Mapiko a Zamoyo Zouluka
Panagona Luso!
Mapiko a Zamoyo Zouluka
▪ Kodi mukuganiza kuti chimene chimauluka mogometsa n’chiyani pakati pa mileme, tizilombo tosiyanasiyana touluka, mbalame ndi ndege? Katswiri wa sayansi ya zinthu zouluka yemwe amaphunzitsa pa yunivesite ya Michigan dzina lake Wei Shyy ananena kuti mwina mungadabwe kumva kuti ndege singanunkhe kanthu poiyerekezera ndi zamoyo zoulukazi zomwe n’zogometsa zedi chifukwa “zimatha kuuluka ngakhale kutakhala kuti kuli mphepo yamphamvu, mvula kapena kukugwa chipale chofewa. * Kodi chinsinsi cha zamoyo zimenezi chagona pati? Zimatha kukupiza mapiko mofulumira kwambiri. Anthu atapanga ndege yoyambirira ankaganiza kuti adzatha kukonza zina zouluka mogometsa chonchi.
Taganizirani Izi: Mapiko a mbalame komanso tizilombo tina touluka amakhala akusintha mogwirizana ndi malo amene zamoyozi zikuuluka. Chifukwa cha zimenezi, zoulukazi zimatha kuima m’malere kapena kukhotera kwina kulikonse mwamsangamsanga. Magazini ina inanena kuti akatswiri a sayansi apeza kuti mileme “ikakhala kuti sikuuluka mothamanga kwambiri, paliwiro la pafupifupi mita imodzi ndi theka pa sekondi imodzi, imatha kutembenuza nsonga ya mapiko ake kenako n’kuwakupiza mwamsangamsanga. Akatswiri asayansi akuganiza kuti luso limeneli ndi limene limathandiza mileme kuti izitha kupita m’mwamba n’kumauluka.”—Science News.
Pali zinthu zambiri zimene sitizimvetsa zokhudza kaulukidwe ka zamoyo zimenezi. Katswiri wina, dzina lake Peter Ifju, yemwe ndi pulofesa wa maphunziro a kakonzedwe ka ndege pa yunivesite ya Florida, anati: “Sitikudziwa kuti zamoyo zimenezi zimatha bwanji kuuluka chonchi. Pali zambiri zimene sitimazimvetsa zokhudza mmene mphepo imakankhira chinthu chimene chikuuluka. Timaona zimene [mbalame ndi tizilombo touluka] zimachita pouluka koma sitimvetsa mmene mphepo imakhudzira zinthu zimenezi zikamauluka.”
Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi mapiko ogometsa a zamoyo zimenezi anangokhalapo mwangozi kapena anachita kulengedwa mwaluso?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Ngakhale kuti zamoyo zambiri zouluka zingathe kuuluka mvula ikugwa, zochuluka zimabisala.
[Chithunzi patsamba 24]
Mtundu wa mbalame zotchedwa choso
[Mawu a Chithunzi]
Laurie Excell/Fogstock/age fotostock
[Chithunzi patsamba 24]
Mleme
[Mawu a Chithunzi]
© Delpho, M/age fotostock