Kodi Tsogolo Lanu Linalembedweratu?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Tsogolo Lanu Linalembedweratu?
Anthu ambiri amakhulupirira kuti moyo wawo ndiponso tsogolo lawo lonse linalembedweratu. Iwo amaganiza kuti tonsefe tikangobadwa, zonse zimene zimatichitikira zimakhala zoti zinalembedwa kale ndi Mulungu. Iwo amati, ‘Mulungu ndi wamphamvuyonse ndipo amadziwa zonse, kapena kuti ndi mwininzeru, motero sangalephere kudziwa chilichonse chimene chinachitika, chikuchitika, ndiponso chidzachitike m’tsogolo.’
NANGA inuyo mukuganiza bwanji? Kodi mumakhulupirira kuti Mulungu analemberatu zochitika zonse za pamoyo wathu? Kapena tifunse kuti, kodi tilidi ndi ufulu wosankha tokha zochita kapena ayi? Kodi Baibulo limati chiyani pankhaniyi?
Kodi Mulungu Amadziwa Zam’tsogolo Zonse Kapena Amangosankhapo Zina?
Baibulo limanena momveka bwino kuti Mulungu amatha kudziwiratu zinthu zam’tsogolo. Lemba la Yesaya 46:10 limati iye amadziwa “za chimaliziro kuyambira pachiyambi.” Anagwiritsiranso ntchito anthu kulemba maulosi ambirimbiri. (2 Petulo 1:21) Ndipotu maulosi onsewo amakwaniritsidwa chifukwa choti Mulungu ali ndi nzeru komanso mphamvu zotha kuwakwaniritsa ndendende. Motero, zinthu zimene Mulungu amadziwiratu ndiponso kulemberatu ndi zokhazo zimene iyeyo wasankha kutero. Komano kodi Mulungu amadziwiratu zonse zimene zidzachitike pa moyo wa munthu aliyense kuphatikizapo chiwerengero cha anthu onse amene adzapulumuke? Baibulo silinena choncho ayi.
Baibulo limatiuza kuti Mulungu amachita kusankha zinthu zimene akufuna kudziwiratu. Mwachitsanzo, Mulungu ananeneratu kuti “khamu lalikulu” la anthu olungama lidzapulumuka anthu oipa akamadzawonongedwa pa mapeto a dongosolo lino la zinthu. (Chivumbulutso 7:9, 14) Komano Mulungu sanatchuliretu chiwerengero chenicheni cha anthu a khamu lalikululi. N’chifukwa chiyani sanatero? N’chifukwa chakuti iye salemberatu zimene zidzachitike kwa munthu aliyense. Mulungu ali ngati bambo wokhala ndi ana ambirimbiri amene amawakonda. Motero, Mulungu amadziwa kuti sipangalephere kukhala ana ena omukonda chifukwa chakuti nayenso amawakonda, koma sanalemberetu kuti ana oterewo adzakhale ochuluka mwakutimwakuti.
Mulungu amagwiritsira ntchito luso lake lolemberatu zinthu za m’tsogolo mofanana ndi mmene amagwiritsira ntchito mphamvu zake. Mphamvu za Mulungu n’zopanda malire chifukwa iye ndiye Wamphamvuyonse. (Salmo 91:1; Yesaya 40:26, 28) Komano kodi mphamvu zimenezi amangozigwiritsira ntchito mosadziletsa? Ayi. Mwachitsanzo, iye anasankha kuti panthawi inayake asagwiritsire ntchito mphamvu zakezi powononga dziko la Babulo, lomwe linali paudani ndi mtundu wa Isiraeli. Mulungu anati panthawi yonseyo anakhala ‘akudzithungata,’ kapena kuti anakhala akudziletsa kudikirira nthawi yoyenerera. (Yesaya 42:14) Mulungu amachitanso chimodzimodzi pogwiritsira ntchito nzeru zake zodziwiratu zam’tsogolo ndiponso mphamvu zake zolemberatu zinthu za m’tsogolo. Yehova amadziletsa pankhani imeneyi kuti atipatse mwayi woti tigwiritsire ntchito bwino ufulu umene iye anatipatsa, wosankha tokha zochita.
Sikuti kudziletsa kumeneku kumachititsa kuti Mulungu akhale woperewera mbali inayake ayi. Kwenikweni, zimenezi n’zimene zimam’kweza kwambiri, ndipo zimachititsanso kuti tizim’konda. Tikutero chifukwa zimenezi zimasonyeza kuti iye samangolamulira mosonyeza kuti ndiye mwininzeru ndi mphamvu. Koma iye amalamulira mosonyezanso chikondi ndipo amalemekeza ufulu wosankha umene anatipatsa anthufe.
