi. Susan anasokonezeka kwambiri. Tsiku lililonse ankangochita zinthu modzikoka basi. Iye anati: “Zinandifoola nkhongono kwambiri.” *

N’chifukwa Chiyani Zimapweteka

Ngati inunso chibwenzi chanu chinatha, mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ndidzatha kuiwala nkhani imeneyi?’ (Salmo 38:6) M’pomveka kuthedwa nzeru chonchi. N’kutheka kuti limeneli ndilo vuto lalikulu kwambiri limene mwakumanapo nalo pa moyo wanu. Ndipotu anthu ena anenapo kuti kutha kwa chibwenzi sikusiyana kwenikweni ndi imfa. Mwina inunso mukumva mmene munthu amamvera akaferedwa. Zina mwa zimene zingakuchitikireni ndi izi:

Kusamvetsa. ‘Zimenezi n’zosatheka ayi, asintha maganizo mawa kapena mkucha uno.’

Kukwiya. ‘Sanganditero ine. Panopo sindikufuna n’komwe kuona nkhope yake!’

Kudzimvera chisoni. ‘Palibe amene angakonde munthu ngati ine.’

Kuvomereza. ‘M’pofunika kungolimba nazo basi. Zinkandiwawa kwambiri poyamba paja, koma panopo ndayamba kuiwalako.’

Nkhani yabwino ndi yakuti mungathe kufika povomereza kuti zagwa zatha basi n’kuiwala nkhaniyi. Koma pali zinthu zingapo zimene zingachititse kuti zimenezi zitheke mwamsanga. Zina mwa izo ndi zinthu monga nthawi imene munakhala pachibwenzi, ndiponso pamene chibwenzicho chinafika. Komano kodi pakali pano mungatani ngati zikukupwetekani kwambiri?

Musafooke

Dziwani kuti pakapita nthawi mudzaiwala nkhaniyo. Mwina mawu amenewa sangakulimbikitseni chibwenzi chanu chikangotha kumene. N’zoona kuti mungadzaiwale pakadutsa nthawi komabe pali zina zimene muyenera kuchita panopa. Mwachitsanzo: Ngati muli ndi chilonda mumadziwa kuti pakapita nthawi chidzapola koma panopo chingamakupwetekeni kwambiri. Motero m’pofunika kuletsa magazi kuti asatayike komanso kuti musamve ululu kwambiri. Muyeneranso kuyesetsa kuti tizilombo toyambitsa matenda tisalowe pachilondacho. Izinso n’zimene zimachitika munthu akakhumudwitsidwa. Panthawi imene zangochitikayo zimakhala zopweteka kwambiri. Koma mukhoza kuchita zinthu zina zimene zingachepetse ululuwo komanso kuti musachite zinthu zina chifukwa cha kupsa mtima. N’zoona kuti pakapita nthawi mudzaiwala nkhaniyo koma panopo chitanipo mbali yanu. Tayesani izi:

Lirani. Kulira si kulakwa. Ndipo Baibulo limanena kuti pali “mphindi yakugwa misozi” komanso “mphindi yakulira.” (Mlaliki 3:1, 4) Kulira sikutanthauza kuti ndinu munthu wopepera. Davide anali msilikali wolimba mtima kwambiri, koma atapanikizika panthawi inayake anavomereza kuti: “Ndiyandamitsa kama wanga usiku wonse; mphasa yanga ndiolobza ndi misozi yanga.”—Salmo 6:6.

Samalirani thanzi lanu. Ngati chibwenzi chatha muyenera kuchita masewero olimbitsa thupi komanso kudya chakudya chabwino kuti musafooke kwambiri chifukwa chodandaula. Pajatu Baibulo limati: “Chizolowezi chochita masewero olimbitsa thupi chipindulitsa.”—1 Timoteyo 4:8.

Kodi muyenera kuchita zinthu ziti kuti mukhale ndi thanzi labwino?

․․․․․

Muzitanganidwa ndi zinthu zina. Musasiye kuchita zinthu zimene zimakusangalatsani. Komanso musayese dala kudzipatula makamaka panthawi inoyo. (Miyambo 18:1) Kucheza ndi anthu amene amakuganizirani kungakuthandizeni kuti muziganizira zinthu zina.

Kodi inuyo mukufuna kuti muzitanganidwa ndi zinthu ziti?

․․․․․

Pempherani ndipo muuzeni Mulungu mmene mukumvera. Izi si zophweka ayi. Anthu ena chibwenzi chawo chikatha amaona ngati kuti Mulungu wawataya. Amatero chifukwa amaganiza kuti, ‘Ine ndakhala ndikupemphera kwanthawi yaitali kuti ndipeze munthu woti ndimange naye banja, moti sindimayembekezera zimenezi ngakhale pang’ono.’ (Salmo 10:1) Komano kodi ndi bwino kuganiza kuti Mulungu ndi amene amachititsa kuti uje ndi uje amange banja? Ayi ndithu si bwino. Ndipo iye si amene amachititsa kuti munthu wina asinthe maganizo pankhani ya chibwenzi. Zoona zake n’zakuti Yehova “amasamala za inu.” (Petulo 5:7) Choncho pempherani kwa iye n’kumufotokozera mmene mukumvera mumtima mwanu. Pajatu Baibulo limati: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatero, mtendere wa Mulungu wopambana luntha lonse la kulingalira, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.

Ngati mukudandaula chifukwa choti chibwenzi chanu chatha, kodi ndi zinthu ziti zimene mungamuuze Yehova?

․․․․․

Yang’anani Zakutsogolo

Mtima wanu ukadzakhazikika mungachite bwino kuganizira zimene zinachitika pachibwenzi chanu. Mukadzakhala okonzeka kuchita zimenezi mudzalembe mayankho a mafunso ali m’munsiwa.

Kodi anakuuzani chifukwa chimene anathetsera chibwenzi? Ngati anakuuzani chilembeni pansipa ngakhale mukuona kuti n’chosamveka.

․․․․․

Kodi pali zifukwa zina zimene mukuona kuti zinachititsa kuti chibwenzicho chithe?

․․․․․

Kodi panopo mukuona kuti pali chinachake chimene mukanachita kuti chibwenzicho chisathe? Ngati zili choncho, ndi chiyani chimene mukanachita?

․․․․․

Kodi kutha kwa chibwenzicho kwakuphunzitsani chiyani pankhani ya mbali zofunikira kukonza pa moyo wanu wauzimu komanso kuti mukhale munthu wokhwima maganizo?

․․․․․

Mukadzakhalanso ndi chibwenzi china kodi mudzapewa kuchita zinthu ziti?

․․․․․

N’zachidziwikire kuti simunkayembekeza kuti chibwenzi chanu chidzatha. Koma kumbukirani kuti: Mvula yamkuntho ikamagwa kunja kuli mitambo bii, munthu amangoona ngati siitha. Koma kenako mvulayo imasiya ndipo kumwamba kumakhala kuli ngwee. Achinyamata amene tawatchula poyamba paja anaona kuti patapita nthawi anaiwala. Nanunso mukhoza kuiwala ndipo musakayikire zimenezi.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.pr418.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina a m’nkhani ino si enieni.

^ ndime 5 Ngakhale kuti anthu amene mawu awo tawatchula m’nkhani ino ndi aakazi, mfundo za m’nkhani ino n’zothandizanso kwa amuna.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi mwaphunzira zinthu ziti zokhudza khalidwe lanu pa chibwenzi chimene munali nacho?

▪ Kodi mwaphunzira chiyani za anthu omwe si amuna kapena akazi anzanu?

▪ Kodi mungamufotokozere ndani ngati mukuona kuti mukulephera kupirira chifukwa cha kutha kwa chibwenzi?

[Bokosi patsamba 20]

YESANI IZI

Susan yemwe tinam’tchula poyamba uja analemba malemba osiyanasiyana n’kuwasunga kuti aziwerenga nthawi zonse akaona kuti wayamba kudandaula. Mwina inunso mungayese kuchita zimenezi mwa kusunga malemba ena amene ali m’nkhani ino.

[Chithunzi patsamba 19]

Kutha kwa chibwenzi kuli ngati bala lopweteka kwambiri koma pakapita nthawi limapola