Komanso taganizirani mfundo iyi. Zitakhala zoona kuti Mulungu amakonzeratu chilichonse, ndiye kuti tingati ngozi zoopsa zonse zimene zakhala zikuchitika ndiponso zoipa zonse ndi mavuto onse a anthu amachititsa ndi iyeyo. Ndiye mutha kuona kuti chiphunzitso chonena kuti Mulungu amalemberatu chilichonse n’choipa kwambiri chifukwa chimam’chotsera ulemu Mulungu. Chiphunzitso chimenechi chimachititsa anthu kuganiza kuti Mulungu ndi wankhanza, wopanda chilungamo komanso wopanda chikondi. Komatu izi zimatsutsana kwambiri ndi zimene Baibulo limanena zokhudza Mulungu.—Deuteronomo 32:4.
Muli ndi Ufulu Wosankha
Kudzera mwa mtumiki wake Mose, Mulungu anauza mtundu wa Isiraeli kuti: “Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, . . . sankhani moyo, . . . [mwa] kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kum’mamatira iye, pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka.” (Deuteronomo 30:19, 20) Mawu amenewa akanakhala osamveka kapena abodza kukanakhala kuti Mulungu anakonzeratu zoti Aisiraeli onse adzamukonde n’kudzapeza moyo kapena kuti asadzamumvere n’kudzawonongedwa. Ndiyeno kodi mukuganiza kuti Mulungu yemwe ndi ‘wokonda chiweruzo,’ kapena kuti wokonda chilungamo komanso yemwe Baibulo limati ndi chikondi angachite zinthu zachinyengo zoterozo?—Salmo 37:28; 1 Yohane 4:8.
Mawu a Mulungu olimbikitsa atumiki ake kuti asankhe moyo akutikhudzanso kwambiri ifeyo masiku ano, chifukwa ulosi wa m’Baibulo ukusonyeza kuti tikuyandikira mapeto a dongosolo lino la zinthu. (Mateyo 24:3-9; 2 Timoteyo 3:1-5) Kodi tingatani kuti tisankhe moyo? Tiyenera kuchita zimene Aisiraeli anachita posankha moyo.
Kodi Mungatani Kuti ‘Musankhe Moyo’?
Kuti tisankhe moyo tiyenera “kukonda Yehova,” “kumvera mawu ake,” ndiponso “kum’mamatira.” Tingathe kuchita zimenezi ngati titamudziwa bwino Mulungu komanso kumvetsa zimene amafuna kuti tizichita. Popemphera kwa Mulungu, Yesu Khristu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”—Yohane 17:3.
Mungadziwe za Mulungu ndi Yesu kuchokera m’Baibulo lomwe ndi Mawu a Mulungu. (Yohane 17:17; 2 Timoteyo 3:16) Mphatso yochokera kwa Mulungu imeneyi ndi umboni wakuti iye sanalemberetu tsogolo lathu koma amafuna kuti aliyense asankhe yekha zochita akamva Mawu Ake.—Yesaya 48:17, 18.
Chifukwa chakuti Mulungu watipatsa Baibulo tingati akutiuza kuti: ‘Cholinga changa chokhudza dziko lapansi ndiponso anthu ndi chakutichakuti, choncho muyenera kuchita zakutizakuti kuti mudzapeze moyo wosatha. Ndiyeno zili ndi inu kusankha kundimvera kapena ayi.’ Apatu taona kuti Mulungu amagwiritsa ntchito mwanzeru mphamvu zake zolemberatu zinthu za m’tsogolo n’cholinga choti atipatse mwayi wogwiritsa ntchito ufulu wosankha tokha zinthu. Ndiyeno kodi inuyo musankha moyo mwa “kumvera mawu [a Mulungu]” ndiponso mwa “kum’mamatira”?
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
▪ Kodi Yehova amagwiritsa ntchito motani nzeru zake zodziwiratu zinthu zam’tsogolo?—Deuteronomo 30:19, 20; Yesaya 46:10.
▪ N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mulungu salemberatu zinthu zonse zimene zimachitikira anthu, kuphatikizapo zoipa zambirimbirizi?—Deuteronomo 32:4.
▪ Kodi kwenikweni tsogolo lathu likudalira pa chiyani?—Yohane 17:3.
[Mawu Otsindika patsamba 13]
Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu amachita kusankha pogwiritsa ntchito mphamvu zake zolemberatu zinthu za m’tsogolo